KUBWERANSO KWA AMBUYE YESU PADZIKOLI

 

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN       ——————             Na. 7

 

KUBWERANSO KWA AMBUYE YESU PADZIKOLI

Wengani : Machitidwe 1

Zaka zokwana zikwi ziwiri zapitazo

Yesu anali atapachikidwa. Otsatira ake onse anakhumudwa ndi zimene zinachitikazi. Chiyembekezo chawo chonse chinali pa iye – koma tsopa no pa nthawi iyo iye anali ataikidwa m’manda.

Koma —   pa tsiku lachitatu, Yesu anatuluka m’manda ali wamoyo!

Izi zitachitika otsatira ake onse anakumbukira mawu amene ananena kwa iwo iye asanaphedwe:

"Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe " (Yohane 16.20).

Chimwemwe chake chinali chachikuru zedi pamene anawonanso kachiwiri Ambuye wawo wokondedwa uja!

"Pamenepo akuphunzira anakondwera pakuona Ambuye" (Yohane 20:20). Ophunzirawo anakondweratu kwabasi!

Yesu atapita kumwamba

Tiyeni tiwerengenso mavesi asanu ndi atatu oyambirira za Machitidwe 1. Tapezani chithunzi cha momwe atumwi anasangalalira pa masiku makumi anayi amenewo, pamene Yesu analinso pakati pawo. Taganizirani za anthu amenewo, patatha masiku makumi anayi, atayima mu tsinde mwa phiri la Azitona, Yesu ali pakati pawo. Mwadzidzidzi, anachotsedwa pakati pawo kupita m’mwamba. Iwo anamuwona pamene iye anali kusiyana nalo dziko lapansi, ndipo kenaka Yesu anabisidwa ndi mitambo. Yesu wachotsedwanso pakati pawo ulendo wachiwiri.

Inde, pa nthawi yotengedwa Yesu kachiwirika, ophunzira  ake sanakhumudwe ayi. Luka akunena kuti,

" ...pakuwadalitsa Iye analekana nawo, natengedwa kumka Kumwamba, Ndipo anamlandira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu." (Luka 24:51-52).

Chinsinsi chimene chinawathandiza kukhalabe ndi chimwemwe

N’chifukwa chiyani iwo anali ndi chimwemwe pamene iye analekana nawo kachiwiri? Mbali ina ndi chifukwa chakuti Yesu anapereka lonjezo kwa iwo. Iye anati kwa iwo:

" ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano" (Mateyu 28:20).

Izitu zinali kutanthauza kuti ngakhale ophunzirawo sanali kutha kumuona Iye pamene anakwera kumwamba, Yesuyo anali kutha kuwaona ndi kuwasamalira iwo nthawi zonse.

Komabe, chimwemwe chawocho sichinabwere pa chifukwa chokhachi ayi. Pamene iwo anali kupenyerera Iye akupita kumwamba, angelo awiri anabwera kwa iwo ndi uthenga nati:

" Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba" (Machitidwe 1:11).

Ophunzirawo ali m’njira kubwerera ku Yerusalemu kuti akatumikire malamulo a Ambuye wawo, anadziwa mosapeneka kuti Yesu mwini yekha adzabweranso pano pa dziko lapansi. Ichi ndi chinthu chimene chinawachititsanso kuti akhale ndi chimwemwe.

Mawu a Yesu

Zonsezi zinachitika pafupifupi zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo, ndipo Yesuyo sanabwerebe mpaka pano. Koma adzabwera.  Iye mwini wake ananena choncho.  Pa Luka 21:27 iye akunena za kubwera kuchokera mumtambo,, ndi mphamvu ndi ulemelero waukuru zedi.

(Kodi mukukumbukira kuti pamene anapita mumtambo angelo ananena kuti adzabweranso “momwemo monga munamuona” alinkupita kumwamba?)

Mafanizo ambiri akunenanso za kubwera kwake kachiwiri. Taonani, mwachitsanzo, fanizo la pa Mateyu 25:1-13. Apa akunena za mkwatibwi, ngakhale apa akunena za ukwati ife tiribe bvuto liri lonse pomvetsa nkhaniyi.  Mkwati ndi Ambuye Yesu Kristu, ndipo nkhaniyi ikutichenjeza ife  kuti pamene Iye adzabweranso, padzakhala ena amene sadzamukonzekera Iye.

Tawonani pa vesi 13. Yesu sanena kuti, “Simukudziwa ngati Mbuye wanu adzabwera kapena ayi”.  Kubweranso kwake ndi chinthu chosakaikira ndi pang’ono pomwe.Koma Iye akunena kuti:

"Pakuti simudziwa tsiku lache, kapena nthawi yache pamene mwana wa munthu adzadza".

