BAIBLULO NDI BUKU LOTITSOGOLERA

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN ——MI—— Na. 3

BAIBLULO NDI BUKHU LOTITSOGOLERA
Kuwerenga : Masalmo 119:1-40
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Baibulo limasonyeza kuti ndi Mawu a Mulungu. Baibulo limanena kuti "Lemba lililonse adaliuzira Mulungu" (2 Timoteo 3:16). Mawu akuti “kuuzira” amatanthauza kuti ‘Mulungu anapumiramo mpweya’. Mulungu ankatsogolera anthu kuti alembe mawu ake. Aneneri a m’Chipangano Chakale kawirikawiri ankanena kuti “Ndipo Mulungu anati”.
Ngati Baibulo lopatulika si Mawu a Mulungu ndiye kuti si lofunikanso ayi; koma ngati lilidi uthenga wochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu, ndiye kuti ndi m’pofunika kumaliwerenga ndi kumayesetsa kuchita zimene likutiuza kuti tichite. Koma ngati tinganyalanyaze uthenga wa m’Baibulo, ndiye kuti tikunyalanyaza Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi.
KODI TIMADZIWA BWANJI KUTI ZIMENEBAIBULO LIMANENA N’ZOONA?
Baibulo linalosera zimene zidzachitike m’tsogolo
Anthufe sitinganene motsimikiza kuti mawa kugwanji. Koma m’Baibulo muli mawu ambiri amene ananeneratu zimene zidzachitika m’tsogolo, ndipo linaneneratu zimenezi kuli zaka zambiri zinthuzo zisanachitike. Zinthu zoterezi zakhala zikuoneka kuti n’zoona chifukwa zinthuzo zinachitikadi patapita nthawi ndipo zina zikuchitikabe.
Taonani zitsanzo izi:
1. Kubadwa kwa Yesu
M’chaputala 2 cha Uthenga Wabwino wa Mateyu timawerenga kuti anzeru a kum’mawa anabwera kwa Herode ndi kufunsa, “Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda?” Ndipo Herode anafunsa akulu a nsembe funsoli, ndipo iwo anayankha, “Mu Betelehemu wa Yudeya”. Kodi iwo anadziwa bwanji izi? Anadziwa izi chifukwa, zaka zambiri za m’mbuyomo, zinanenedwa m’bukhu lina la m’Chipangano Chakale–-Mika 5:2.
2. Imfa ya Yesu
Tsopano pitani pa Salmo 22 ndipo muwerenge mavesi onse mosamala kwambiri. Mu Salmo limeneli akufotokozamo za kupachikidwa kwa Yesu. Onani kuti chakumapeto kwa vesi la 16 kuli mawu akuti– “Anandiboola m’manja anga ndi m’mapazi anga”. Tawerenganinso vesi 18. Pavesili pali mawu akuti– “Agawana zobvala zanga, nalota maere pa malaya anga.”
Ndiyeno werengani Yohane 19:23-24, ndipo muona kuti zimene zafotokozedwa ndi zimenedi asilikali anam’chitira Yesu atamupachika. Kodi zikanatheka bwanji kuti wolemba Masalmo alembe za imfa ya Yesu zaka za m’mbuyo Yesu asanabadwe n’komwe ngati wolembayo sanauziridwe ndi Mulungu?
Izi n’zochititsa chidwi, chifukwa m’masiku a wolemba Masalmo, Ayuda sankadziwa chilichonse chokhudza kupachika anthu pa mtanda – iwo anali kupha anthu awo olakwa mwakuwaponya miyala.
3. Zinthu zina zikuluzikulu zimene zinaloseredwa
Panopa werengani Yesaya 13:19-20. Pamene mneneri Yesaya anali kulemba mawu amenewa onena za mzinda wa Babulo, Ababulo anali mtundu waukulu kwambiri m’dziko lonse lapansi; wolemera ndi wamphamvu kwambiri. Koma tsopano, malo amene panali mtundu wa Babulo, pasanduka bwinja ndipo ndi chipululu chokhachokha. Zaka zambiri zapitazo pamene zinanenedwa izi, ulosi wa Yesaya wakwaniritsidwa monga m’mene ananenera. Ndi Mulungu yekha amene akanatha kuoneratu kuti kusintha uku kudzachitika. Pali zitsanzo zambiri monga izi. Ndi Mulungu yekha mwini amene angathe kuona za m’tsogolo, ndipo ulosi umene walembedwa m’Baibulo ukuonetsa kuti Mulungu anali kuuza anthu zinthu zoti anthuwo alembe.

Akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza umboni wa zinthu zambiri zotchulidwa m’Baibulo
Akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza kuti mizinda ya Sodomu ndi Gomora inalikodi (Genesis 19). Chimodzimodzinso ndi mizinda ya Ai, Asikeloni, Beteli, Beti-semesi, Gibeya, Hazori, Yeriko, Lakisi, Megido, Samariya, Sekemu, ndi maina ena ambiri amene atchulidwa m’Baibulo.

Baibulo silinasinthe ngakhale kuti papita zaka zambirimbiri
Pa mipukutu imene inapezeka ku Nyanja Yakufa m’chaka cha 1947, panali mpukutu wa buku la Yesaya. Mpukutuwu unalembedwa zaka pafupifupi zaka 2000 zapitazo. Zimene zalembedwa mumpukutuwu n’chimodzimodzi ndi zimene zili m’buku la Yesaya masiku ano. Izi zikusonyeza kuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe ngakhale pang’ono ngakhale kuti papita nthawi yayitali.
Yesu ankakhulupirira Chipangano Chakale
Pali anthu ena masiku ano amene amatsutsa zoti Adamu ndi Hava anali anthu enieni amene anakhala ndi moyo padziko lapansili. Enanso amatsutsa zoti Nowa anamangadi chingalawa ndi kulowetsamo nyama zonse zija. Amaganiza kuti iwo ndi anzeru ndipo sangakhulupirire nkhani zimene iwowo amaona kuti ndi nthano, monga ya Yona amene anamezedwa ndi chinsomba chachikulu. Koma anthuwa Yesu ankakhulupirira nkhani zimenezi!
Yes ankakhulupirira zimene Chipangano Chakale chimaphunzitsa pa:

Adamu ndi Hava, Nowa ndi chigumula, Loti ndi mkazi wake, Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Davide ndi Solomo, Yona ndi chinsomba
(onani Mateyu 19:4,5) (onani Luka 17:26,27) (onani Luka 17:29-32) (onani Mateyu 8:11) (onani Mateyu 12:3,42) (onani Mateyu 12:40)

Ife sitinganyalanyaze maganizo a Ambuye Yesu Khristu. Iye anaukitsidwa kwa akufa ndi Mulungu atafa kwa masiku atatu. Uwu ndi umboni woona wochokera m’mbiri, umene anthu oganiza bwino ayenera kuulandira. Zodabwitsa zoterezi zikanatha kuchitika ndi mphamvu ya Mulungu yekha basi.
Palibe munthu amene anapezapo umboni wosonyeza kuti Baibulo silolondola
Anthu ambiri omwe amadana ndi Baibulo, kuphatikizapo anthu ochenjera kwambiri, anayesetsa kuti apeze umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi losalondola koma alephera. Tikaganizira zimenezi, tingavomereze kuti zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
* Panapita zaka zoposa 2,000 kuti Baibulo lonse lilembedwe.
* Ena mwa anthu amene analemba Baibulo anali abusa, mafumu, asodzi, madokotala, ndiponso osoka mahema.
* M’Baibulo muli mabuku 66; 39 m’Chipangano Chakale ndipo 27 m’Chipangano Chatsopano.
* Onse amene analemba Baibulo analemba zogwirizana—nkhani yokhudza cholinga cha Mulungu kwa ife anthu.
* Pafupifupi onse amene analemba Baibulo anali Ayuda.
* Nkhani zambiri zimene zili m’Baibulo zimafotokoza zinthu zokhudzana ndi Ayuda.

Tiyeni tione mwachidule zimene zili m’mbali zosiyanasiyana za Baibulo:
CHIPANGANO CHAKALE
BUKHU
ZIMENE ZILI M’BUKHULO

GENESIS
Chiyambi cha dziko komanso zimene Mulungu ankachita ndi anthu oyambirira

EKSODO LEVITIKO NUMERI DEUTERONOMO
Mabukuwa akutiuza mmene Mulungu anasankhira Ayuda kuti akhale anthu Ake komanso mmene anawatulutsira ku Igupto n’kuwapatsa dziko ka Kanani (Israyeli).

YOSWA ESTERE
Mbiri ya Ayuda ikupitirira m’mabuku amenewa.

MASALIMO
1 • • NYIMBO YA SOLOMO
Awa ndi mabuku a ndakatulo komanso a nzeru.

YESAYA
MALAKI
«
Awa ndi mabuku a aneneri. Amafotokoza mmene Ayuda anafunikira kumvera Mulungu komanso amafotokoza zinthu zina zofunika zokhudzana ndi mbiri ya dzikoli. (Ena mwa maulosi amenewa akukwaniritsidwa panopa ena adzakwaniritsidwa m’tsogolo.)

CHIPANGANO CHATSOPANO

MATEYU MARK LUKA YOHANE
MACHITIDWE A ATUMWI
AROMA
YUDA
CHIBVUMBULUTSO
Mabuku anayi awa amafotokoza za moyo wa Yesu, imfa yake, ndiponso kuuka kwake kwa akufa.
Muli nkhani yokhudza mipingo 6 yoyambirira (kapena ma eklesia) imene Akhristu a M’zaka 100 Zoyambirira anapanga. (Mipingoyi ndi chitsanzo chimene tiyenera kutengera masiku ano.)
Makalata osiyanasiyana amene atumwi analembera ku matchalitchi amene anali atangoyamba kumene.
Bukhu la ulosi.

(Ngati mufuna kudziwa mabuku onse opezeka m’Baibulo, mukhoza kuwapeza p tsamba loyamba la Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano m’Baibulo lomwelo.)
Kodi pali mabukhu enanso ochokera kwa Mulungu kuwonjezera pa Baibulo? ^
Yankho ndi lakuti, "Ayi". Zipembedzo zambiri padziko lapansi zili ndi mabuku awo amene amawaona kuti ndi 'opatulika'. Mwachitsanzo, Asilamu ali ndi Korani, buku lomwe amati ndi Mawu a Mulungu. Nawonso a Mormon ali ndi “buku la Mormon”, limene amanena kuti linatumizidwa kwa iwo ndi Mulungu. Ena mwa mabuku amenewa amatenga mbali ya chiphunzitso chawo m’Baibulo; ena amapereka malangizo abwino ndi anzeru, koma m’mbali zambiri mabuku amenewa samagwirizana ndi uthenga wa m’Baibulo.
Tsopano ndi chachidziwikire kuti Mulungu sanganene chinthu chimodzi m’buku limodzi ndi chinthu china cholekana m’buku lina. Chifukwa cha ichi ndi buku limodzi lokha limene lingakhale louziridwa ndi Mulungu. Baibulo limanena lokha kuti ilolo ndi louziridwa ndi Mulungu.
Baibulo—Bukhu lotsogolera pa moyo wa munthu
Mulungu anaona umoyo womvetsa chisoni wochimwa wa munthu ndipo chifukwa cha ichi anatuma mwana wake, Yesu, kufa kuti anthu akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Yesu Kristu anationetsanso ife momwe tingakhalire m’moyo wokondweretsa Mulungu. Bukhu lopatulika liri ndi zitsanzo zina za anthu a chikhulupiriro. Ilonso limationetsa ife momwe ena analepherera ndiponso nkhani ya Ayuda ikutipatsa ife kutengapo phunziro pa zolakwa zawo zonse.
POMALIZA-
Mulungu wa kumwamba anaganiza mwakuya n’kutipatsa bukhu lotithandiza kuti timudziwe, ndiponso kuti tizikhala moyo umene Iye afuna. Kudzera m’Baibulo, Mulungu watiuza chifukwa chimene analengera dziko lapansi, ndi kuti mbiri ya dzikoli idzakhala bwanji, mpaka kufikira nthawi imene Uthenga Wabwino udzakwaniritsidwa, ndiponso nthawi imene chifuniro cha Mulungu chidzakwaniritsidwa.
Mulungu watipatsa Baibulo kuti lizititsogolera pa moyo wathu mpaka kuti tidzalowe mu Ufumu wake n’kupeza moyo wosatha. Palibe bukhu lina limene lingafanane ndi Baibulo. Si bukhu lachikale lakutha ntchito – ndi mawu opatsa moyo. Ngati tiwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, mosamala ndi mwapemphero, likhoza kusintha moyo wathu, ndipo tingathe kukondweretsa Mulungu.
Mwachidule
1. Baibulo ndi bukhu lapadera. Limanena lokha kuti ndi Mawu a Mulungu opita amuna ndi akazi.
2. Limapereka chiyembekezo cha moyo wosatha kwa amuna ndi akazi.
3. Yesu ankakhulupirira Malemba a m’Chipangano Chakale.
4. Pali umboni wambiri wosonyeza kuti Baibulo ndi loona: akatswiri ofufuza zinthu zakale apeza zinthu zotchulidwa m’Baibulo; muli maulosi ambiri amene akwaniritsidwa.
5. Limatiuza zimene Mulungu ankachita ndi anthu, kuyambira pamene munthu analengedwa kufika pamene padziko lonse padzadzaza ulemerero wa Mulungu.
6. Baibulo ndi mphatso imene Mulungu watipatsa, ndipo limatipatsa malangizo othandiza pa moyo wathu. Tikuyenera kumaliwerenga tsiku ndi tsiku.
Mavesi oyenera kuwerenga : Salmo 1; Salmo 22; 2 Timoteo 3. Lowezani : 2 Timoteo 3:16-17.
"Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino."
Christadelphian Bible Mission Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Chichewa
Tags: