Eksodo
1 Ndipo maina a ana a Israyeli, amene analoŵa m’Aigupto ndi Yakobo ndi awa, analoŵa munthu ndi banja lake: 2 Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda; 3 Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini; 4 Dani ndi Nafitali, Gadi ndi Aseri. 5 Ndipo amoyo onse amene anatuluka m’chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi aŵiri; koma Yosefe anali m’Aigupto. 6 Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse. 7 Ana a Israyeli ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nawo. 8 Pamenepo inaloŵa mfumu yatsopano m’ufumu wa Aigupto, imene siinadziŵa Yosefe. 9 Ndipo ananena ndi anthu ake, Tawonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, achuluka, natiposa mphamvu. 10 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m’dzikomo. 11 Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu awo. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramese. 12 Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana a Israyeli. 13 Ndipo Aaigupto anawagwiritsa ana a Israyeli ntchito yosautsa; 14 nawawitsa moyo wawo ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zawo zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa. 15 Ndipo mfumu ya Aigupto inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifra, dzina la mnzake ndiye Puwa; 16 ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwawone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo. 17 Koma anamwino anawopa Mulungu, ndipo sanachita monga mfumu ya Aigupto inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo. 18 Ndipo mfumu ya Aigupto inaitana anamwino, ninena nawo, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana aamunawo akhale ndi moyo? 19 Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aigupto; pakuti ali ndi mphamvu, nawona ana asanafike anamwino. 20 Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu. 21 Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anawopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja. 22 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m’nyanja, koma ana aakazi onse alekeni amoyo.
2 Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi. 2 Ndipo anaima mkaziyo, nawona mwana wamwamuna; mmene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu. 3 Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m’mbali mwa nyanja. 4 Ndipo mlongo wake anaima patali, adziŵe chomwe adzamchitira. 5 Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m’nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m’mbali mwa nyanja; ndipo iye anawona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge. 6 Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo, tawonani, khandalo lirikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. 7 Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo? 8 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo. 9 Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa. 10 Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m’madzi. 11 Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu awo; ndipo anawona munthu M-aigupto ali kukantha Mhebri, wa abale ake. 12 Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anawona kuti palibe munthu, anakantha M-aigupto, namfotsera mumchenga. 13 M’mawa mwake anatulukanso, ndipo, tawonani, anthu aŵiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako? 14 Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha M-aigupto? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziŵika. 15 Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m’dziko la Midyani; nakhala pansi pachitsime. 16 Ndipo wansembe wa Midyani anali nawo ana aakazi asanu ndi aŵiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wawo. 17 Pamenepo anadza abusa nawapitikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lawo. 18 Mmene anafika kwa Rehueli atate wawo, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero? 19 Ndipo anati iwo, Munthu M-aigupto anatilanditsa m’manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi. 20 Ndipo anati kwa ana ake aakazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya. 21 Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora. 22 Ndipo anawona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Gerisomu; pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko la eni. 23 Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aigupto; ndi ana a Israyeli anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wawo, nalira, ndi kulira kwawo kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. 24 Ndipo Mulungu anamva kubuula kwawo, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo. 25 Ndipo Mulungu anapenya Aisrayeli, ndi Mulungu anadziŵa.
3 Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midyani; natsogolera gululo mtsogolo mwa chipululu, nafika ku phiri la Mulungu, ku Horebe. 2 Ndipo mthenga wa Mulungu anamuonekera m’chilangali chamoto chotuluka mkati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo tawonani, chitsamba chirikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho. 3 Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikawone chowoneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. 4 Pamene Yehova anawona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali mkati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndiri pano. 5 Ndipo iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika. 6 Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anawopa kuyang’ana Mulungu. 7 Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m’Aigupto, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziŵa zowawitsa zawo; 8 ndipo ndatsikira kuwalanditsa m’manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. 9 Ndipo tsopano, tawona kulira kwa ana a Israyeli kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aaigupto awapsinja nako. 10 Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israyeli m’Aigupto. 11 Koma Mose anati kwa Mulungu, Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israyeli m’Aigupto? 12 Ndipo iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo m’Aigupto, mudzatumikira Mulungu paphiri pano. 13 Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? ndikanena nawo chiyani? 14 Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu. 15 Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo. 16 Muka, nukasonkhanitse akulu a Israyeli, nunene nawo, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandiwonekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuwona chomwe akuchitirani m’Aigupto; 17 ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m’mazunzo a Aigupto, kukuloŵetsani m’dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. 18 Ndipo adzamvera mawu ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israyeli, kwa mfumu ya Aigupto, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu. 19 Koma ine ndidziŵa kuti mfumu ya Aigupto siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ayi. 20 Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aigupto ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka. 21 Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Aigupto; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu; 22 koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m’nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolidi, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aaigupto.
4 Ndipo Mose anayankha nati, Koma tawonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mawu anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuwonekera iwe. 2 Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m’dzanja lako? Nati, Ndodo. 3 Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa. 4 Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumchira; ndipo anatambasula dzanja lake, naigwira, nikhalanso ndodo m’dzanja lake; 5 kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. 6 Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, tawonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa. 7 Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifukwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, tawonani, linasandukanso lomwe lakale. 8 Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mawu a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mawu a chizindikiro chotsirizachi. 9 Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mawu ako, ukatunge madzi a kunyanja, ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda. 10 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosoŵa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilakhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa mkamwa molemera, ndi wa lilime lolemera. 11 Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu mkamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Sindine Yehova kodi? 12 Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala mkamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule. 13 Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma. 14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziŵa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, tawona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m’mtima mwake. 15 Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mawu; ndipo Ine ndidzakhala mkamwa mwako, ndi mkamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite. 16 Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati mkamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu. 17 Ndipo ukaigwire m’dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo. 18 Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kumka kwa abale anga amene ali m’Aigupto, ndikawone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino. 19 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’Midyani, Muka, bwerera kumka ku Aigupto; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako. 20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pa bulu, nabwerera kumka ku dziko la Aigupto; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m’dzanja lake. 21 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kumka ku Aigupto, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m’dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita. 22 Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova, Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israyeli. 23 Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; tawona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba. 24 Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha. 25 Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka. 26 Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe. 27 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona. 28 Ndipo Mose anauza Aroni mawu onse a Yehova amene adamtuma nawo, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira. 29 Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israyeli; 30 ndipo Aroni anawafotokozera mawu onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu. 31 Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israyeli, ndi kuti adawona mazunzo awo, anawerama, nalambira Mulungu.
5 Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analoŵa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m’chipululu. 2 Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziŵa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite. 3 Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m’chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikumike ndi mliri, kapena ndi lupanga. 4 Ndipo mfumu ya Aigupto inanena nawo, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zawo? Mukani ku akatundu anu. 5 Farao anatinso, Tawonani, anthu a m’dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu awo. 6 Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitawo awo, ndi kuti, 7 Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nawo njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu. 8 Ndipo muziwaŵerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. 9 Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mawu amabodza. 10 Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitawo awo anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu. 11 Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu. 12 Pamenepo anthuwo anabalalika m’dziko lonse la Aigupto kufuna chiputu ngati udzu. 13 Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu. 14 Ndipo anapanda akapitawo a ana a Israyeli, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale? 15 Pamenepo akapitawo a ana a Israyeli anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu? 16 Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, tawonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu. 17 Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova. 18 Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiŵerengero chake cha njerwa. 19 Ndipo akapitawo a ana a Israyeli anawona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake. 20 Ndipo potuluka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nawo; 21 ndipo ananena nawo, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m’dzanja lawo kutipha nalo. 22 Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? mwandituma bwanji? 23 Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m’dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse.
6 Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzawona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m’dziko lake. 2 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA: 3 ndipo ndinawonekera Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziŵika kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA. 4 Ndipo ndinakhazikitsanso nawo chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo awo, anali alendo m’mwemo. 5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa. 6 Chifukwa chake nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu; 7 ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto. 8 Ndipo ndidzakuloŵetsani m’dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova. 9 Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israyeli; koma sanamvera Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera. 10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 11 Loŵa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto, kuti alole ana a Israyeli atuluke m’dziko lake. 12 Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula? 13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti atulutse ana a Israyeli m’dziko la Aigupto. 14 Akulu a mbumba za makolo awo ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni. 15 Ndi ana aamuna a Simeoni ndiwo: Yemweli, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli mwana wa mkazi wa m’Kanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni. 16 Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwawo ndiwo: Gerisoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziŵiri. 17 Ana aamuna a Gerisoni ndiwo: Libni ndi Simei, mwa mabanja awo. 18 Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amramu ndi Izara, ndi Hebroni, ndi Uziyeli; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu kudza zitatu. 19 Ndipo ana aamuna a Merai ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwawo. 20 Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziŵiri. 21 Ndi ana aamuna a Izara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri. 22 Ndi ana aamuna a Uziyeli ndiwo: Misayeli, ndi Elisafana, ndi Sitiri. 23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara. 24 Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora. 25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putieli akhale mkazi wake, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja awo. 26 Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nawo, Tulutsani ana a Israyeli m’dziko la Aigupto mwa makamu awo. 27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aigupto, awatulutse ana a Israyeli m’Aigupto; Mose ndi Aroni ameneŵa. 28 Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m’dziko la Aigupto, 29 Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto zonsezi Ine ndizinena nawe. 30 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndiri wa milomo yosadula, ndipo Farao adzandimvera bwanji?
7 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Tawona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako. 2 Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israyeli atuluke m’dziko lake. 3 Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m’dziko la Aigupto. 4 Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aigupto, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israyeli, m’dziko la Aigupto ndi maweruzo aakulu. 5 Ndipo Aaigupto adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aigupto, ndi kutulutsa ana a Israyeli pakati pawo. 6 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita. 7 Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao. 8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti, 9 Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka. 10 Ndipo Mose ndi Aroni analoŵa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka. 11 Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anachita momwemo ndi matsenga awo. 12 Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo. 13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova. 14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. 15 Muka kwa Farao m’mawa; tawona, atuluka kumka kumadzi; uime kumlinda m’mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m’dzanja lako. 16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m’chipululu; koma, tawona, sunamvera ndi pano. 17 Atero Yehova, Ndi ichi udzadziŵa kuti Ine ndine Yehova: tawonani, ndidzapanda madzi ali m’nyanja ndi ndodo iri m’dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. 18 Ndi nsomba ziri m’nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aaigupto adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m’nyanjamo. 19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m’Aigupto, pa nyanja yawo, pa ngalande zawo, ndi pa matamanda awo, ndi pa matawale awo onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m’dziko lonse la Aigupto, m’zotengera zamtengo, ndi zamwala. 20 Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m’nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m’nyanjamo anasanduka mwazi. 21 Ndi nsomba za m’nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m’nyanjamo; ndipo munali mwazi m’dziko lonse la Aigupto. 22 Ndipo alembi a Aigupto anachita momwemo ndi matsenga awo; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova. 23 Ndipo Farao anatembenuka, naloŵa m’nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake. 24 Koma Aaigupto onse anakumba m’mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoza kumwa madzi m’nyanjamo. 25 Ndipo anafikira masiku asanu ndi aŵiri atapanda nyanja Yehova.
8 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Loŵa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. 2 Ndipo ukakana kuwalola amuke, tawona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule; 3 ndipo m’nyanjamo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzaloŵa m’nyumba mwako, ndi m’chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m’nyumba za anyamata ako, ndi pa anthu ako, m’michembo yanu yootcheramo, ndi m’mbale zanu zoumbiramo. 4 Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse. 5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule pa dziko la Aigupto. 6 Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pa madzi a m’Aigupto; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Aigupto. 7 Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga awo, nakweretsa achule pa dziko la Aigupto. 8 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe. 9 Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ayi; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti awonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m’nyanja mokha? 10 Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mawu anu, kuti mudziŵe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu. 11 Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m’nyanja mokha. 12 Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao. 13 Ndipo Yehova anachita monga mwa mawu a Mose; nafa achulewo kuchokera m’zinyumba, ndi m’mabwalo, ndi m’minda. 14 Ndipo anawaola miulu miulu; ndi dziko linanunkha. 15 Koma pamene Farao anawona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. 16 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m’dziko lonse la Aigupto. 17 Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoŵeta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m’dziko lonse la Aigupto. 18 Alembi anateronso ndi matsenga awo kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoŵeta. 19 Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. 20 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; tawona, atuluka kumka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire. 21 Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, tawona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aaigupto zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo. 22 Ndipo tsiku ili ndidzalemba malire dziko la Goseni, mmene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziŵe kuti ine ndine Yehova pakati pa dzikoli. 23 Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi. 24 Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m’nyumba ya Farao, ndi m’nyumba za anyamata ake, ndi m’dziko lonse la Aigupto; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo. 25 Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m’dzikomu. 26 Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aaigupto; tawonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aaigupto pamaso pawo sadzatiponya miyala kodi? 27 Timuke ulendo wa masiku atatu m’chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe. 28 Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m’chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere. 29 Ndipo Mose anati, Onani, ndirikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova. 30 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. 31 Ndipo Yehova anachita monga mwa mawu a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse. 32 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthaŵi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.
9 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Loŵa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. 2 Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, 3 tawona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoŵeta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamila, pa ng’ombe, ndi pa zoŵeta zazing’ono ndi kalira woopsa. 4 Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoŵeta za Israyeli ndi zoŵeta za Aigupto; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israyeli. 5 Ndipo Yehova anaika nthaŵi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu [ichi] m’dzikomu. 6 Ndipo m’mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoŵeta zonse za m’Aigupto; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoŵeta za ana a Israyeli. 7 Ndipo Farao anatuma, tawonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoŵeta za Aisrayeli. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalola anthu amuke. 8 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng’anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao. 9 Ndipo lidzakhala fumbi losalala pa dziko lonse la Aigupto, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoŵeta ngati zironda zobuka ndi matuza, m’dziko lonse la Aigupto. 10 Ndipo anatenga phulusa la m’ng’anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zironda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoŵeta. 11 Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zirondazo; popeza panali zironda pa alembi ndi pa Aaigupto onse. 12 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvera iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose. 13 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire. 14 Pakuti nthaŵi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziŵe kuti palibe wina wonga ine pa dziko lonse lapansi. 15 Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uwonongeke pa dziko lapansi. 16 Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi. 17 Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke? 18 Tawona, mawa monga nthaŵi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m’Aigupto kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino. 19 Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoŵeta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoŵeta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m’nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa. 20 Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mawu a Yehova anathawitsira m’zinyumba anyamata ake ndi zoŵeta zake; 21 koma iyeyu wosasamalira mawu a Yehova anasiya anyamata ndi zoŵeta zake kubusa. 22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Aigupto, pa anthu ndi pa zoŵeta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m’dziko la Aigupto. 23 Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Aigupto. 24 Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m’dziko lonse la Aigupto chiyambire mtundu wawo. 25 Ndipo matalala anapanda m’dziko lonse la Aigupto zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoŵeta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo. 26 M’dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israyeli, munalibe matalala. 27 Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nawo, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa. 28 Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso. 29 Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m’mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziŵe kuti dziko lapansi nla Yehova. 30 Koma inu ndi anyamata anu ndidziŵa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu. 31 Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa. 32 Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amadzala m’mbuyo. 33 Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m’mudzi nasasatulira manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko. 34 Pamene Farao anawona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anawonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake. 35 Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose.
10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Loŵa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pawo; 2 ndi kuti ufotokozere m’makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m’Aigupto, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pawo; kuti mudziŵe kuti ine ndine Yehova. 3 Ndipo Mose ndi Aroni analoŵa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire; 4 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, tawona, mawa ndidzafikitsa dzombe m’dziko lako; 5 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo; 6 ndipo lidzadzaza m’nyumba zako, ndi m’nyumba za anyamata ako onse, ndi m’nyumba za Aaigupto onse; sanachiona chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lerolino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao. 7 Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simunayambe kudziŵa kuti Aigupto lawonongeka? 8 Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nawo, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo ani? 9 Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng’ombe zathu; pakuti tiri nawo madyerero a Yehova. 10 Ndipo ananena nawo, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana aang’ono anu mumuke; chenjerani, pakuti pali choipa pamaso panu. 11 Chotero ayi, mukani tsopano, inu amuna aakulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapitikitsa pamaso pa Farao. 12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Aigupto, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Aigupto, lidye zitsamba zonse za m’dziko, ndizo zonse adazisiya matalala. 13 Pamenepo Mose analoza ndodo yake pa dziko la Aigupto; ndipo Yehova anawombetsa padziko mphepo ya kum’mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum’mawa inadza nalo dzombe. 14 Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Aigupto, ndipo linatera pakati pa malire onse a Aigupto, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere. 15 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m’dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala chabiriwiri chirichonse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m’dziko lonse la Aigupto. 16 Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu. 17 Ndipo tsopano, ndikhululukirenitu kulakwa kwanga nthaŵi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha. 18 Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. 19 Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m’Nyanja Yofiira; silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Aigupto. 20 Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke. 21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Aigupto, ndiwo mdima wokhudzika. 22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m’dziko lonse la Aigupto masiku atatu; 23 sanawonana, sanaukanso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israyeli kudayera m’nyumba zawo. 24 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng’ombe zanu zokha zitsale; mumuke nawo ana anu aang’ononso. 25 Koma Mose anati, Mutipatsenso m’dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu. 26 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziŵa umo tidzamtumikira Yehova. 27 Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke. 28 Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usawonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa. 29 Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzawonanso nkhope yanu.
11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Aigupto; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse. 2 Lankhula tsopano m’makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolidi. 3 Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aaigupto. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m’dziko la Aigupto, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu. 4 Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka ine kumka pakati pa Aigupto; 5 ndipo ana onse oyamba a m’dziko la Aigupto adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoŵeta. 6 Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m’dziko lonse la Aigupto, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere. 7 Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israyeli ngakhale anthu kapena zoŵeta; kuti mudziŵe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aaigupto ndi Aisrayeli. 8 Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima. 9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m’dziko la Aigupto. 10 Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli atuluke m’dziko lake.
12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m’dziko la Aigupto, ndi kuti, 2 Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka. 3 Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate awo, mwana wa nkhosa pabanja. 4 Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu awo; muziŵerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwawo. 5 Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi. 6 Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinayi la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo. 7 Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m’nyumba zimene adyeramo. 8 Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yootcha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa. 9 Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ayi, koma yootcha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake. 10 Ndipo musasiyako kufikira m’mawa; koma yotsalira kufikira m’mawayo muipsereze ndi moto. 11 Ndipo muziidya chotero: okwinda m’chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m’dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paskha wa Yehova. 12 Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Aigupto usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m’dziko la Aigupto, anthu ndi zoŵeta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aigupto; Ine ndine Yehova. 13 Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha ine dziko la Aigupto. 14 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la madyerero a Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la madyerero, likhale lemba losatha. 15 Masiku asanu ndi aŵiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m’nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiŵiri, munthu amene adzasadzidwa kwa Israyeli. 16 Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiŵiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita. 17 Ndipo muzisunga madyerero a mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m’dziko la Aigupto; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m’mibadwo yanu, lemba losatha. 18 Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinayi madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi aŵiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake. 19 Chisapezeke chotupitsa m’nyumba zanu masiku asanu ndi aŵiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israyeli, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m’dziko. 20 Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa. 21 Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israyeli, nanena nawo, Pitani, dzitengereni ana a nkhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paskha. 22 Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m’mwazi uli m’mbale, ndi kupaka mwazi uli m’mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m’mawa. 23 Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aaigupto; koma pamene adzawona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola wowononga alowe m’nyumba zanu kukukanthani. 24 Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthaŵi zonse. 25 Ndipo kudzakhala, pamene muloŵa m’dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku. 26 Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? 27 mudzati, Ndiko nsembe ya Paskha wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israyeli m’Aigupto, pamene anakantha Aaigupto, napulumutsa nyumba zathu. 28 Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israyeli anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo. 29 Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m’dziko la Aigupto, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam’nsinga ali m’kaidi; ndi ana oyamba onse a zoŵeta. 30 Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse, ndi Aaigupto onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m’Aigupto; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m’mwemo. 31 Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena. 32 Muka nazoni zoŵeta zanu zazing’ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso. 33 Ndipo Aaigupto anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m’dziko; pakuti anati, Tiri akufa tonse. 34 Ndipo anthu anatenga mtanda wawo usanatupe, ndi zoumbiramo zawo zomangidwa m’zovala zawo pa mapewa awo. 35 Ndipo ana a Israyeli anachita monga mwa mawu a Mose; napempha Aaigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zovala. 36 Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aaigupto, ndipo sanawakaniza. Ndipo anawafunkhira Aaigupto. 37 Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wakuchokera ku Ramese kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osaŵerenga ana. 38 Ndipo anthu ambiri [osakanizika] anakwera nawo; ndi nkhosa ndi ng’ombe, zoŵeta zambirimbiri. 39 Ndipo anawotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nawo ku Aigupto, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba. 40 Ndipo kukhala kwa ana a Israyeli anakhala m’Aigupto ndiko zaka mazana anayi kudza makumi atatu. 41 Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anayi kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko a Aigupto. 42 Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m’dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku midabwo yawo. 43 Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Psakha ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko; 44 koma kapolo wa mwini aliyense, wogula ndi ndalama, utamdula, ndipo adyeko. 45 Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko. 46 Audye m’nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake. 47 Msonkhano wonse wa Israyeli uzichita ichi. 48 Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m’dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko. 49 Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m’dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu. 50 Ndipo ana onse a Israyeli anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita. 51 Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israyeli m’dziko la Aigupto, monga mwa makamu awo.
13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, 2 Ndipatulire ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israyeli, mwa anthu ndi mwa zoŵeta; ndiwo anga. 3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka m’Aigupto, m’nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa. 4 Mutuluka lero lino mwezi wa Abibu. 5 Ndipo kudzakhala atakuloŵetsa Yehova m’dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno. 6 Masiku asanu ndi aŵiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiŵiri likhale la madyerero a Yehova. 7 Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi aŵiriwo ndipo kasawoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisawoneke kwanu m’malire ako onse. 8 Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine m’Aigupto. 9 Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chikumbutso pakati pa maso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale mkamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa m’Aigupto ndi dzanja lamphamvu. 10 Chifukwa chake uzikasunga lemba ili pa nyengo yake chaka ndi chaka. 11 Ndipo kudzakhala, atakuloŵetsa Yehova m’dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo, 12 kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nawo odzera kwa zoŵeta; amunawo ndi a Yehova. 13 Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola. 14 Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? ukanene naye, Yehova anatitulutsa m’Aigupto, m’nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu; 15 ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m’dziko la Aigupto, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoŵeta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola. 16 Ndipo chizikhala ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chapamphumi pakati pa maso ako; pakuti Yehova anatitulutsa m’Aigupto ndi dzanja lamphamvu. 17 Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilitsi, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m’mbuyo kumka ku Aigupto. 18 Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, kuti njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israyeli anakwera kuchokera m’dziko la Aigupto okonzeka. 19 Ndipo Mose anamuka nawo mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israyeli ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nawo mafupa anga osawasiya kuno. 20 Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu. 21 Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m’njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; 22 sanachotsa mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.
14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 2 Lankhula ndi anthu a Israyeli, kuti abwerere m’mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja yamchere, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja. 3 Ndipo Farao adzanena za ana a Israyeli, Amizidwa dziko, chipilulu chawatsekera. 4 Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aaigupto adzadziŵa kuti ine ndine Yehova, Ndipo anachita chomwecho. 5 Ndipo anauza mfumu ya Aigupto kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israyeli amuke osatigwiriranso ntchito? 6 Ndipo anamanga gareta lake, napita nawo anthu ake; 7 napita nawo magareta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magareta onse a m’Aigupto, ndi akapitawo awo onse. 8 Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aigupto, ndipo iye analondola ana a Israyeli; koma ana a Israyeli adatuluka ndi dzanja lokwezeka. 9 Ndipo Aaigupto anawalondola, ndiwo akavalo ndi magareta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni. 10 Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso awo, tawonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pawo; ndipo anawopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anafuulira kwa Yehova. 11 Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m’chipululu chifukwa panalibe manda m’Aigupto? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa m’Aigupto? 12 Si awa mawuwo tinalankhula nanu m’Aigupto ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m’chipululu ayi. 13 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musawope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse. 14 Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete. 15 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa ine? lankhula ndi ana a Israyeli kuti aziyenda. 16 Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israyeli alowe pakati pa nyanja pouma. 17 Ndipo ine, tawonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aaigupto, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magareta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. 18 Ndipo Aaigupto adzadziŵa kuti ine ndine Yehova, polemekezedwa ine pa Farao, pa magareta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. 19 Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israyeli, unachokako, nutsata pambuyo pawo; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pawo, nuima pambuyo pawo; 20 nuloŵa pakati pa ulendo wa Aaigupto ndi ulendo wa Aisrayeli; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzake usiku wonse. 21 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana. 22 Ndipo ana a Israyeli analoŵa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere. 23 Ndipo Aaigupto anawalondola, naloŵa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magareta ake, ndi apakavalo ake. 24 Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m’moto ndi m’mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aaigupto. 25 Ndipo anagulula njinga za magareta awo, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aaigupto anati, Tithawe pamaso pa Israyeli; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aaigupto. 26 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aaigupto, magareta awo, ndi apakavalo awo. 27 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m’mayendedwe ake mbanda kucha; ndipo Aaigupto pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aaigupto mkati mwa nyanja. 28 Popeza madziwo anabwerera, namiza magareta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idaloŵa pambuyo pawo m’nyanja; sanatsala wa iwowa ndi mmodzi yense. 29 Koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi palamanzere. 30 Chomwecho Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lomwelo m’manja a Aaigupto; ndipo Israyeli anawona Aaigupto akufa m’mphepete mwa nyanja. 31 Ndipo Israyeli anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aaigupto, ndipo anthuwo anawopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.
15 Pamenepo Mose ndi ana a Israyeli anayimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzayimbira Yehova pakuti wapambanatu; Kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. 2 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Ndipo wakhala chipulumutso changa; Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; Ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa. 3 Yehova ndiye wankhondo; Dzina lake ndiye Yehova. 4 Magareta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m’nyanja; Ndi akazembe ake osankhika anamira m’Nyanja Yofiira. 5 Nyanja inawamiza; Anamira mozama ngati mwala. 6 Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani. 7 Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira inu; Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu. 8 Ndipo ndi mpumo wa m’mphuno mwanu madzi anaunjikika, Mayendedwe ake anakhala chiriri ngati mulu; Zozama zinalimba mkati mwa nyanja. 9 Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha; Ndidzakhuta nawo mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawawononga. 10 Munawombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza; Anamira m’madzi aakulu ngati mtovu. 11 Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa, woyera, Wowopsa pomyamika, wakuchita zozizwa? 12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja, Nthaka inawameza. 13 Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; Mwa mphamvu yanu mudawalondolera njira yakumka pokhala panu poyera. 14 Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; Kuda mtima kwagwira anthu okhala m’Filistiya. 15 Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; Agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Moabu; Okhala m’Kanani onse asungunuka mtima. 16 Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; Pa dzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; Kufikira apita anthu anu, Yehova, Kufikira apita anthu amene mudawaombola. 17 Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la choloŵa chanu, Pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, Malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. 18 Yehova adzachita ufumu nthaŵi yomka muyaya. 19 Pakuti akavalo a Farao analoŵa m’nyanja, ndi magareta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m’nyanja; koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja. 20 Ndipo Miriamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m’dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang’ombe. 21 Ndipo Miriamu anawayankha, Yimbirani Yehova, pakuti wapambanatu; Kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. 22 Ndipo Mose anatsogolera Israyeli kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako naloŵa m’chipululu cha Suri; nayenda m’chipululu masiku atatu, osapeza madzi. 23 Pamene anafika ku Mara, sanakhoza kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; chfukwa chake anatcha dzina lake Mara. 24 Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani? 25 Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m’madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa; 26 ndipo anati, Ngati udzamveratu mawu a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zowona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aaigupto sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe. 27 Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi aŵiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi aŵiri; ndipo anamanga chigono chawo pomwepo pa madziwo.
16 Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israyeli linaloŵa m’chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiŵiri atatuluka m’dziko la Aigupto. 2 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni m’chipululu; 3 nanena nawo ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m’dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m’chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala. 4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tawona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m’chilamulo changa kapena iyayi. 5 Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nawo, atawonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi. 6 Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziŵa kuti Yehova anakutulutsani m’dziko la Aigupto; 7 ndi m’mawa mwake mudzawona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife? 8 Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m’mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nawo. Koma ife ndife chiyani? simulikudandaulira ife koma Yehova. 9 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu. 10 Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, tawonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo. 11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 12 Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nawo ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m’mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziŵa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu. 13 Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m’mawa padagwa mame pozungulira tsasa. 14 Ndipo atasansuka mame adagwawo, tawonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang’ono kamphumphu, kakang’ono ngati chipale panthaka. 15 Ndipo pamene ana a Israyeli anakawona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? pakuti sanadziŵa ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nawo, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu. 16 Amenewo ndiwo mawu walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m’hema mwake. 17 Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang’ono. 18 Ndipo pamene anayesa omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang’ono sunamsoŵa; yense anaola monga mwa njala yake. 19 Ndipo Mose ananena nawo, Palibe munthu asiyeko kufikira m’mawa. 20 Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m’mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nawo. 21 Ndipo anauola m’mawa ndi m’mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuŵa umasungunuka. 22 Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, nawonjezapo linzake, maomeri aŵiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose. 23 Ndipo ananena nawo, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziotcha, otchani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m’mawa. 24 Ndipo anausunga kufikira m’mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi. 25 Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo. 26 Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe. 27 Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeza. 28 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti? 29 Tawonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku aŵiri; khalani yense m’malo mwake, munthu asatuluke m’malo mwake tsiku lachisanu ndi chiŵiri. 30 Ndipo anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiŵiri. 31 Ndipo mbumba ya Israyeli inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosanganiza ndi uchi. 32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mawu anauza Yehova, Dzazani omeri nawo, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nawo m’chipululu, muja ndinakutulutsani m’dziko la Aigupto. 33 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu. 34 Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko. 35 Ndipo ana a Israyeli anadya mana zaka makumi anayi, kufikira ataloŵa dziko la midzi; anadya mana kufikira analoŵa malire a dziko la Kanani. 36 Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa.
17 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linachoka m’chipululu cha Sini, m’zigono zawo, monga mwa mawu a Yehova, nagona m’Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu. 2 Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nawo, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova? 3 Ndipo pomwepo anathu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoŵeta zathu ndi ludzu? 4 Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? andilekera pang’ono kundiponya miyala. 5 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israyeli; nutenge m’dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke. 6 Tawona, ndidzima pamaso pako pathanthwe m’Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israyeli. 7 Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israyeli; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iyayi? 8 Pamenepo anadza Amaleki, nayambana ndi Israyeli m’Refidimu. 9 Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleki; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m’dzanja langa. 10 Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleki; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri, anakwera pamwamba pa chitunda. 11 Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israyeli analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleki analakika. 12 Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litaloŵa dzuŵa. 13 Ndipo Yoswa anathyola Amaleki ndi anthu ake ndi kuukali kwa lupanga. 14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m’buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleki pansi pa thambo. 15 Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi: 16 nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleki m’mibadwo mibadwo.
18 Ndipo Yetero, wansembe wa Midyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israyeli anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israyeli m’Aigupto. 2 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwawo), ndi ana ake aŵiri; 3 dzina la winayo ndiye Gerisomu, pakuti anati, Ndakhala mlendo m’dziko lachilendo; 4 ndi dzina la mnzake ndiye Eliezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao. 5 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake aamuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu; 6 nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ake omwe aŵiri. 7 Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, naloŵa m’hema. 8 Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aaigupto chifukwa cha Israyeli; ndi mavuto onse anakomana nawo panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa. 9 Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israyeli, ndi kuwalanditsa m’dzanja la Aaigupto. 10 Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m’dzanja la Aaigupto, ndi m’dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aaigupto. 11 Tsopano ndidziŵa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse; pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa. 12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israyeli anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu. 13 Ndipo kunatero kuti m’mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yawo; ndipo anthu anakhala chiriri pamaso pa Mose kuyambira m’mawa kufikira madzulo. 14 Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anawona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chiriri pamaso pako kuyambira m’mawa kufikira madzulo? 15 Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu; 16 akakhala nawo mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziŵitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake. 17 Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Chinthu uchitachi sichiri chabwino ayi. 18 Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nawo; pakuti chikulaka chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha. 19 Tamvera mawu anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m’malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu; 20 nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziŵitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita. 21 Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna owona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi; 22 ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthaŵi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing’ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe. 23 Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwawo mumtendere. 24 Ndipo Mose anamvera mawu a mpongozi wake, nachita zonse adazinena. 25 Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisrayeli onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi. 26 Ndipo anaweruza anthu nthaŵi zonse; mlandu wakuwalaka amabwera nawo kwa Mose, ndi milandu yaing’ono yonse amaweruza okha. 27 Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kumka ku dziko lake.
19 Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israyeli m’dziko la Aigupto, tsiku lomwelo, analoŵa m’chipululu cha Sinai. 2 Pakuti anachoka ku Refidimu, naloŵa m’chipululu cha Sinai, namanga tsasa m’chipululumo; ndipo Israyeli anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo. 3 Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m’phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israyeli, kuti, 4 Inu munawona chimene ndinachitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa ine ndekha. 5 Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; 6 ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mawu amene ukalankhule ndi ana a Israyeli. 7 Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pawo mawu awa onse amene Yehova adamuuza. 8 Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nawo mawu a anthu kwa Yehova. 9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tawona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthaŵi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mawu a anthuwo. 10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zawo, 11 nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse. 12 Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m’phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu; 13 dzanja lirilonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liwu lake azikwera m’phirimo. 14 Ndipo Mose anatsika m’phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zawo. 15 Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi. 16 Ndipo kunali tsiku lachitatu, m’mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liwu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. 17 Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde pa phiri. 18 Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m’moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m’ng’anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19 Ndipo pamene liwu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mawu. 20 Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pake pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo. 21 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzawona, ndipo angagwe ambiri a iwowa. 22 Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova. 23 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m’phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m’phirimo, ndi kulipatula. 24 Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule. 25 Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nawo.
20 Ndipo Mulungu ananena mawu onse ameneŵa, nati: 2 INE ndine YEHOVA Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Aigupto, ku nyumba ya akapolo. 3 Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. 4 Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; 5 usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene akudana ndi ine; 6 ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi ine, nasunga malamulo anga. 7 Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo. 8 Uzikumbukira tsiku a Sabata, likhale lopatulika. 9 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse; 10 koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndilo Sabata la kwa Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iriyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m’mudzi mwako; 11 chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m’menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiŵiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. 12 Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. 13 Usaphe. 14 Usachite chigololo. 15 Usabe. 16 Usamnamizire mnzako. 17 Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako. 18 Ndipo anthu onse anawona mabingu ndi zimphezi, ndi liwu la lipenga, ndi phiri lirikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe. 20 Ndipo Mose anati kwa anthu, Musawope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe. 21 Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu. 22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israyeli, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba. 23 Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi ine; musadzipangire milungu yagolidi. 24 Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng’ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa. 25 Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo chosemera chako, waliipsa. 26 Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angawoneke maliseche ako pamenepo.
21 Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pawo. 2 Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiŵiri azituluka waufulu chabe. 3 Akaloŵa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye. 4 Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha. 5 Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; 6 pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake amboole khutu lake ndi lisungulu; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse. 7 Ndipo munthu akagulitsa mwana wake wamkazi akhale mdzakazi, iyeyu asatuluke monga amatuluka anyamata. 8 Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza anachita naye monyenga. 9 Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana aakazi. 10 Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zake zake. 11 Ndipo akapanda kumchitira izi zitatu, azituluka chabe, osaperekapo ndalama. 12 Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu. 13 Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikira pothawirapo iye. 14 Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe. 15 Munthu wakukantha atate wake, kapena amayi wake, aphedwe ndithu. 16 Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m’dzanja lake, aphedwe ndithu. 17 Munthu wakutemberera atate wake, kapena amayi wake, aphedwe ndithu. 18 Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonyo, wosafa iye, koma wakhulungira pakama; 19 akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkhanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse. 20 Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo aliridwe ndithu. 21 Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena aŵiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wake. 22 Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza. 23 Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo, 24 diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, 25 kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo. 26 Munthu akampanda mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu chifukwa cha diso lake. 27 Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake. 28 Ng’ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng’ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng’ombeyo azimasuka. 29 Koma ngati ng’ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng’ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso. 30 Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira. 31 Ingakhale yatunga mwana wamwamuna kapena wamkazi, aichitire monga mwa chiweruzo ichi. 32 Ng’ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekele a siliva makumi atatu, ndipo ng’ombeyo aiponye miyala. 33 Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalivundikira, ndipo ikagwamo ng’ombe kapena bulu, 34 mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yake. 35 Ng’ombe ya mwini ikapweteka ng’ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng’ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo. 36 Kapena kudadziŵika kuti ng’ombeyo ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng’ombe kulipa ng’ombe, koma yakufayo ndi yake.
22 Munthu akaba ng’ombe, kapena nkhosa, nakaipha, kapena kuigulitsa, azilipa ng’ombe zisanu pa ng’ombeyo, ndi nkhosa zinayi pa nkhosayo. 2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi. 3 Litamtulukira dzuŵa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake. 4 Akachipeza chakubacho chiri m’dzanja lake chamoyo, ngakhale ng’ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza. 5 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa. 6 Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu. 7 Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m’nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza. 8 Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake. 9 Mlandu uli wonse wa cholakwa, kunena za ng’ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse aŵiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake. 10 Munthu akaikiza bulu, kapena ng’ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipitikitsa osachiona munthu; 11 lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo aŵiri, kuti sanatulutsa dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe. 12 Koma ngati chidabedwa kwawoko ndithu, alipe kwa mwiniyo. 13 Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho. 14 Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. 15 Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake. 16 Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. 17 Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha namwali. 18 Wanyanga usamlola akhale ndi moyo. 19 Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. 20 Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, awonongeke konse. 21 Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m’dziko la Aigupto. 22 Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. 23 Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo; 24 ndi mkwiyo wanga udzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe. 25 Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamŵerengera phindu. 26 Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma poloŵa dzuŵa uchibwezere kwa iye; 27 popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira ine, ndidzamva; pakuti ine ndine wachisomo. 28 Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako. 29 Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse ine. 30 Uzitero nazo ng’ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amayi wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa ine. 31 Ndipo muzindikhalira ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.
23 Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa. 2 Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; 3 kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake. 4 Ukakomana ndi ng’ombe kapena bulu wa mdani wako zirimkusokera, uzimbwezera izo ndithu. 5 Ukawona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu. 6 Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi. 7 Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama, pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa. 8 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. 9 Usampsinja mlendo; pakuti mudziŵa mtima wa mlendo popeza munali alendo m’dziko la Aigupto. 10 Ndipo uzibzala m’munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; 11 koma chaka chachisanu ndi chiŵiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira iwowa zoŵeta za kubusa zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako waazitona. 12 Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri uzipumula; kuti ng’ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke. 13 Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako. 14 Muzindichitira ine madyerero katatu m’chaka. 15 Uzisunga madyerero a mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi aŵiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m’menemo unatuluka m’Aigupto; koma asawoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; 16 ndi madyerero a masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m’munda; ndi madyerero a kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m’munda. 17 Katatu m’chaka aamuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. 18 Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m’mawa. 19 Uzibwera nazo zoyambayamba za m’munda mwako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwana wa mbuzi mu mkaka wa make. 20 Tawona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamalo pomwe ndakonzeratu. 21 Musamalire iye, ndi kumvera mawu ake; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa liri m’mtima mwake. 22 Pakuti ukamveratu mawu ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe. 23 Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawawononga. 24 Usagwadira milungu yawo, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zawo; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zawo. 25 Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe. 26 M’dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuŵerenga kwa masiku ako. 27 Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapitikitsa anthu onse amene udzafika kwawo, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m’mbuyo mwawo. 28 Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. 29 Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zirombo za kuthengo zingakuchulukire. 30 Ndidzawaingitsa pang’ono pang’ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko choloŵa chako. 31 Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisiti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m’dzikolo m’dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako. 32 Usapangana nawo, kapena ndi milungu yawo. 33 Asakhale m’dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa ine; pakuti ukatumikira milungu yawo, kudzakukhalira msampha ndithu.
24 Ndipo iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israyeli makumi asanu ndi aŵiri; ndipo mugwadire pakudza kutali; 2 ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye. 3 Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mawu onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mawu onse walankhula Yehova tidzachita. 4 Ndipo Mose analembera mawu onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziŵiri, kwa mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli. 5 Ndipo anatuma ana a Israyeli a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, zang’ombe. 6 Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m’zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe. 7 Ndipo anatenga buku la Chipangano, naŵerenga m’makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera. 8 Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Tawonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mawu awa onse. 9 Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israyeli makumi asanu ndi aŵiri anakwerako; 10 ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe. 11 Koma sanatulutsa dzanja lake pa akulu a ena a Israyeli; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa. 12 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa ine m’phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo, ndawalembera kuti uwalangize. 13 Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu. 14 Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo tawonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa. 15 Ndipo Mose anakwera m’phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo. 16 Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiŵiri iye ali mkati mwa mtambo anaitana Mose. 17 Ndipo mawonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba pa phiri, pamaso pa ana a Israyeli. 18 Ndipo Mose analoŵa mkati mwa mtambo, nakwera m’phirimo; ndipo Mose anakhala m’phiri masiku makumi anayi usana ndi usiku.
25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 2 Lankhula ndi ana a Israyeli, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini. 3 Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, 4 ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; 5 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu; 6 mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; 7 miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa. 8 Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pawo. 9 Monga mwa zonse ine ndirikuonetsa iwe, chifaniziro cha kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange. 10 Ndipo azipanga likasa la mtengo wasitimu: utali wake mikono iŵiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu. 11 Ndipo ulikute ndi golidi wowona, ulikute mkati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolidi pozungulira pake. 12 Ndipo uliyengere mphete zinayi zagolidi, ndi kuziika ku miyendo yake inayi; mphete ziŵiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziŵiri pa ina. 13 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi. 14 Nupise mphiko m’mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo. 15 Mphiko zikhale m’zimphete za likasa; asazisolole. 16 Ndipo uziika m’likasamo mboni imene ndidzakupatsa. 17 Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golidi wowona; utali wake mikono iŵiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. 18 Uzipanganso akerubi aŵiri agolidi; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake aŵiri a chotetezerapo. 19 Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo awe aŵiri. 20 Ndipo akerubi afunyululire mapiko awo m’mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko awo, ndi nkhope zawo zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo. 21 Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m’likasamo. 22 Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndiri pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi aŵiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israyeli. 23 Ndipo uzipanga gome la mtengo wasitimu; utali wake mikono iŵiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu. 24 Ndipo ulikute ndi golidi wowona ndi kulipangira mkombero wagolidi pozungulira pake. 25 Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m’kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolidi. 26 Nulipangire mphete zinayi zagolidi, ndi kuika mphetezo pa ngondya zinayi zokhala pa miyendo yake inayi. 27 Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome. 28 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi, kuti anyamulire nazo gome. 29 Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golidi wowona. 30 Ndipo uziika mkate wowonekera pa gomelo pamaso panga nthaŵi zonse. 31 Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golidi wowona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m’mwemo; 32 ndipo m’mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m’mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m’mbali inzake. 33 Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungulume, mutu wa luwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungulume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikapo nyalicho. 34 Ndipo pa choikapo nyali chomwe pakhale zikho zinayi zopangika ngati katungulume, mitu yake ndi maluwa ake; 35 pakhale mutu pansi pa mphanda ziŵiri zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziŵiri zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziŵiri zotuluka m’mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikapo nyalicho. 36 Miyu yawo ndi mphanda zawo zikhale zotuluka m’mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golidi wowona. 37 Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziŵiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake. 38 Ndipo mbano zake, ndi zoolera zake, zikhale za golidi wowona. 39 Achipange ichi ndi zipangizo izi zonse za talente wa golidi wowona. 40 Ndipo uyang’anire uzipanga monga mwachifaniziro chawo, chimene anakuonetsa m’phirimo.
26 Ndipo uzipanga kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri. 2 Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi aŵiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inayi; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi. 3 Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake. 4 Ndipo uziika magango a nsalu yamadzi m’mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m’mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. 5 Uziika magango makumi asanu pa nsalu yotchingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m’mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake. 6 Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolidi, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti kachisi akhale mmodzi. 7 Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kachisi; uziomba nsalu khumi ndi imodzi. 8 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inayi; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo. 9 Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema. 10 Ndipo uziika magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. 11 Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m’magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi. 12 Ndipo chotsalacho pa nsalu za hemalo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, ichinge pambuyo pake pa kachisi. 13 Ndi mkono wa pa mbali ino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira m’utali wake wa nsalu za hemalo, ichinge pambali zake za kachisi, mbali ino ndi mbali ina, kumphimba. 14 Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake. 15 Ndipo uzipangira kachisi matabwa oimirika, a mtengo wasitimu. 16 Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu. 17 Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iŵiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a kachisi. 18 Ndipo uzipanga matabwa a kachisi, matabwa makumi aŵiri ku mbali ya kumwera, kumwera. 19 Nuzipanga makamwa makumi anayi asiliva pansi pa matabwa makumi aŵiri; makamwa aŵiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iŵiri, ndi makamwa aŵiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iŵiri; 20 ndi pa mbali yake ina ya kachisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi aŵiri; ndi makamwa asiliva makumi anayi; 21 makamwa aŵiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa aŵiri pansi pa thabwa lina. 22 Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya kachisi ya kumbuyo kumadzulo. 23 Nupange matabwa aŵiri a ngondya za kachisi za kumbuyo. 24 Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse aŵiri; azikhala a ngondya ziŵiri. 25 Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa awo asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa aŵiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa aŵiri pansi pa thabwa lina. 26 Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wasitimu; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya kachisi, 27 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya kachisi ya kumbuyo kumadzulo. 28 Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo. 29 Ndipo uzikuta matabwa ndi golidi, ndi kupanga mphete zawo zagolidi zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golidi. 30 Ndipo uutse kachisi monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m’phiri. 31 Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri; 32 ndipo uichinge pa mizati inayi ya mitengo yasitimu, zokuta ndi golidi; zokowera zawo zikhale zagolidi, ndi makamwa anayi asiliva. 33 Ndipo uzichinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugaŵirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulikitsa. 34 Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m’malo opatulikitsa. 35 Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya kachisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto. 36 Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula. 37 Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi; zokowera zawo zikhale zagolidi; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
27 Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wasitimu, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale lampwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu. 2 Ndipo uzipanga nyanga zake pa ngondya zake zinayi; nyanga zake zikhale zotuluka m’mwemo: nulikute ndi mkuwa. 3 Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa. 4 Ndipo ulipangire made, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zake zinayi mphete zinayi zamkuwa. 5 Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo pozungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo. 6 Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi mkuwa. 7 Ndipo apise mphiko m’mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziŵiri za guwa la nsembe polinyamula. 8 Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m’phirimo; alipange momwemo. 9 Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu ya bafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana; 10 ndi nsichi zake makumi aŵiri, ndi makamwa awo makumi aŵiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva. 11 Momwemonso pa mbali ya kumpoto m’utali mwake pakhale nsalu zotchingira za mikono zana limodzi m’utali mwake; ndi nsichi zake makumi aŵiri, ndi makamwa awo akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. 12 Ndipo m’kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zotchingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa awo khumi. 13 Ndipo m’kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum’mawa, kum’mawa, mukhale mikono makumi asanu. 14 Ndi nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa awo atatu. 15 Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa awo atatu. 16 Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi aŵiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinayi, ndi makamwa awo anayi. 17 Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zawo zasiliva, ndi makamwa awo amkuwa. 18 Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa. 19 Zipangizo zonse za kachisi, m’machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa. 20 Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. 21 Aroni ndi ana ake aikonze m’chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m’mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yawo, alisunge ana a Israyeli.
28 Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israyeli, kuti andichitire ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni. 2 Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. 3 Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire ine ntchito ya nsembe. 4 Ndipo zovala azisoka ndizi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire ine ntchito ya nsembe. 5 Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 6 Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. 7 Akhale nazo zapamapewa ziŵiri zomangika ku nsonga zake ziŵiri, kuti amangike nazo. 8 Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nawo, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 9 Ndipo utenge miyala iŵiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israyeli; 10 maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzake, mwa kubadwa kwawo. 11 Uloche miyala iŵiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi. 12 Ndipo uiike miyala iŵiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina awo pa mapewa ake aŵiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. 13 Ndipo upange zoikamo za golidi; 14 ndi maunyolo aŵiri a golidi wowona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo. 15 Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 16 Chikhale champwamphwa, chopindika, utali wake chikhato chimodzi, ndi kupingasa kwake chikhato chimodzi. 17 Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inayi ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; 18 ndi mzere wachiŵiri wa nofeki, safiri, ndi yahaloni; 19 ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; 20 ndi mzere wachinayi wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m’zoikamo zawo. 21 Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi aŵiri, monga maina awo; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga mwa maina awo, kwa mafuko khumi ndi aŵiri. 22 Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golidi wowona. 23 Nupangire pa chapachifuwa mphete ziŵiri zagolidi, ndi kuzika mphete ziŵirizo pa nsonga zake ziŵiri za chapachifuwa. 24 Numange maunyolo aŵiri opota agolidi ku mphete ziŵiri pansonga pake pa chapachifuwa. 25 Koma nsonga zake ziŵiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziŵiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziŵiri za efodi, mtsogolo mwake. 26 Ndipo upange mphete ziŵiri zagolidi, ndi kuzimanga pansonga zake ziŵiri za chapachifuwa, m’mphepete mwake, mkatimo ku mbali ya kuefodi. 27 Upangenso mphete ziŵiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziŵiri za efodi, m’munsi, ku mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. 28 Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke pa efodi. 29 Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakuloŵa iye m’malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. 30 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakuloŵa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israyeli pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza. 31 Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha. 32 Ndipo poloŵa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira poloŵa pake, wa ntchito yoomba, ngati poloŵa pa malaya ochinjiriza, pangang’ambike. 33 Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira; 34 mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. 35 Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nawo; ndipo limveke liwu lake pakuloŵa iye m’malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe. 36 Ndipo upange golidi waphanthiphanthi wowona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA. 37 Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira. 38 Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zawo zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova. 39 Ndipo upikule malaya amkati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika. 40 Ndipo usokere ana a Aroni malaya amkati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma. 41 Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lawo, ndi kuwapatula, andichitire ine ntchito ya nsembe. 42 Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche awo; ziyambire m’chuuno zifikire kuntchafu. 43 Ndipo azivale Aroni, ndi ana ake, pakuloŵa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo ku guwa la nsembe kutumikira m’malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.
29 Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng’ombe yamphongo, ndi nkhosa ziŵiri zamphongo zangwiro, 2 ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu. 3 Ndipo uziike mu mtanga umodzi, ndi kubwera nazo mumtanga, pamodzi ndi ng’ombe yamphongo ndi nkhosa ziŵiri zamphongo. 4 Ndipo ubwere nawo Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m’madzi. 5 Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya amkati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m’chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; 6 ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. 7 Pamenepo utenge mafuta odzoza nawo nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza. 8 Ndipo ubwere nawo ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya amkati. 9 Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m’chuuno mwawo, nuwamangire akapa pamutu pawo; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna. 10 Ndipo ubwere nayo ng’ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja awo pamutu pa ng’ombe yamphongoyo. 11 Nuphe ng’ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako. 12 Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng’ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe. 13 Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi imso ziŵiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe. 14 Koma nyama ya ng’ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo. 15 Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja awo pamutu pa nkhosa yamphongoyo. 16 Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira. 17 Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m’ziŵalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziŵalo zake, ndi pamutu pake. 18 Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. 19 Ndipo utenge nkhosa yamphongo inayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja awo pamutu pa nkhosa yamphongoyo. 20 Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja la ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lawo lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lawo lamanja, ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira. 21 Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nawo, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zawo zomwe pamodzi ndi iye. 22 Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, ndi mafuta akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi imso ziŵiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam’mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo yakudzaza manja; 23 ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosaganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, ziri mu mtanga wa mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova; 24 ndipo uike zonsezo m’manja a Aroni, ndi m’manja a ana ake aamuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25 Pamenepo uzilandire m’manja mwawo, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. 26 Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako. 27 Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam’mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ake aamuna; 28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israyeli; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israyeli, ya kwa nsembe zamtendere zawo, ndiyo nsembe yawo yokweza ya Yehova. 29 Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja awo atazivala; 30 mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m’malo mwake azivala masiku asanu ndi aŵiri, pakuloŵa iye m’chihema chokomanako kutumikira m’malo opatulika. 31 Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m’malo opatulika. 32 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mumtanga, pa khomo la chihema chokomanako. 33 Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi. 34 Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m’mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi. 35 Ndipo utero nawo Aroni, ndi ana ake aamuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja awo masiku asanu ndi aŵiri. 36 Nukonze ng’ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula. 37 Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi aŵiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulikitsa; chirichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika. 38 Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; ana a nkhosa aŵiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza. 39 Mwana wa nkhosa wina ukonze m’mawa; ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo; 40 ndi pa mwana wa nkhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anayi la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anayi la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira. 41 Ndi mwana wa nkhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira chopereka cha m’mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. 42 Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko. 43 Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israyeli; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga. 44 Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake aamuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe. 45 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli, ndi kukhala Mulungu wawo. 46 Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, amene ndinawatulutsa m’dziko la Aigupto, kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova Mulungu wawo.
30 Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wasitimu. 2 Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale lampwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iŵiri; nyanga zake zituluke m’mwemo. 3 Ndipo ulikute ndi golidi wowona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolidi pozungulira. 4 Ndipo ulipangire mphete ziŵiri zagolidi pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziŵiri, pa mbali zake ziŵiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo. 5 Ndipo upange mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi. 6 Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga iri ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chiri pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe. 7 Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m’mawa ndi m’mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize. 8 Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu. 9 Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena chopereka; musathirepo nsembe yothira. 10 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m’chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulikitsa la Yehova. 11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 12 Pamene uŵerenga ana a Israyeli, monga mwa maŵerengedwe awo, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuŵerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pawo, pakuŵerengedwa iwowa. 13 Ichi achipereke, yense wakupita kwa oŵerengedwa; limodzi la magawo aŵiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi aŵiri,) limodzi la magawo aŵiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova. 14 Yense wakupita kwa oŵerengedwawo, wa zaka makumi aŵiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova. 15 Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo aŵiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. 16 Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israyeli, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israyeli pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. 17 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti, 18 Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. 19 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna azisambiramo manja awo ndi mapazi awo; 20 pakuloŵa iwo m’chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova; 21 asambe manja awo ndi mapazi awo, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbewu zake, mwa mibadwo yawo. 22 Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti, 23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu, ndi kinimani lonunkhira limodzi mwa magawo aŵiri a mureyo, ndilo masekeli mazana aŵiri kudza makumi asanu, ndi kane lonunkhira mazana aŵiri kudza makumi asanu, 24 ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi; 25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika. 26 Ndipo udzoze nawo chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, 27 ndi gomelo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikapo nyali ndi zipangizo zake, 28 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake. 29 Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika. 30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe. 31 Nulankhule ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu. 32 Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika. 33 Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. 34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi libano lowona; miyeso yofanana; 35 ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosanganiza mwa machitidwe a wosanganiza, chokometsera ndi mchere, chowona, chopatulika; 36 nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m’chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu. 37 Koma za chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova. 38 Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wake.
31 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 2 Tawona ndaitana ndi kumtchula dzina lake, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda; 3 ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziŵitso, ndi m’ntchito zirizonse, 4 kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golidi ndi siliva ndi mkuwa, 5 ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mtengo, kuchita ntchito zirizonse. 6 Ndipo Ine, tawona, ndampatsa Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m’mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe; 7 chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chiri pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho; 8 ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikapo nyali chowona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo; 9 ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake; 10 ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe; 11 ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe. 12 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 13 Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziŵe kuti ine ndine Yehova wakukupatulani. 14 Ndipo muzisunga Sabata; popeza mdilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m’mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wake. 15 Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiŵiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu. 16 Chifukwa chake ana a Israyeli azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yawo, likhale pangano losatha; 17 ndicho chizindikiro chosatha pakati pa ine ndi ana a Israyeli; pakuti Yehova analenga zam’mwamba ndi dziko lapansi masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiŵiri, nawonanso mphamvu. 18 Ndipo atatha iye kulankhula ndi Mose, pa phiri la Sinai, anampatsa magome aŵiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.
32 Koma pamene anawona kuti Mose anachedwa kutsika m’phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Aigupto, sitidziŵa chomwe chamgwera. 2 Ndipo Aroni ananena nawo, Thyolani mphete zagolidi ziri m’makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. 3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolidi zinali m’makutu mwawo, nabwera nazo kwa Aroni. 4 Ndipo anazilandira ku manja awo, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwana wa ng’ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Aigupto. 5 Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova. 6 Ndipo m’mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kuseŵera. 7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nawo kuchokera m’dziko la Aigupto adziipsa; 8 apatuka msanga njira imene ndinawauza; adziyengera mwana wa ng’ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Aigupto. 9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, tawona, ndiwo anthu opulupudza; 10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa iwo ndi kuwatha, ndi kuuza iwe ukhale mtundu waukulu. 11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba? 12 Akaneneranji Aaigupto, ndi kuti, Anawatulutsa choipa, kuti awaphe m’mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu. 13 Kumbukirani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nawo, Ndidzachulukitsa mbewu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbewu zanu, likhale choloŵa chawo nthaŵi zonse. 14 Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake. 15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m’phirimo, magome aŵiri a mboni ali m’dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe. 16 Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo. 17 Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono. 18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa olakika, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang’ombe. 19 Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anawona mwana wa ng’ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m’manja mwake, nawaswa m’tsinde mwa phiri. 20 Ndipo anatenga mwana wa ng’ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli. 21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? 22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziŵa anthuwa kuti akhumba choipa. 23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Aigupto, sitidziŵa chomwe chamgwera. 24 Ndipo ndinanena nawo, Aliyense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m’moto, ndimo anatulukamo mwana wa ng’ombe uyu. 25 Ndipo pamene Mose anawona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani awo, 26 Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana aamuna onse a Levi anasonkhana kwa iye. 27 Ndipo ananena nawo, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Yense amange lupanga lake m’chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake. 28 Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mawu a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu. 29 Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino. 30 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu. 31 Ndipo Mose anabwerera kumka kwa Yehova, nati, Ha! pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolidi. 32 Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwawo; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m’buku lanu limene munalembera, 33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m’buku langa. 34 Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kumka nawo kumene ndinakuuza; tawona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwawo. 35 Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwana wa ng’ombe amene Aroni anapanga.
33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m’dziko la Aigupto, kumka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbewu zako ilo; 2 ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapitikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi; 3 kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira. 4 Ndipo pamene anthu anamva mawu awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake. 5 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israyeli, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kuloŵa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziŵe chomwe ndikuchitireni. 6 Ndipo ana a Israyeli anazichotsera zokometsera zawo kuyambira pa phiri la Horebe. 7 Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kumka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono. 8 Ndipo kunali, pakutuluka Mose kumka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chiriri, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira ataloŵa m’chihemacho. 9 Ndipo kunali, pakuloŵa Mose m’chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose. 10 Ndipo anthu onse anawona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake. 11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kumka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoka m’chihemamo. 12 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Tawonani, Inu munena ndi ine, Kwera nawo anthu awa; koma simunandidziŵitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziŵa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga. 13 Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziŵitsetu njira zanu, kuti ndikudziŵeni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu. 14 Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza. 15 Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno. 16 Pakuti chidziŵika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pankhope ya dziko lapansi? 17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziŵa dzina lako. 18 Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu. 19 Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo. 20 Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo. 21 Ndipo Yehova anati, Tawona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe; 22 ndipo kudzakhala, pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira; 23 ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzawona m’mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzawoneka.
34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome aŵiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mawu omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa. 2 Nukonzekeretu m’mawa, nukwere m’mawa m’phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri. 3 Palibe munthu akwere ndi iwe, asawonekenso munthu aliyense m’phiri monse; ndi zoŵeta zazing’ono kapena zoŵeta zazikulu zisadye kuphiri kuno. 4 Ndipo anasema magome aŵiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m’phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m’dzanja mwake magome aŵiri amiyala. 5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, nafuula dzina la Yehova. 6 Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; 7 wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi. 8 Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi, nalambira. 9 Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale choloŵa chanu. 10 Ndipo Iye anati, Tawona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pawo adzawona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa. 11 Dzisungire chimene ine ndikuuza lero lino: tawona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. 12 Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu; 13 koma mupasule maguwa a nsembe awo, ndi kuphwanya zoimiritsa zawo, ndi kulikha zifanizo zawo; 14 pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje; 15 ungachite pangano ndi iwo okhala m’dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yawo, nangaphere nsembe milungu yawo, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake; 16 ndipo ungatengereko ana ako aamuna ana awo aakazi; nangachite chigololo ana awo aakazi potsata milungu yawo, ndi kuchititsa ana anu aamuna chigololo potsata milungu yawo. 17 Usadzipangire milungu yonyenga. 18 Uzisunga madyerero a mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi aŵiri, monga ndakuuza pa nthaŵi yonenedwa, m’mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka m’Aigupto. 19 Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoŵeta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng’ombe ndi za nkhosa. 20 Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamawoneka pamaso panga opanda kanthu. 21 Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiŵiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula. 22 Ndipo uzichita madyerero a masabata, ndiwo madyerero a zipatso zoyamba za masika a tirigu, ndi madyerero a kututa pakutha pa chaka. 23 Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, katatu chaka chimodzi. 24 Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzawoneka pamaso a Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi. 25 Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m’mawa. 26 Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa make. 27 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mawu awa; pakuti monga mwa mawu awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli. 28 Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anayi, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mawu a panganolo, mawu khumiwo. 29 Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome aŵiri a mboni m’dzanja lake la Mose, pakutsika iye m’phirimo, Mose sanadziŵa kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza iye adalankhula naye. 30 Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israyeli anawona Mose, tawonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anawopa kumyandikiza. 31 Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nawo. 32 Ndipo atatero, ana onse a Israyeli anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m’phiri la Sinai. 33 Ndipo Mose atatha kulankhula nawo, anaika chophimba pankhope pake. 34 Koma pakuloŵa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israyeli chimene adamuuza. 35 Ndipo ana a Israyeli anawona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose naikanso chophimba pankhope pake, kufikira akaloŵa kulankhula ndi iye.
35 Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israyeli, nanena nawo, Siwa mawu amene Yehova anauza, kuti muwachite. 2 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe. 3 Musamasonkha moto m’nyumba zanu zirizonse tsiku la Sabata. 4 Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova anauza ndi kuti, 5 Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; 6 golidi, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; 7 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wasitimu; 8 ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma; 9 ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya chapachifuwa. 10 Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova anauza; 11 kachisi, hema wake, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa awo; 12 likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka; 13 gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate wowonekera; 14 ndi choikapo nyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika; 15 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la kachisi; 16 guwa la nsembe yopsereza, ndi made amkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake; 17 nsalu zotchingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo; 18 zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zawo; 19 zovala za kutumikira nazo m’malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe. 20 Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linachoka pamaso pa Mose. 21 Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika. 22 Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m’makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zidzingwiri, zonsezi zokometsera zagolidi; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolidi. 23 Ndipo aliyense kwawo kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa a akatumbu, anabwera nazo. 24 Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwawo kunapezeka mtengo wasitimu wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nawo. 25 Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja awo, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 26 Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi. 27 Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa; 28 ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma. 29 Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yawo inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova anauza ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chofuna mwini, kuchipereka kwa Yehova. 30 Ndipo Mose anati kwa ana a Israyeli, Tawonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda; 31 ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziŵitso, za m’ntchito zirizonse; 32 kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa; 33 ndi kuzokota miyala, ndi kuzokota mitengo, kuchita m’ntchito zirizonse zaluso. 34 Ndipo anaika m’mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Aholiabu mwana wa Ahisama, wa fuko la Dani. 35 Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zirizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iriyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso.
36 Pamenepo anachita Bezaleli ndi Aholiabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m’mtima mwawo adziŵe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova. 2 Ndipo Mose adaitana Bezaleli ndi Aholiabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m’mtima mwawo, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita. 3 Ndipo analandira Mose chopereka chonse, chimene ana a Israyeli adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anawonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zofuna mwini, m’mawa ndi m’mawa. 4 Ndipo aluso onse, akuchita ntchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya ntchito yawo analinkuchita; 5 nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike. 6 Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mawu mwa chigono chonse, ndi kuti, Asawonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina. 7 Popeza zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso. 8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga kachisi ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri. 9 Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi aŵiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inayi; nsalu zonse zinafanana muyeso wawo. 10 Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake. 11 Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m’mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m’mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiŵiri. 12 Anaika magango makumi asanu pa nsalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m’mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake. 13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolidi, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo kachisi anakhala mmodzi. 14 Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kachisi; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi. 15 Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inayi; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wawo. 16 Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha. 17 Ndipo anapanga magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m’mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china. 18 Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi. 19 Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake. 20 Ndipo anapanga matabwa a kachisi, oimirika, a mtengo wasitimu. 21 Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu. 22 Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iŵiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a kachisi. 23 Ndipo anapanga matabwa a kachisi; matabwa makumi aŵiri a ku mbali ya kumwera, kumwera; 24 napanga makamwa makumi anayi pansi pa matabwa makumi aŵiri; makamwa aŵiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iŵiri, ndi makamwa aŵiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iŵiri. 25 Ndi ku mbali ina ya kachisi, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi aŵiri, ndi makamwa awo makumi anayi asiliva; 26 makamwa aŵiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa aŵiri pansi pa thabwa lina. 27 Ndi ku mbali ya kumbuyo ya kachisi kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi. 28 Anapanganso matabwa aŵiri a ku ngondya za kachisi, m’mbali zake ziŵiri. 29 Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nawo onse aŵiri pa ngondya ziŵiri. 30 Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa awo asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi. 31 Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wasitimu; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya kachisi, 32 ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzake ya kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a kachisi ali pa mbali ya kumadzulo. 33 Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo. 34 Ndipo anakuta matabwa ndi golidi, napanga mphete zawo zagolidi zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golidi. 35 Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri. 36 Ndipo anaipangira mizati inayi yasitimu, nazikuta ndi golidi; zokowera zawo zinali zagolidi; ndipo anaziyengera makamwa anayi asiliva. 37 Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; 38 ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zawo; nakuta mitu yawo ndi mitanda yawo ndi golidi; ndi makamwa awo asanu anali amkuwa.
37 Ndipo Bezaleli anapanga likasa la mtengo wasitimu; utali wake mikono iŵiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; 2 ndipo analikuta ndi golidi wowona mkati ndi kunja, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pake. 3 Ndipo analiyengera mphete zinayi zagolidi pa miyendo yake inayi; mphete ziŵiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziŵiri pa mbali yake ina. 4 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi. 5 Ndipo anapisa mphiko m’mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa. 6 Ndipo anapanga chotetezerapo cha golidi wowona; utali wake mikono iŵiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. 7 Anapanganso akerubi aŵiri agolidi; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake aŵiri a chotetezerapo; 8 kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m’chotetezerapo, pa mathungo ake aŵiri. 9 Ndipo akerubi anafunyulira mapiko awo m’mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko awo, ndi nkhope zawo zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zawo. 10 Ndipo anapanga gome la mtengo wasitimu; utali wake mikono iŵiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; 11 ndipo analikuta ndi golidi wowona, nalipangira mkombero wagolidi pozungulira pake. 12 Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m’kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolidi. 13 Ndipo analiyengera mphete zinayi zagolidi, naika mphetezo pa ngondya zake zinayi zokhala pa miyendo yake inayi. 14 Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo. 15 Ndipo anapanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi, kunyamulira nazo gomelo. 16 Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golidi wowona. 17 Ndipo anapanga choikapo nyali cha golidi wowona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m’mwemo; 18 ndi m’mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m’mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m’mbali yake ina; 19 pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungulume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungulume, mutu ndi luwa; zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikapo nyali. 20 Ndipo pa choikapo nyali chomwe panali zikho zinayi zopangika ngati katungulume, mitu yake ndi maluwa ake; 21 ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziŵiri, zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziŵiri, zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziŵiri, zotuluka m’mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m’mwemo. 22 Mitu yawo ndi mphanda zawo zinatuluka m’mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golidi wowona. 23 Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziŵiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golidi wowona. 24 Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golidi wowona. 25 Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wasitimu; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, lampwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iŵiri; nyanga zake zinatuluka m’mwemo. 26 Ndipo analikuta ndi golidi wowona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolidi pozungulira pake. 27 Ndipo analipangira mphete ziŵiri zagolidi pansi pa mkombero wake, pa ngondya zake ziŵiri, pa mbali zake ziŵiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo. 28 Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi golidi. 29 Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nawo, ndi chofukiza chowona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosanganiza.
38 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu. 2 Ndipo anapanga nyanga zake pa ngondya zake zinayi; nyanga zake zinakhala zotuluka m’mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa. 3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa. 4 Ndipo anapangira guwa la nsembelo made, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa matso ake wakulekeza pakati pake. 5 Ndipo anayengera mathungo anayi a made amkuwawo mphete zinayi, zikhale zopisamo mphiko. 6 Napanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi mkuwa. 7 Ndipo anapisa mphikozo m’zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere. 8 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. 9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi; 10 nsichi zake makumi aŵiri, ndi makamwa awo makumi aŵiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva. 11 Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi aŵiri, ndi makamwa ake makumi aŵiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. 12 Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zotchingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. 13 Ndi pa mbali ya kum’mawa, kum’mawa, mikono makumi asanu. 14 Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu; 15 momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu. 16 Nsalu zotchingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa. 17 Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva. 18 Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi aŵiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo. 19 Ndi nsichi zake zinali zinayi, ndi makamwa ake anayi, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva. 20 Ndi zichiri zonse za chihema, ndi za bwalo lake pozungulira, nza mkuwa. 21 Ichi ndi chiŵerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziŵerenga, monga mwa mawu a Mose, achite nazo Alevi; anaziŵerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe. 22 Ndipo Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, anapanga zonse zimene Mulungu adauza Mose. 23 Ndi pamodzi naye Aholiabu, mwana wa Ahisama, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 24 Golidi yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golidi wa choperekacho, ndicho matalente makumi aŵiri kudza asanu ndi anayi, ndi masekeli masana asanu ndi aŵiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika. 25 Ndipo siliva wa iwo oŵerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi aŵiri, mphambu makumi asanu ndi aŵiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika; 26 munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo aŵiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kumka kwa oŵerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi aŵiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu. 27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi. 28 Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi aŵiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizitsana pamodzi. 29 Ndi mkuwa wa choperekacho ndiwo matalente makumi asanu ndi aŵiri, ndi masekeli zikwi ziŵiri kudza mazana anayi. 30 Ndipo anapanga nawo makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe, 31 ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo poungulira.
39 Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m’malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose. 2 Ndipo anaomba efodi wa golidi, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 3 Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. 4 Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziŵirizo anamlumikiza. 5 Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nawo unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adamuuza Mose. 6 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m’zoikamo zagolidi, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israyeli. 7 Ndipo anaika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso kwa ana a Israyeli; monga Yehova adamuuza Mose. 8 Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 9 Chinakhala champwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake chikhato chimodzi, ndi kupingasa kwake chikhato chimodzi, chinakhala chopindika. 10 Ndipo anaika pomwepo mizere inayi ya miyala; mzere wa edomu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba. 11 Ndi mzere wachiŵiri wa nofeki, safiri, ndi yahalomu. 12 Ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama. 13 Ndi mzere wachinayi wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golidi maikidwe ake. 14 Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi aŵiri, monga mwa maina awo; ngati malochedwe a chosindikizira, yonse monga mwa maina ake, kwa mafuko khumi ndi aŵiriwo. 15 Ndipo anapangira pachapachifuwa maunyolo ngati zingwe, ntchito yopota ya golidi wowona. 16 Anapanganso zoikamo ziŵiri zagolidi, ndi mphete ziŵiri zagolidi; naika mphete ziŵirizo pa nsonga ziŵiri za chapachifuwa. 17 Ndipo anamanga maunyolo aŵiri opota agolidi pa mphete ziŵiri pa nsonga za chapachifuwa. 18 Ndi nsonga zake ziŵiri zina za maunyolo aŵiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziŵiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, mtsogolo mwake. 19 Ndipo anapanga mphete ziŵiri zagolidi, naziika pa nsonga ziŵiri za chapachifuwa, m’mphepete mwake mkatimo, pa mbali ya kuefodi. 20 Ndipo anapanga mphete ziŵiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziŵiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. 21 Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose. 22 Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, ntchito yoomba ya lamadzi lokha; 23 ndi pakati pake poloŵa mutu, ngati poloŵa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira poloŵa pake, pangang’ambike. 24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. 25 Ndipo anapanga miliu ya golidi wowona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza. 26 Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose. 27 Ndipo anaomba malaya a bafuta, ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake aamuna, 28 ndi nduwira ya bafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa, 29 ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose. 30 Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golidi wowona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA. 31 Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nawo pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose. 32 Potero anatsiriza ntchito yonse ya kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israyeli adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo. 33 Ndipo anabwera naye kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangaizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake; 34 ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiirira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera; 35 likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo; 36 gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate wowonekera; 37 choikapo nyali chowona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira; 38 ndi guwa la nsembe lagolidi, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho; 39 guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ake amkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake; 40 nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya kachisi, za ku chihema chokomanako; 41 zovala zokoma za kutumikira nazo m’malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe. 42 Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israyeli anachita ntchito zonse. 43 Ndipo Mose anawona ntchito zonse, ndipo, tawonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
40 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 2 Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse kachisi wa chihema chokomanako. 3 Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nuchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo. 4 Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikapo nyalicho, ndi kuyatsa nyali zake. 5 Ndipo ukaike guwa la nsembe lagolidi chakuno cha likasa la mboni, numange pakachisi nsalu yotsekera pakhomo. 6 Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kachisi wa chihema chokomanako. 7 Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. 8 Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. 9 Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nawo kachisi, ndi zonse ziri m’mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika. 10 Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa. 11 Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula. 12 Ndipo ubwere nawo Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi. 13 Nuveke Aroni zovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire ine ntchito ya nsembe. 14 Ndipo ubwere nawo ana ake aamuna ndi kuwaveka malaya amkati; 15 nuwadzoze, monga unadzoza atate wawo, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwawo kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yawo. 16 Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita. 17 Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiŵiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kachisi. 18 Ndipo Mose anautsa kachisi, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake. 19 Ndipo anayalika hema pamwamba pa kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose. 20 Ndipo anatenga mboniyo, naiika m’likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa; 21 naloŵa nalo likasa m’kachisi, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. 22 Ndipo anaika gomelo m’chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga. 23 Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. 24 Ndipo anaika choikapo nyali m’chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya kachisi. 25 Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. 26 Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m’chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga; 27 nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose. 28 Ndipo anapachika kukachisi nsalu yotsekera pakhomo. 29 Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose. 30 Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. 31 Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake aamuna anasamba manja awo ndi mapazi awo mmenemo; 32 pakuloŵa iwo m’chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose. 33 Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi. 34 Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kachisiyo. 35 Ndipo Mose sanathe kuloŵa m’chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kachisi. 36 Ndipo pakukwera mtambo kuchokera kukachisi, ana a Israyeli amayenda maulendo awo onse; 37 koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wawo kufikira tsiku loti wakwera. 38 Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pakachisi msana, ndi usiku munali moto mmenemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israyeli, m’maulendo awo onse.