Petro anapereka umboni

Pasanapite masiku ambiri ndithu Yesu atakwera kumwamba, pamene tiwerenga za Petro m’kachisi wa ku Yerusalemu, akuyankhula  molimba mtima kwa Ayuda amene anakonza kuti Yesu apachikidwe. Pa Machitidwe 3:19-20 Petro akuyankhula kwa Ayuda kuti::

" Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye, ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Kristu Yesu."

Komanso Petro ananena za kubwera kwa Kristu mu kalata amene analembera okhulupilira. Pa 2 Petro 3:4  iye akulemba za iwo amene anganene  posakhulupilira,

"Liri kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe".

Mwina mwamvapo anthu akugwiritsa ntchito mawu ofanana ndi amenewa kwambiri. Koma Mulungu mwini wache walonjeza kutumiza Ambuye, ndipo tikudziwa kuti adzasunga lonjezan lake. Petro anapitiriza pa vesi ya 9 ndi 10 pamene ananena kuti:

"Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu,

 wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa; Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala. . ."

Umboni umene Paulo anapereka

Panthawi ina, Yesu mwini wache anaonekera kwa mtumwi Paulo, ndipo anamutuma iye kukalalikira anthu ena. Paulo amanena kuti uthenga wabwino umene iye analalikira unaperekedwa ndi Yesu Kristu. Ndipo Paulo anaphunzitsa za kubweranso kwa Ambuye. Pa 2 Timoteo 4:1 tikuwerenga kuti:

“Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake. . ."

Paulo analemba makalata awiri opita ku mpingo wa ku Tesalonika. Mudzapeza makalatawa m’buku lopatulika lanu. Makalatawa ali ndi mitu isanu ndi itatu, ndipo – chodabwitsa ndi ichi kuti- m’mutu uli wonse Paulo akutchula za kubwera kwa Yesu.

Pa 1 Atesalonika 4:16 Paulo akukamba za kuuka kwa akufa pa nthawi imene Yesu adzabweranso:

"Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka."

Koma pa 2 Atesalonika 1:7,8,  Paulo akunena za m’mene Yesu adzakhalira...

". . . pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake; m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu".

Apa akunena za Yesu kuti adzabwera kudzalanga anthu ena; koma tikapitiriza kuwerenga, tipeza kuti Paulo akunenanso za anthu ena amene Yesu akubwera kudzawapatsa chimwemwe, popeza adzabwera. “kudzayamikiridwa ndi onse akukhulupilira”.

Kodi Yesu adzachita chiyani akadzabwera?

Kubwera kwa Yesu kudzasintha miyoyo ya anthu onse amene ati adzakhale ndi moyo pa nthawi imeneyo. Idzakhala nthawi yochititsa chidwi ndi yonthunthumiritsa kwa

(a) Okhulupilira amene akulondera ndi kudikira kubwera kwake;

(b) Onse amene adzakhala ndi moyo pa nthawi imeneyo, koma sadziwa uthenga wabwino woona;

(c) Mtundu wa a Israyeli.

Tiyeni tione magulu amenewa, lilonse palokhapalokha:

(a) Okhulupilira enieni (amene ‘ali mwa Kristu’) ndi amene akudikira kubwera kwake:

Yesu adzaukitsa akufa onse amene anafa m’chikhulupiliro, kenaka ndi kusonkhanitsa okhulupilira onse amane ati akhale ndi moyo pa nthawiyo. '*

"Taonani ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika." (1 Akorinto s 15:51,52)

Anthu onse amene ali osakhulupirika adzakanidwa, koma kwa okhulupirika, kudzakhala chimwemwe chachikuru. Yesu adzawapatsa iwo moyo wosatha.Monga momwe Paulo anenera, akuti Iye “adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lache la ulemelero” (Afilipi 3:21). Monga iye, iwonso adzagawana nawo moyo wosatha, moyo wopanda ululu ndi mazunzo ali onse. Iwo adzathandiza Yesu  pa ntchito ya kuphunzitsa za Mulungu kwa mitundu yonse,  ndiponso kuthandiza anthu a dziko lapansi kuti alandire  chikondi  chachikuru cha Yesu ndi kuyenda m’njira zake.

(b) Anthu a padziko lapansili:

Pa nthawi yakubwera kwa Yesu Kristu, chiweruzo cha Mulungu chidzatsanuliridwa kwa anthu ochimwa, ndipo padzakhala nthawi ya mabvuto akuru pa dziko. Izi ndi zoopsya kwambiri, koma ndi zofunikabe kuchitika. Popanda chiweruzo cha Mulungu, dziko lapansi siridzatembenukira kwa Iye, ndi kulandira Ambuye Yesu ngati mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.

Akatha kutsanulira chiweruzo cha Mulungu, anthu a dziko lapansi adzakhala okonzeka kulandira Yesu ngati Mfumu yawo. Iye adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pano pa dziko. Ulamuliro wache udzakhala wanzeru ndi wachikondi, ndipo adzasamalira osauka ndi amene akufuna chithandizo. Tapitani pa Masalmo 72 ndipo muwerenge mutu wonse. Mutu umenewu udzakupatsani chithunzi cha ulamuliro wa Yesu. Mutuwu ukunena za momwe adzasamalira osauka ndi osowa chithandizo chiri chonse.

Anthu a dziko lapansi amene ati apulumuke posakhudzidwa ndi chiweruziro cha Mulungu adzakhala mu Ufumu wa Mulungu ndipo adzalandira madalitso ambiri. Komabe anthu amenewa chilakolako chochita uchimo chidzawakhalira ndipo azifa monga ngati momwe aliri anthu lero, ngakhale masiku a moyo wawo azikhala ambiri kuposa momwe ziliri pano. Pa nthawi ya moyo wawo, adzaphunzitsidwa njira za Mulungu ndi kukhala ndi mwayi wolandira kapena kukana Ambuye Yesu. Pakatha zaka chikwi (1000) Yesu akulamula, padzakhala chiukiriro ndi chiweruziro chachiwiri kwa iwo amene anali pa dziko m’zaka chikwi zimenezi. Ena adzapatsidwa moyo wosatha, ndipo ena adzakanidwa. Potsiriza, imfa idzachotsedwa pa dziko kwa muyaya.

(c) N’chiyani chidzachitikire Ayuda?

Yesu adzabweranso pa nthawi imene mtundu wa Israyeli udzakhala pa mabvuto osaneneka. Adzakhala atazunguliridwa ndi adani kumbali zonse. Yesu, ndi mphamvu yache yopatsidwa ndi Mulungu, adzagonjetsa amene adzamenyana ndi  Aisrayeli. Ndipo Ayuda ambiri adzazindikira  tsopano kuti Yesu ndiye Mfumu yawo imene inalonjezedwa kwa iwo – ndipo anampachika! Mneneri Zekariya akuti iwo “adzandipenyera ine amene anandipyoza; nadzamlira” (Zekariya 12:10).

Anthu amenewa adzalandira Yesu mosangalala monga mfumu.

Ambuye adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu, ndipo Ayuda adzakhala mtundu waukuru mwa mitundu yonse. Likulu la dziko lawo, Yerusalemu, lidzakhala likulu la dziko lonse lapansi. Lidzakhala maziko a kupemphera anthu onse. Idzakhala nthawi ya chimwemwe kwa Ayuda, atabvutika kwambiri m’mbuyo monsemu.

Chimenechitu ndi chikondi, chimwemwe ndi mtendere wochuluka zimene zidzasefukira kuchokera ku likulu la dziko lapansi!

N’chiyani chidzachitikire inuyo ndi ineyo?

Werenganinso fanizo la anamwali khumi, pa Mateyu 25:1-13. Ngati ife tiri ochenjera, monga anamwali asanu ochenjera  mu fanizoli, tidzakhala tikuphunzira mawu a Mulungu, ndi kumakonzekera tsopano lino kubwera kwa Yesu. Pamene Yesu ananena kwa mtumwi Yohane,  “Indetu; ndidza msanga” (Chibvumbulutso 22:20), iye anayankha, “Idzani Ambuye”.

Mwachidule

1.   Yesu Kristu adzabweranso pa dziko lapansi lino.

2.   Tiri ndi chitsimikizo chonse pa nkhaniyi, popeza Yesuyo anachita kunena yekha.

3.   nawonso angelo ananena chimodzimodzi. Petro, Paulo, ndi Yohane ananenanso chimodzimodzi.

4.   Iyeyo akamabwera, adzapereka moyo wosatha kwa omtsatira ake amene anali okhulupirika.

5.   Iyeyo adzapanga mtundu wa Israyeli kukhala mtundu waukuru kuposa mitundu yonse.

6.   Adzaphunzitsa njira za Mulungu kwa anthu onse a dziko lapansi.

7.  Ngati ife tiri ochenjera, tidzakhala tikukonzekera kubwera kwake tsopano lino.

Machaputala oyenera kuwerenga: 1 Atesalonika  4; Danieli 12:1-4; Mateyu 25:1-13

Lowezani vesili : Machitidwe 1:11

Angelo anati: " Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kumka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba."

 

 

Swahili Title: 
Kurudi kwa Bwana Yesu Duniani - Somo la 07
Swahili Word file: 
PDF file: 
Hebew file: 
Arabic file: