KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN Na. 4

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN  Na. 4

 

UTHENGA WABWINO

Kuwerenga : Yesaya 55 Uthenga Wabwino

Munthu aliyense amasangalala kumva uthenga wabwino. Ndipotu Uthenga Wabwino wa m’Baibulo ndi wosangalatsadi. Mawu akuti "Uthenga Wabwino" akutanthauza "uthenga wabwino" wopezeka m’mabuku anayi oyambirira a m’Chipangano Chatsopano.

 

Mabuku anayi oyambirira a mu Chipangano Chatsopano nthawi zambiri amatchedwa kuti ‘uthenga wabwino’ chifukwa cha nkhani yabwino imene ikupezeka m’mabuku amenewa. Ndi uthenga wabwino wonena za a Mbuye wathu Yesu Khristu. Iye anali Mwana wa Mulungu ndipo anabadwa mwa Mariya.

Mabukuwa ndi mbali chabe ya uthenga wabwino!

Komanso kuwonjezera pa makhalidwe a Mulungu amene Yesu anasonyeza monga chikondi ndi chifundo, koma anaonetsanso mphamvu yaikulu ya Mulungu pa zizindikiro zimene iye anachita. Chinthu china chochititsa chidwi kwambiri n’chakuti iye sanachitepo tchimo ngakhale pang’ono. Chifukwa cha zimenezi, iye anaukutsidwa kwa akufa. Iye ndi munthu yekhayo amene anaukitsidwa kwa akufa amene adakali ndi moyo mpaka pano.

 

Uthenga wabwino umenewu si wonena za Yesu Khristu yekha ayi, koma ndi uthenga wabwino kwa ifenso. Mwa imfa yake ndi kuuka kwa akufa kwake, Yesu watsegula njira kwa ife anthu ochimwa kuti machimo athu akhululukidwe. Iye watipatsa ife chiyembekezo cha moyo pamene timwalira. Tsono uthenga wabwino ndi uwu wakuti ife sitiyeneranso kukhala mwa chisokonezo monga momwe tikukhalira pano. Mulungu watipatsa njira yakuti tipulumuke ku uchimo ndiponso ku imfa.

Pali zambiri zokhudza uthenga wabwino!

Panopa Ambuye Yesu Khristu ali kumwamba, koma adzabweranso pano padziko lapansi posachedwa. Chibvumbulutso 1:7 ikunena za kubweranso kwa Yesu:

"Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse apa dziko adzamlira Iye. Terotu. Amen."

Pamene Yesu Khristu adzabweranso, iye adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pano pa dziko lapansi. Dziko lapansi lidzakhala malo osiyana ndi momwe likuonekera tsopano. Tauzidwa kuti kudzakhala.

sikudzakhalanso nkhondo;

sikudzakhalanso njala;

sikudzakhalanso kulira;

sikudzakhalanso uchimo;

sikudzakhalanso imfa.

Ambuye Yesu akadzakhala mfumu yadziko lonse lapansi, padzakhala chilungamo ndiponso mtendere. Dziko lapansi lidzapereka zipatso zambiri, mwakuti njala sidzakhalaponso:

"Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena" (Yesaya 25:8).

Mulungu adzatipatsa ufumu pompano padziko lapansi. Imeneyi mphatso yochititsa chidwi imene wapereka. Inde tikudziwa kuti pali malamulo ofuna kutsatira kuti tilandire mphatso imeneyi, ndi chifukwa chake kuli kofunikira kuwerenga mawu a Mulungu kuti tidziwe zimene Mulungu akufuna kuti ife tichite pa moyo wathu masiku ano.

Anthu a m’nthawi ya Chipangano Chakale ankadziwa Uthenga Wabwino

Tikamawerenga za Abrahamu, timauzidwa kuti iye anauzidwa uthenga wabwino (Agalatiya 3:8). Chifukwa cha chikhulupiriro chake ndi kumvera kwake, Mulungu anapereka malonjezano kwa Abrahamu. Iye anauzidwa kuti adzalandira dziko la Israyeli ngati cholowa chake kwa muyaya. Abrahamu anakalamba mpaka anamwalira, osalandira mbali iliyonse ya dziko limene Mulungu anamulonjeza lija.

Ife tikudziwa kuti Mulungu amasunga malonjezano ake nthawi zonse.Tsopano kuti akhale m’dziko limene Mulungu anamulonjeza, Abrahamu ayenera kuuka kwa akufa. (Tikudziwanso kuti Abrahamu anali kukhulupirira za kuuka kwa akufa – Ahebri 11:19) Tsono lonjezano la moyo pamene munthu amwalira linaperekedwanso kwa Abrahamu.

 

Dziko limene Abrahamu analonjezedwa lidzakhala maziko a ufumu wa m’tsogolomo. Abrahamu adzaukitsidwa kwa akufa ndi kudzakhala mu ufumu wa Mulungu pano pa dziko lapansi pamene Ambuye Yesu Khristu adzabweranso. Tsono Abrahamu anali kudziwa za uthenga wabwino wa ufumu umene ukubwerawu ndipo anali kudikirira ufumuwo (Ahebri 11:10).

 

Nayenso Mfumu Davide anali kudikirira nthawi imene mbewu yake idzalamulira ku Yerusalemu."*

 

Mudzaphunzira zambiri za malonjezano amene Mulungu analonjeza Abrahamu ndi Davide m’maphunziro a m’tsogolomo.

Kodi Ambuye Yesu Khristu adzabweranso liti?

Tsiku limene Yesu adzabwere sitikulidziwa. Koma tikudziwa, kuchokera pa zinthu zimene zikuchitika m’dziko lapansi lero lino, kuti sipapita nthawi yayitali asanabwerenso pano pa dziko. Ayuda analibe dziko lawolawo kwa zaka pafupifupi 2000. Koma pakali pano abwerera m’dziko lawo lakale, ndipo m’chaka cha 1948 dziko la Israyeli linakhazikitsidwa. Izi ndi zimene zinali kufunika kuti zichitike Ambuye asanabwerenso.

Masiku ano, padziko lapansi pano pali ziwawa zambirimbiri ndiponso zosaneneka, ndipo anthu amachita chili chonse chokondweretsa iwo eni mopanda kuchita mantha kapena manyazi. Pali nkhondo, njala, matenda oopsa pa dziko lonse lapansi. Anthu ambiri ali kuchita mantha ndi tsogolo lawo, monga momwe Yesu ananenera m’mene zinthu zidzakhalire m’tsogolomu:

 

"Anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi" (Luka 21:26).

Yesu ananenanso kuti zinthu zimenezi pakuona zinthu zimenezi zikadzayamba kuchitika padziko lapansi, ndiye kuti watsala pang’ono kubwera. Mudzaphunzira zambiri za izi m’maphunziro a m’tsogolomo.

Yesu adzabweranso monga Mfumu ya padziko lonse lapansi

Yesu anamuuza Pontio Pilato kuti iye anabadwa kudzakhala mfumu. Pa mtanda pake panalembedwa mawu awa: ‘Yesu Mnazarayo, Mfumu ya Ayuda’. Koma sikuti adzangokhala mfumu ya Ayuda okha ayi. Adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Mulungu ananena za ichi zaka zambirimbiri zapitazo. Iye anati:

"Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja. Ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi" (Salmo 72:8).

Kodi chidzachitike n’chiyani Yesu akadzabweranso padziko lapansili?

Yesu adzaukitsa akufa ndi kuwaweruza. Anthu okhawo amene anachita chilungamo cha Mulungu adzalandira moyo wosatha ndi malo mu Ufumu pano pa dziko. Iwowa adzathandiza Yesu kulamulira dziko lapansi.

Pa nthawi imeneyo, Yerusalemu adzakhala likulu la dziko lonse, ndipo Yesu Khristu adzalamulira dziko lonse lapansi. Idzakhala nthawi ya chisangalalo chachikulu. Yesu ananena ndi ophunzira ake kuti azipemphera kuti nthawi iyi ifike. Pa nthawi iye akupemphera, anati:

 

"Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano." (Mateyu 6:10-13).

 

Pakadzapita zaka chikwi chimodzi Ambuye atabwera, uchimo ndiponso imfa zidzatheratu. Mulungu adzakhala “Zonse mu zonse” – monga m’mene Iye anakonzera pachiyambi penipeni:"Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja." (Habakuku 2:14) Uthenga Wabwino wosangalatsa ndi wakuti ifeyo tingadzakhale mu Ufumu umenewu

Kodi tingatani kuti tidzakhale nawo mu Ufumu wa Mulungu padziko lapansili?

Tiyenera kumakumbukira kuti anthu onse ndi ochimwa, ndipo tikuyenera kuchitapo kanthu. Pamene mtumwi Paulo anali kwa Atene, ananena kuti:

"Nthawi za kusadziŵako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima . . . chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa" (Machitidwe 17:30, 31).

Mulungu akulamula anthu onse kuti atembenuke mtima. Kutembenuka mtima ndi kusiya kudzikondweretsa wekha ndi kuyesetsa kukondweretsa Mulungu. Ife tonse ndife anthu ochimwa, chifukwa cha ichi tiyenera kutembenuka mtima ndi kubatizidwa m’madzi. Tiziyesetsa kukhala monga m’mene Yesu anali kukhalira. Kwa iwo amene achita izi, Yesu Khristu adzawapatsa moyo wosatha pamene Iye adzabweranso.

(N’kutheka kuti mwazindikira kale kuti uthenga wabwinowu sikuti ukunena za kupita kumwamba – kupita kumwamba si chiphunzitso cha buku lopatulika. Uthenga wabwino ukunena za moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu padziko pano.)

Mwachidule

1. Baibulo lonse likunena za uthenga wabwino. Anthu okhulupirira m’chipangano chakale ndi chatsopano anamvetsa bwino za uthenga wabwinowu.

2. Kuti apulumutse anthu, Yesu anakhala ndi moyo wangwiro ndi kufa modzipereka.

3. Mulungu anaukitsa Yesu kwa akufa – ndipo kenaka Yesuyo anakwera kupita kumwamba.

4. Ambuye Yesu adzabweranso kudzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pano pa dziko.

5. Iye adzaukitsa akufa ndi kuwaweruza. Amene ati alandiridwe adzapatsidwa moyo wosatha mu ufumu wake pano pa dziko lapansi.

6. Tikakhulupirira Uthenga Wabwinowu tiyesetsa kutsatira chitsanzo cha Ambuye Yesu.

Mavesi oyenera kuwerenga : Yesaya 45:18; Zekariya 9:9; Mateyu 25:31-34;

1 Akorinto 15:28

Lowezani : Genesis 12:1-3

" Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kumka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi."

Christadelphian Bible Mission A Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Swahili Title: 
Injili - Somo la 04
English files: 
Swahili Word file: 
PDF file: 
Hebew file: