KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN •^————— Na. 1 KUGWIRITSA NTCHITO KOSI YA BAIBULOYI Kuwerenga : Salmo 19 Kosi Yophunzitsa Baibulo ya ma Christadelphians yakonzedwa m’njira yakuti ikuthandizeni kumvetsa Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Baibulo, lomwe nthawi zina limatchedwa "Malemba", ndi buku lokhalo lomwe limatiuza molondola zokhudza Mulungu komanso mapulani ake okhudza dziko lapansili. Baibulo limalonjeza kuti aliyense amene amaliwerenga moona mtima adzalandira madalitso. Mukufunikira mukhale ndi Baibulo lanulanu Kukhala ndi Baibulo ndi mwayi wapadera kwambiri. Kuti mupindule ndi kosiyi mukuyenera kukhala ndi Baibulo lanulanu lathunthu (osati Chipangano Chatsopano chokha). Ngati mulibe Baibulo, mungaligule motchipa ku nthambi ya Bible Society. Pafupifupi m’dziko lililonse muli nthambi zimenezi. Koma ngati simungakwanitse kuchita zimenezi, dziwitsani mphunzitsi wanu mwachangu. Iye angakuthandizeni kuti mupeze Baibulo lakale. Kosiyi ili ndi mapepala a mafunso okwana 40, amene mukufunika kumayankha mlungu uliwonse. Ngati mphunzitsi wanu amakhala kutali kwambiri ndi kumene inuyo muli, ndiye kuti muzatumiziridwa maphunziro angapo komanso Mapepala a Mafunso onse nthawi imodzi. Mphunzitsi wanu ndi: Nambala Yanu Ndi Chonde, muzigwiritsa ntchito nambala imeneyi pa makalata onse, komanso pa mapepala a mayankho, ndi zina ndi zina. Chonde, tumizani mayankho anu onse (pamodzi ndi mayankho) kwa mphunzitsi wanu. Zingakhale bwino ngati mutangolemba dzina la mphunzitsi lanu basi, ngakhale kuti mungaone mayina ndi maadiresi ena ambiri pa mabuku athu. Mawu ochokera m’Baibulo amene muwapeze mu kosiyi achokera m’Baibulo Revised Nyanja (Union) Version, koma mwina Baibuloli silingapezeke m’mayiko ena. (Mwina mungaone kuti mawu a m’Baibuloli akhoza kusiyana pang’ono ndi mawu a m’Mabaibulo ena amene akupezeka m’dziko lanu.) Komabe, sikuti tanthauzo la mawuwo limasiyana ayi ngakhale kuti mabaibulo angasiyane. Kosiyi ndi ya ulele. Mungafunike kulipira mtengo wotumizira kalata kwa mphunzitsi wanu kamodzi pamwezi. Cholinga chathu n’chofuna kukuthandizani kuti muzisangalala mukamawerenga Malemba, komanso tikufuna kuti inuyo mudziwe uthenga wosangalatsa wachipulumutso chodzera mwa Yesu Khristu. Sitipereka masatifiketi kwa anthu amene amaliza maphunzirowa ayi, koma mukamaliza maphunziro okwana 60, tikufuna kukuthandizani kuti mupitirize kuphunzira Baibulo. Malifalensi a Baibulo Pakaperekedwa lifalensi ya m’Baibulo, izilembedwa mooneka chonchi: Genesis 1 —izi zikutanthauza kuti Buku la Genesis, chaputala 1; Genesis 1:1 -7— zi zikutanthauza kuti buku la Genesis, chaputala 1, vesi 1 mpaka 7. Mmene mungaphunzirire Muziyesetsa kuphunzira mutu umodzi mlungu uliwonse. Tikukupemphani kuti muzionetsetsa kuti mwamvetsa phunziro limodzi musanapite ku lina. Zimakhala zothandiza kuwerenga phunziro lililonse katatu. Nthawi yoyamba, muziyesetsa kudziwa zokhudza phunzirolo, nthawi yachiwiri, muziwerenga mavesi onse kuchokera m’Baibulo lanu ndipo muzilemba manotsi papepala kapena muzilemba mafunso omwe mwaona kuti ndi ovuta. Nthawi yachitatu muziwerenga pamodzi ndi malifalensi ena amene aikidwa koyambirira kwa phunzirolo. Kenako kumapeto kwa phunziro lililonse, mupezako mavesi ena othandiza kwambiri, omwe mungachite bwino kumawawerenga m’Baibulo lanu, komanso lemba limodzi limene tikukulimbikitsani kuti muliloweze pa mtima. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musaiwale mavesiwa ndipo angakuthandizeni pamoyo wanu wonse. Tikamakutumizirani mapepala anu oyambirira, timatumizanso PULANI YOKUTHANDIZANI POWERENGA BAIBULO. Pulaniyi inakonzedwa m’njira yokuthandizani kuti muziwerenga chaputala chimodzi m’Baibulo tsiku lililonse. Mukamayesetsa kuchita zimenezi, ndiye kuti simuchedwa kuzolowera mbali zosiyanasiyana za Baibulo. (Mungachite bwino kusunga Pulani Yokuthandizani Powerenga Baibulo mkati mwa Baibulo lanu, kuti muzitha kuigwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku.) Palinso chinthu china chothandiza chimene tikufuna kuti mukhale nacho. Mphunzitsi wanu akangolandira mayankho a mafunso a Pepala Loyamba, adzakutumizirani kope laulere la buku lotchedwa BUKU LOTHANDIZA POWERENGA BAIBULO. M’bukuli muli ndemanga zachidule za kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.Bukuli ndi lifalensi yothandiza kwambiri ya Baibulo chifukwa lili ndi zinthu ngati mapu ambirimbiri komanso zithunzi zina. Kuyankha Mafunso Tikukupemphani kuti mwezi uliwonse muzitumiza mayankho a mafunso kwa mphunzitsi wanu. tumizani mayankhowo pa positi.) Chonde, muziyankha mafunsowo m’mawu anuanu. Musangokopera zimene zalembedwa m’phunzirolo. Muziyesetsa kufotokoza zimene inuyo mukukhulupirira kuti n’zoona. Ngati simukugwirizana ndi mfundo zina zimene zili m’phunziro linalake kapena muli ndi funso, chonde, fotokozani. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri. Musaiwale kuti tingakuthandizeni bwino ngati tikudziwa zimene mukuganiza. Ngati pa zifukwa zina simungathe kutumiza mayankho anu, tumizani uthenga wachidule wotidziwitsa kuti mukufunitsitsa kupitirizabe ndi kosiyi ndipo mukufunabe kuti muzilandira nawo mapepala a maphunzirowa. Kugwiritsa ntchito nthawi moyenera N’zoona kuti kuphunzira maphunziro amenewa kuzikutengerani nthawi yanu ina tsiku lililonse, mwina 15, powerenga Baibulo. Komanso ola limodzi mlungu uliwonse pophunzira phunziro lililonse. Mungafunikenso kupeza nthawi yoti muyankhe mafunso. Mudzaonanso kuti Malemba amene ali m'maphunzirowa ndi osangalatsa ndiponso ofunika kutherapo nthawi ndithu powaphunzira. Muzipemphera musanayambe kuwerenga Baibulo komanso mukamaliza Musanayambe kuphunzira, muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kumvetsa mawu ake. Taonani pemphero ili lochokera m’buku la Masalmo: "Munditsegulire maso, kuti ndipenye Zodabwiza za m’chilamulo chanu" (Salmo 119:18) Tikamupempha, Mulungu adzatsegula maso athu ndipo adzatithandiza kumvetsa buku Lake, Baibulo. Zimene tidzachita mukangokhala chete, osatiuza chilichonse Tikukhulupirira kuti mukudziwa zoti pali anthu ambirimbiri padziko lonse lapansili amene akufunitsitsa kulandira ndi kuphunzira kosi ya Baibuloyi. Tikapanda kumva chilichonse kuchokera kwa inu, (mwachitsanzo mukapanda kutitumizira mayankho onse a mafunso) tidzaganiza kuti simukufunanso kupitiriza kuphunzira. Ndiye ifeyo tidzasiya kukutumizirani maphunziro ena. Ngati zikukuvutani kuyankha kapena kutumiza mapepala onse okhala ndi mayankho, chonde dziwitsani mphunzitsi wanu ndipo mufotokoze chifukwa chake. Mukatero ndiye kuti ife tidzapitiriza kukutumizirani maphunzirowa. Chomwe tikufuna n'kudziwa zoti zimene tikutumizazo zikulandiridwa komanso kugwiritsidwa ntchito pophunzira Mawu a Mulungu. Kosi Yonse ya Baibulo M’munsimu muli mitu ya maphunziro 60 a kosi imeneyi: « 1 Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kosiyi 2 Kodi ma Christadelphians ndi Ndani? 3 Baibulo ndi Buku Lothandiza 4 Uthenga Wabwino Pepala la Mafunso Na. 1 5 Mulungu Ndiponso Chilengedwe 6 Mulungu Anakonda Dziko Lapansi 7 Kubweranso kwa Yesu Padziko Lapansi 8 Zizindikiro za Kubwera kwa Yesu Pepala la Mafunso Na. 2 9 Ufumu Wanu Udze 10 Mmene Mulungu Amaonera Mbiri Yakale 11 Ufumu wa Mulungu Udzabweretsa Mtendere Padzikoli Pepala la Mafunso Na. 3 12 Malonjezo Amene Mulungu Analonjeza Abulahamu 13 Mbiri Yokhudza Ayuda, Gawo I 14 Mbiri Yokhudza Ayuda, Gawo II 15 Lonjezo la Mulungu kwa Davide Pepala la Mafunso Na. 4 16 Atate ndi Mwana 17 Moyo wa Yesu 18 Imfa ya Yesu 19 Kuukitsidwa ndi Kukwera Kumwamba kwa Yesu Khristu Pepala la Mafunso Na. 5 20 Mzimu Woyera wa Mulungu 21 Mphatso za Mzimu Woyera 22 Uchimo ndi Zotsatirapo Zake, Gawo I 23 Uchimo ndi Zotsatirapo Zake, Gawo II Pepala la Mafunso Na. 6 24 Mwachisomo, Mwapulumutsidwa 25 Kuukitsidwa kwa Akufa 26 Chiweruzo 27 Moyo Wosatha Pepala la Mafunso Na. 7 28 Angelo 29 Mdyerekezi (ziwanda) ndi Satana 30 Mdyerekezi ndi Uchimo 31 Ubatizo Pepala la Mafunso Na. 8 32 Ukwati wa Chikhristu 33 Mavuto a M’banja 34 Udindo Wathu ku Boma 35 Pemphero 36 Kuyenda M’moyo Watsopano Pepala la Mafunso Na. 9 37 Kuwerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku 38 Kusonkhana ndi Anzathu a Chikhulupiriro Chimodzi 39 Mphamvu ya Lilime 40 Kunyema Mkate Pepala la Mafunso Na. 10 41 Moyo wa Banja pa Utumiki wa Yesu 42 Vuto la Tchimo 43 Mawu a Mulungu M’moyo Wathu wa Tsiku ndi Tsiku 44 Eklesia wa Mulungu Pepala la Mafunso Na. 11 45 Mmene Timaonera Anthu Ena Zimamukhudza Kwambiri Mulungu 46 Kukonda Mnansi Wanu 47 Zimene Baibulo Limaphunzitsa pa Nkhani ya Mavuto 48 Kukhala mwa Mantha Pepala la Mafunso Na. 12 49 Kodi Kukhala ndi Mtima Wofuna Kuchita Zinthu Zotsogola ndi Wabwino? 50 Kukhala Woona Mtima Pamaso pa Mulungu ndi Mwana Wake Yesu Khristu 51 Kusonyeza Mkwiyo Komanso Kudziletsa 52 Mmene Wophunzira wa Yesu Amaonera Boma Pepala la Mafunso Na. 13 53 Kugonana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu 54 Kusankha Munthu Womanga Naye Banja 55 Mfundo Zina Zokhudza Chiweruzo Komanso Ufumu 56 Kukhala ndi Chiyembekezo pa Moyo ndi Mphatso ya Mtengo Wamtengo Wapatali Pepala la Mafunso Na. 14 57 Kuchita Zinthu Mogwirizana ndi ‘Chikhulupiriro’ Komanso Chikhristu 58 Chisomo cha Mulungu 59 Chidule cha Ziphunzitso za M’Baibulo 60 Zoyenera Kuchita Pepala Lomaliza la Mafunso Christadelphian Bible Mission, Box CBM, 404 Shaftmoor lane, Birmingham B28 8SZ, England

Chichewa