KODI MA CHRISTADELPHIANS NDI NDANI

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN •^•^ Na. 2 KODI MA CHRISTADELPHIANS NDI NDANI? Kuwerenga : Yohane 15 Cholinga cha kosi ya Baibuloyi ndi kuthandiza anthu kuphunzira Malemba. Komabe, mwina mungadabwe kuti, kodi ma Christadelphians ndi ndani? Choncho munkhani ino tikufotokozerani pang’ono zokhudza ifeyo. Ma Christadelphians ndi gulu la amuna ndi akazi amene akupezeka padziko lonse, amene amawerenga Baibulo lonse ndipo amaliona kuti ndi Mawu a Mulungu ouziridwa. Amakhulupirira malonjezo onse onena za Ambuye Yesu Khristu komanso onena za dziko la m’tsogolo, amene ali m’Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano. Ma Christadelphians akuyembekezera kuti Yesu adzabweranso kuchokera kumwamba kuti adzakhazikitse ufumu wa Mulungu padziko lapansili. Dzina lakuti Christadelphian linachokera kumawu awiri achigiriki, amene amatanthauza Abale mwa Khristu. Kodi ma Christadelphians amakhala kuti? Ma Christadelphians akupezeka m’mayiko oposa 50. Amapezeka ku Britain komanso m’mayiko ambiri a ku Ulaya. Amapezekanso m’mayiko ambirimbiri ku Africa; ku Far East, kuchokera ku India mpaka ku Indonesia; ku Australasia ndi kuzilumba za panyanja ya Pacific. Akupezekanso m’mayiko a ku North ndi South America kuchokera ku Canada mpaka kukafika ku Argentina, komanso pazilumba za ku Caribbean. M’gululi muli amuna ndi akazi a mitundu yosiyanasiyana komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana. Kosi ma Christadelphians amakhulupirira zotani? Ma Christadelphians chikhulupiriro cha chagona pa zinthu zimene Yesu ndi ophunzira ake ankakhulupirira komanso kuphunzitsa zaka pafupifupi 2000 zapitazo. Uthenga weniweni wa Chikhristu sunasinthe. Koma n’zomvetsa chisoni kuti kwa zaka mahandiredi ambirimbiri matchalitchi “Achikhristu” akhala akutsatira komanso kuphunzitsa zinthu zimene zinachokera ku zipembedzo zonyenga. Ngakhale zili choncho, padzikoli pakhala pakupezeka kagulu ka anthu ochepa kwambiri amene sanasiye kutsatira choonadi. Mwachitsanzo, ku Ulaya zaka zoposa 400 zapitazo kunali anthu ambiri amene anaphunzira uthenga woona wabwino chifukwa choti ankawerenga Baibulo pawokha pamene Baibulolo linasindikizidwa m’zinenero za anthuwo. Amuna ndi akazi amenewa anayamba kutchedwa "Abale mwa Khristu". Koma n’zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa anthu amenewa anazunzidwa koopsa, ndipo ena anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ambiri anathawa m’nyumba zawo, koma pamene ankathawa anatenga Uthenga Wabwino n’kumaufalitsa m’mayiko ambiri a ku Ulaya, kuwoloka nyanja zikuluzikulu. Koma sipanapite nthawi yaitali kuti choonadicho chisakanikiranenso ndi ziphunzitso zonyenga. (Pali phunziro la mphamvu apa: Choonadi sichisokonezedwa pokhapokha ngati anthu amene ali ndi choonadiwo akuwerenga ndi kuphunzira pawokha Mawu a Mulungu.) Kosi gulu la ma Christadelphian linayamba bwanji? Mu 1832, dokotala wina wa ku England, dzina lake John Thomas, amenenso anali m’busa wa tchalitchi chinachake, anakwera sitima yapamadzi imene inkapita ku New York. Iye anachita izi chifukwa bambo ake ankafuna kusamukira ku America. Ulendowu uli mkati, sitimayo inawomba nthaka chifukwa cha namondwe woopsa amene anachitika panyanjayo, ndipo Dr. Thomas ankangoganiza kuti basi, afera pomwepo. Iye anazindikira kuti sankadziwa zambiri zokhudza tsogolo, ndipo analumbira kuti ngati safa komanso akafika kumtunda ali wabwinobwino, ndiye kuti sapuma koma nthawi yomweyo adzayamba kufufuza choonadi pa nkhani yokhudza moyo umene anthu angakhale nawo pambuyo pomwalira. N’zosangalatsa kuti mkuluyu sanafe ndipo anafikadi ku New York. Atangofika, iye anachitadi zimene analonjeza zija. Anakhala masiku okwana 15 akuphunzira Baibulo mwakhama zedi Ndipo analinso ndi mpata wounika zimene matchalitchi ambirimbiri "Achikhristu" amaphunzitsa. Atakhutira kuti wamvetsa bwino zinthu zimene zinalembedwa m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano chomwe zokhudza Yesu Khristu komanso zokhudza kubwera kwa ufumu wa Mulungu padziko lapansi, anakonza zoti abatizidwe, thupi lonse limire m’madzi. Iye anapitiriza kulalikira m’madera osiyanasiyana ku America komanso ku Britain ndipo analemba magazini ndi mabuku ambirimbiri a nkhani zachipembedzo. M’gulu la anthu amene anayamba kukhulupirira zinthu zofanana ndi John Thomas n’kuyamba kugwirizana naye pa ntchito yakeyi munali Robert Roberts, yemwe kwawo kunali ku Scotland. Roberts anathandiza pa nthawi yokonza dongosolo labwino pakati pa Akhristu a agululi amene anayamba kuchuluka kwambiri, ndipo magulu amene ankaikamo anthuwa ankawatchula kuti ma eklesia. "Eklesia" ndi mawu a m’Baibulo amene amatanthauza "msonkhano wa anthu amene aitanidwa". Ma Christadelphians amaona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito mawu amenewa kusiyana ndi "tchalitchi"—dzina lomwe nthawi zina limatanthauza nyumba imene anthu amapemphereramo m’malo mwa anthu amene akupemphera ali mkati mwa nyumbayo. Dzinali koyamba limamveka lachilendo Mawu lakuti Christadelphian linagwiritsidwa ntchito koyamba mu 1864 pamene anthu okhulupirira anapempha boma la America kuti asamalembedwe ntchito za usilikali pa nthawi imene ku America kunali nkhondo ya pachiweniweni. Popeza pamafunika dzina loti anthuwa azidziwika nalo, John Thomas anakumbukira "Abale mwa Khristu" amene anali zaka zoposa 300 m’mbuyomo, choncho anasankha dzina lakuti ma 'Christadelphian', lomwe ndi dzina lachigiriki otanthauza Abale mwa Khristu. Ma Christadelphians a m’zaka za ma 1800 amene ankayenda zedi n’kumalalikira uthenga m’mayiko osiyanasiyana padziko lapansili. Choncho pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 1800, anthuwa anali akupezeka m’mayiko ambirimbiri padziko lonse lapansi. Kodi gulu la ma Christadelphians linalinganizidwa komanso kukonzedwa motani? Pali makomiti osiyanasiyana amene amayang’anira ndi kuyendetsa ntchito ya umishonale, kuyang’anira ndi kuzonda odwala komanso okalamba, komanso anthu amene ali okhaokha. Komanso tili ndi maofesi m’mayiko angapo ndipo timafalitsa magazini ndi mabuku kudzera m’ma ofesi amenewa. Koma tilibe anthu kapena atumiki amene amalipidwa. Tilibenso bungwe limene tingati ndi lamphamvu kapena limene limayang’anira gulu lathu. Ndalama zoyendetsera ntchito yathu yonse anthu a m’gulu la ma Koma mwina mungafunse kuti: ngati palibe gulu loyendetsa gulu limeneli, kodi ntchito yonse ya ma Christadelphans imayenda bwanji? Yankho ndi lakuti izi zimatheka chifukwa choti tonse tili ndi chikhulupiriro chofanana komanso timachita zinthu zofanana. Zimenezi zimathandiza kuti tizichita zinthu mogwirizana komanso mokondana monga mamembala a gululi. Gulu lililonse limakhala ndi dongosolo lawo loyendetsera zinthu ndipo limasankha lokha “akulu” otsogolera gululo. Izi zimachitika posankha akuluwo kamodzi chaka chilichonse mochita kuvota. Anthu amene amasankhidwa kuti azitumikira eklesia mu mautumiki osiyanasiyana, monga alembi, asungichuma, matcheyamani a misonkhano. Iwo salipidwa chifukwa cha ntchito yawoyi komanso iwo si "ansembe" chifukwa timakhulupirira kuti Yesu, amene panopa ali kumwamba, ndi Wansembe yekhayo— amene mamembala onse atchalitchi obatizidwa ayenera kumuululira machimo awo komanso kupempherako. Ma Christadelphians samanga matchalitchi akuluakulu komanso ogometsa. N’zoona kuti pali m’madera ena amene mamembala a gululi amatha kupeza kapena kumanga nyumba zawozawo zopemphereramo. Komabe m’madera ambiri amapempherera m’nyumba ndi m’maholo ochita kubwereka. Zikhulupiriro zofanana Ma Christadelphians, kulikonse kumene ali apadzikoli, akhala akuwerenga ndi kuphunzira mabuku awo opatulika ndipo akhala akukhulupirira zinthu zofanana. Patha zaka pafupifupi 100 tsopano pamene takhala ndi mawu a chikhulupiriro chathu. Tili ndi chikalata chotchedwa Chikalata cha Chikhulupiriro (chidule cha ziphunzitso za m’Baibulo) ndipo aliyese yemwe ndi membala amayenera kuchita zimenezi nthawi zonse kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha ma Christadelphian onse, chomwe ndi chochokera m’Baibulo. Zimenezi n’zimene zimatichititsa kuti tizigwirizana kwambiri. "Thupi limodzi . . . mzimu umodzi" (Aefeso 4:4-5) Zimenezi zimachititsa kuti ma Christadelphians, kuli konse kumene ali, azitha kugwirizana komanso kuchitira zinthu pamodzi. Mtundu wa anthu umene tikuyesetsa kukhala Aliyense amafunika kuthandizidwa ndi Mulungu. Pa chifukwa chimenechi, timakhulupirira kuti ndi kofunika kwambiri kuti tizipemphera. Chinthu chimodzi chimene timayesetsa kuchita tsiku ndi tsiku ndi kuwerenga Baibulo. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri ngati mmene kulili kudya chakudya nthawi ndi nthawi. Kamodzi pa mlungu, timakumana ndi kudya mkate pang’ono ndiponso kumwa vinyo pang’ono pokumbukira imfa ya Ambuye wathu Yesu Khristu. Mudzapeza kuti ma Christadelphians ndi anthu osangalala chifukwa ali ndi chikhulupiriro chotsimikizika ndi zochita zawo. Popeza Yesu akubwera posachedwapa, tikufunika kukhala okonzeka. Izi zikutanthauza kukhala m’moyo woyera ndi wokhulupirika. Zikutanthauzanso kupewa zinthu zonse zoipa. Ma Christadelphians ndi anthu omvera malamulo a dziko lawo. Amayesetsa kuchita zinthu zabwino momwe angathere, koma salowerera ndale, ndiponso samenya nkhondo kapena kutengera anthu kubwalo la milandu kuti akaweruzidwe. Amakhala ndi mkazi m’modzi komanso amapewa chigololo. (Timazindikira kuti ena alipo kale amene ali ndi akazi opitirira m’modzi pa nthawi imene iwo afika pakukhulupirira mawuwa, ndipo zoterezo zakambidwa mu Phunziro 33.) Ma Christadelphian ali ndi Cholinga cha m’Baibulo Timatchulana mwachidule kuti ma CBM ndipo ntchito yathu ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’dziko lonse lapansi. CBM imalengeza maphunziro, imalemba mabuku ndi zinthu zina zowerenga ndiponso imathandiza anthu kumvetsa Baibulo. CBM ili ndi anthu ogwira ntchito amene salipidwa malipiro alionse koma ndi a Christadelphian ongodzipereka kugwira ntchitoyi kuwonjezera pa ntchito imene amagwira yolembedwa ndi ena kumene amalandira malipiro. Cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuphunzira uthenga wabwino, kuwalimbikitsa kulapa ndi kubatizidwa, ndiponso kuti azitsatira chitsanzo cha Yesu komanso cha ophunzira ake. Tikufuna kugawana nanu zikhulupiriro zathu, chiyembekezo chathu ndiponso chimwemwe chathu Ma Christadelphian amakhulupilira kuti chikhulupiriro chawo n’chogwirizana ndi uthenga wabwino woona umene ukupezeka m’Baibulo lonse. Tikukhulupirira kuti inunso mudzasangalala kupeza Choonadi. Sikuti muzangosangalala basi kuti mwapeza chinthu chabwino, koma mudzakhalanso ndi chiyembekezo, chisangalalo komanso chikondi. Mulungu akudalitseni pamene mukuyesetsa kufunafuna zinthu zimenezi. Patsamba lotsatira pali mfundo zina zofunika kwambiri za m’Baibulo. Mavesi oti muwerenge : Salmo 119:130; Mateyu 28:19-20; Yohane 17:3. Lowezani : Yohane 15:13-14 " Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu." ZIPHUNZITSO ZINA ZOFUNIKA KWAMBIRI ZA M’BAIBULO * Baibulo ndi uthenga woona wokhawo wochokera kwa Mulungu. * Pali Mulungu m’modzi yekha basi, Mlengi, amene amayendetsa zinthu padzikoli. * Yesu Khristu ndi mwana wa Mulungu, wobadwa mwa Mariya. Anali munthu wosachimwa. Anafa imfa ya pa mtanda kupulumutsa iwo akukhulupilira iye. Anaukitsidwa kwa akufa ndipo pakali pano ali kumwamba. * Posachedwapa Yesu adzabwera kuchokera kumwamba. Adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pano padziko lapansi. Iye adzalamulira ngati Mfumu ndipo likulu lake lidzakhala Yerusalemu m’dziko la Israyeli. * Ayuda ndi mboni za Mulungu pa cholinga chake, ngakhale ambiri mwa Ayudawo sadziwa zimenezi. Mulungu anapereka malonjezano kwa Abrahamu ndi kwa Davide amene adzakwaniritsidwa pakubwera kwakenso kwa Yesu pano padziko lapansi. * Imfa ndi chilango cha uchimo ndipo anthu onse ndi ochimwa. Chiyembekezo cha moyo wina tikafa ndicho chiukiriro cha akufa Yesu akadzabwera. * Padzakhala chiweruzo. Otsatira a Yesu onse okhulupirika adzapatsidwa moyo wosatha ndipo iwo adzathandiza iye kukonza mavuto a dziko lapansi ndi kubweretsa mtendere ndi madalitso kwa mitundu yonse ya anthu. Tiyenera kukhulupirira uthenga wabwino, kulapa machimo athu ndi kubatizidwa. Ngati tiyesetsa kwambiri kutsatira malamulo a Mulungu, ndi kupemphera kuti atikhululukire tikalephera, tidzapulumutsidwa ndithu. * Zimene Buku lopatulika lanenera zokhudza zinthu za kumbuyo ndi zinthu za nthawi ino zochitika m’dziko lapansi zawonekadi kuti zachitika. Zizindikiro zikuonetsa kuti Yesu Khristu watsala pang’ono kubwera. Ndi chifukwa chake kuli kofunika kuti muyambe kuphunzira buku lopatulika panopa. Christadelphian Bible Mission Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Chichewa
Tags: