KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN Na. 6

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN  Na. 6

 

 

MULUNGU ANAKONDA DZIKO LAPANSI

Kuwerenga : Yesaya 53

Kodi vuto n’chiyani ndi dziko lapansili?

Zikuonekeratu kuti chinachake chinalakwika m’dziko lapansi limene tikukhalamoli. Tsiku lililonse timamva nkhani zomvetsa chisoni zokhudza upandu ndi chiwawa. Padziko lonse lapansi pali nkhondo ndi zokhazokha. Matenda oopsa akufalikira m’dziko lonse msanga. Anthu ambiri akufa ndi njala, chikhalirecho anthu ena ali nacho chakudya chambiri kuposa chimene angakwanitse kudya. Mafumu ndi atsogoleri ambiri samakhudzidwa ndi m’mene anthu amene iwo akuwalamulira akukhalira.

Zonsezi zikuchitika nthawi ndi nthawi. Panopa tafika pozizolowera, tikungoona kuti ndi mmene zinthu zimakhalira. Koma tikakhala pansi ndi kuganiza, tikhoza kufunsa “Chifukwa chiyani mavutowa akuchulukira?”

Zoonadi, pamene Mulungu analenga dziko lapansi – ndi kulipanga kukhala malo angwiro kuti anthu azikhalamo – Iye anafuna kuti akhale m’malo abwino osati ngati m’mene ziliri pakali pano kuti dziko lino lili ndi mavuto a mitundumitundu ndipo sizikudziwika kuti tikulowera kuti.

Chiyambi cha mavuto

Pachiyambi, Mulungu analenga munthu ndipo anam’patsa dzina loti Adamu. Mulungu Iye anaphunzitsa munthuyo njira zake. Ndipo Mulunguyo anam’patsa Adamu lamulo losavuta kuti alitsatire. Monga mmene bambo amayembekezera kuti ana ake azimumvera, Mulungu ankayembekezera kuti Adamu azimumvera. Mulungu anati:

"Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu" .(Genesis 2:16-1 7).

Adamu sanamvere Mulungu. Zotsatira za kusamvera kwake zinabweretsa imfa, monga momwe Mulungu ananenera kuti zichitika. Izi zinapangitsanso kuti zikhale zosavuta kuti Adamu achimwe nthawi yina, ndipo kuonjezera apo, munthu aliyense amabadwa ndi tchimo.

Pa Aroma 5:12 pali mawu akuti:

//. . . monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa."

Adamu anachimwa, ndipo chifukwa cha kuchimwako, anafa. Taonani kuti Mulungu SANALONJEZE Adamu ndi Hava kuti adzapita kumwamba pamene iwo amwalira. Imeneyo ikanakhala mphoto. Iwo anauzidwa kuti adzafa, ndipo chimenechi n’chilango, osati mphoto.

Zimenezi zimatichitikiranso ifeyo

Ifenso timachimwa ndi kufa. Pamene mumawerenga Yesaya 53, kodi munaona mawu ali pa vesi 6?

" tonsefe tinkangoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa. Aliyense analowera njira yake."

Mneneri Yeremiya akutiuza ife nkhani imodzimodzi yomweyo, koma m’mawu olekana, pamene iye akuti:

"Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika" (Yeremiya 17:9).

Zinthu zonsezi zimaziwerenga m’Baibulo, ndipo timadziwa kuti zimenezi ndi zoona tikaona zimene zimachitika pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Nayenso mtumwi Paulo anati:

"Pakuti ndidziwa kuti m’kati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino" (Aroma 7:18).

Aliyense angagwirizane ndi zimene Paulo ananena chifukwa nthawi zambiri sitimatha kukhala anthu abwino monga momwe tingafunire kukhala. Ndipo anthu ambiri safuna n’komwe kukhala anthu abwino.

Nanga mavutowa angathetsedwe bwanji?

Adamu asanachimwe, anali kukhala mwa mtendere ndi Mulungu. Koma ubwenzi umenewu unasokonezeka. Adamu anachimwa, ndipo sakanatha kukhala pa ubwenzi ndi Mlengi wake.

N’kutheka kuti mwina Adamu sanali kudziwa kuti ndi mavuto aakulu motani amene iye anali kuyambitsa pamene ankachimwa. Atangochimwa, zaka zikwizikwi zotsatirazo, ali yense wa mbewu yake ( kuphatikizapo inu ndi ine) watsatira mapazi ake pochimwa (kupatula Yesu yekha). Ndipo chifukwa ndife tonse ochimwa, ubwenzi wathu ndi Mulungu unasokonezeka.

Zinthu zafika poipa kwambiri kuposa izi. Kuyambira pa kubadwa kwathu takhala tiri m’banja la Adamu ndipo talandira nawo zotsatira za kuchimwa kwake. Ndife zolengedwa zakuti tidzafa kuyambira pa chiyambi chathu. Ndipo timapitirizabe kuononga zinthu powonjezera kuchita machimo athuathu.

Zinthu zafika poipa mwakuti anthu sangathe kuchita chilichonse kuti adzipulumutse iwo wokha.

Tidzapulumutsidwa mwa chisomo cha Mulungu

Mulungu, mwa chisomo ndi chikondi chake, sanasiye anthu kuti afe m’machimo awo ayi. Mulungu anapeza njira yakuti anthuwo abwererenso kwa Iye. Tikuwerenga pa Yohane 3:16 kuti:

"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupilira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha".

Mtumwi Paulo ananena kuti:

"Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiliro" (Aefeso 2:8).

Chisomo cha Mulungu n’chikondi chake chimene amatipatsa ife kwa ulele, kutikhululukira ife chifukwa cha Khristu. Mulungu wachitapo mbali Yake. Iye watipatsa ife Yesu. Watsegula njira.

Njirayo ndi “kudzera m’chikhulupiriro”. Ngati sitikhulupirira mawu a Mulungu, sizingatheke tikhale ndi chisomo Chake:

"Koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumufuna Iye" (Ahebri 11:6).

Yesu ndiponso mtanda

Yesu sanachite tchimo ngakhale limodzi. Iye anali kuchita zinthu zimene zinali kukondweretsa Mulungu nthawi zonse. Koma ngakhale izi zinali chonchi, zinapezeka kuti anamupachika pamtanda. Mulungu sanamupulumutse iye ku imfa yoopsa imeneyi. Vesi lina limene tawerenga mu Yesaya 53 lanena kuti:

"Ambuye aika pa Iye kusayeruzika kwathu tonse."

Baibulo likutiphunzitsa kuti kudzera mu imfa ya Yesu Khristu pamtanda, komanso pa kumvera chifuniro cha atate wake, zikhoza kutheka kuti machimo athu akhululukidwe, ndipo kenako tingakhale ndi chiyembekezo cha moyo.

Pali chinthu chochititsa chidwi pa nkhani imeneyi – chikondi cha Mulungu pakupereka mwana wake yekhayo, ndi chikondi cha Yesu pa kumvera chifuniro cha atate wake. Pakukhulupirira iye , tikhoza kukhala ndi moyo. Ichi ndicho chiyembekezo chimene chili mu mtima wa Mkristu aliyense.

Kodi inuyo muli m’banja liti?

Banja ndi chinthu china chimene tiyenera kuchiganizira pa nkhani ya chipulumutso. Adamu anali mutu wa banja la munthu ndipo kuchokera mwa iye, pamodzi ndi mkazi wake Hava, ife tonse tinabadwa. Adamu anachimwa ndipo anabweretsa imfa kwa anthu onse, motero anthu onse amafa. Ambuye wathu Yesu Khristu anayambitsa banja latsopano. Akanachita ichi pokhapokha pogonjetsa uchimo. Izi zinafunika nsembe yangwiro kuti agonjetse temberero limene Adamu anabweretsa kwa anthu onse. Yesu ndiye amene anali nsembe yangwiro imeneyo.

Apa tsopano tikuonapo mabanja awiri – banja la Adamu ndi banja la Khristu. Tonse tabadwa m’banja la Adamu ndipo ngati sitichitapo kanthu za ichi ndi kudzapezeka kuti tafa m’banja lomwelo la Adamu, ndiye kuti tidzaonongeka kwa muyaya. Tiyenera tichitepo kanthu! Khristu akufuna ife kuti tikhale mbali ya banja lake ndipo tikhoza kuchita ichi pa kuphunzira za Yesu ndi cholinga cha Mulungu, ndipo kenako tibatizidwe. Ubatizo ( monga momwe mudzaphunzira m’tsogolo ndi chiphiphiritso cha kufa ndi kuuka kukhalanso ndi moyo. Zimenezi zimatanthauza kuti tafa ku banja la Adamu ndipo tauka ndi kukhalanso ndi moyo ku banja la Khristu.

Mukawerenga pa Aroma 5:12, 18-21 mudzaona m’mene mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito mawu amenewa a mabanja.

Ife tiyenera tithokoze Mulungu ndi Ambuye Yesu pokonza kuti zitheke kuti ife tithawe kuchokera ku banja la Adamu.

 

 

ADAMU amene anachimwa

 


YESU KHRISTU amene sanachimwe

  

 

BANJA LA ANTHU amene akupitiriza kuchimwa

 BANJA LA MULUNGU amene safuna uchimo ndipo amakhululukira anthu olakwa

 

KUKHALA MOYO

 


KUPULUMUTSIDWA mwa Chikhulupiriro komanso Kumvera

 


MOYO

KUFA

  

 

AMAFA KWA MUYAYA

 


ANAUKITSIDWA KWA AKUFA N’KUKHALA NDI MOYO KWA MUYAYA

  

 

Kukhulupirira mwa iye

Aliyense akudziwa kuti ngati akufuna kukondweretsa Mulungu, ayenera kukhulupirira zimene Iye watichitira kudzera mu imfa ya Yesu. Lemba la Yohane 3:16 likutiuza kuti:

"Yense wakukhulupirira Iye (Yesu) asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha."

Izi sizitanthauza kuti ife pongonena kokha kuti “ndimakhulupirira Yesu” ndiye kuti tidzapulumutsidwa ku machimo ndi imfa ayi. Zikhoza kuoneka choncho poyamba, koma taimani ndi kuganiza bwino za chinthuchi. Ngati timakhulupiriradi chinthu chinachake, timachita zinthu zogwirizana ndi chinthucho. Ngati mwana wathu wadwala ndipo tikukhulupirira kuti dokotala akhoza kumuthandiza, sitimangonena kokha kuti, “ndikukhulupirira kuti dokotala akhoza kumuthandiza”, kenaka n’kungomusiya mwanayo kuti papitirizebe kudwala ayi. Timathamangira kwa dokotalayo, ndipo chifukwa chakuti timamukhulupirira, timachita chilichonse chimene dokotalayo watiuza.

Apa ndi chimodzimodzinso pa kukhulupirira mwa Yesu. Ngati tikhulupiriradi, tidzafunafuna kuti tipeze chimene iye afuna kuti ife tichite, ndipo tichite ndi mphamvu ndi nzeru zathu zonse. Ndipo kumvera kumayambira pobatizidwa pomira m’madzi thupi lonse, monga m’mene analamulira.

Pokhapokha ngati tichita izi, tikhoza kukhala nawo pa gulu la anthu akuti ‘sadzaonongeka, koma akhala nawo moyo wosatha’.

Mphatso ya moyo wosatha

Moyo mu ufumu wake ndi mphatso ya Mulungu kwa omwe akhulupilira mawu ake ndi kuyetsetsa kumvera Iye. Anthu oterewa amapemphera tsiku ndi tsiku kuti, "Ufumu wanu udze".

Pamene Yesu adzabwera, adzakhazikitsa ufumu wa Mulungu. Iye adzakhala pa mpando wa Davide ku Yerusalemu, kulamulira pa dziko lonse lapansi. Kenaka anthu amene akhala akuyembekezera Iye, amene ayesetsa kukhala monga m’mene Mulungu afunira, adzapatsidwa mphatso yaikuru kuposa mphatso zonse, moyo wosatha. Choncho sadzafanso.

Adzakhala ndi moyo kwa muyaya ndi kumathandiza Ambuye Yesu pa ntchito yawo yolamulira dziko lapansi.Kenaka adzayimba mawu amene tikuwawerenga pa Chibvumbulutso:

"Ndipo ayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikilo zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko" (Chibvumbulutso 5:9,10).

Mwachidule

1. Mavuto onse ali m’dziko lapansi adza chifukwa cha kuchimwa kwa munthu, zinthu zimene tazitenga kuchokera kwa Adamu ndi Hava.

2. Chifukwa cha uchimo, tonse timafa, ndipo imfa ndi chilango.

3. Uthenga wabwino ndi wakuti Mulungu wapereka njira kwa anthu kuti apulumutsidwe ku zotsatira za uchimo.

4. Ife sitingathe kudzipulutsa tokha tingayese motani. Tidzapulumutsidwa chifukwa cha chisomo cha Mulungu, ndipo chipulumutso ndi mphatso.

5. Njira ya chipulumutso ndi kudzera kwa Ambuye Yesu ndipo izi zinatheka chifukwa cha nsembe ya Yesu.

6. Ife mbali yathu ndi kukhulupirira motsimikiza.

7. Amene aonetsa chikhulupiriro chenicheni amachitapo kanthu pobatizidwa ndi kuyesetsa kumvera ndi kutsatira Ambuye Yesu.

8. Mulungu akulonjeza kuti amene akhulupilira ndi kutsatira Yesu Khristu adzakhala ndi moyo kwa muyaya mu Ufumu wake pano pa dziko lapansi ndipo Yesu ngati Mfumu yawo.

Machaputala oyenera kuwerenga : Aefeso 2

Lowezani : Yohane 3:16

"Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha."

Christadelphian Bible Mission Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Swahili Title: 
Mungu aliupenda ulimwngu - Somo la 06
Swahili Word file: 
PDF file: 
Hebew file: 
Arabic file: