Genesis

Chichewa
Chichewa file
Literature type
Literature notes

Genesis

1 Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 2 Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi. 3 Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. 4 Ndipo anawona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima. 5 Ndipo Mulungu anatcha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku loyamba. 6 Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi. 7 Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero. 8 Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku lachiŵiri. 9 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uwoneke mtunda: ndipo kunatero. 10 Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anawona Mulungu kuti kunali kwabwino. 11 Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbewu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbewu yake, pa dziko lapansi: ndipo kunatero. 12 Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbewu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbewu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anawona Mulungu kuti kunali kwabwino. 13 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku lachitatu. 14 Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka; 15 zikhale zounikira m’thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero. 16 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziŵiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching’ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. 17 Mulungu ndipo adaika zimenezo m’thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi. 18 nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anawona Mulungu kuti kunali kwabwino. 19 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku lachinayi. 20 Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga. 21 Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m’madzi mwa mitundu yawo, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anawona Mulungu kuti kunali kwabwino. 22 Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m’nyanja, ndi mbalame zichuluke pa dziko lapansi. 23 Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku lachisanu. 24 Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yawo, ng’ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yawo: ndipo kunatero. 25 Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yawo; ndi ng’ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yawo; ndipo Mulungu anawona kuti kunali kwabwino. 26 Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. 27 Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. 28 Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi. 29 Ndipo anati Mulungu, Tawonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbewu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse mmene muli chipatso cha mtengo wakubala mbewu; chidzakhala chakudya cha inu: 30 ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi mmene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero. 31 Ndipo anaziwona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

2 Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lawo lonse. 2 Tsiku lachisanu ndi chiŵiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ku ntchito yake yonse. 3 Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga. 4 Imeneyo ndiyo mibadwo yawo ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. 5 Ndi zomera zonse za m’munda zisanakhale m’dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m’munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka; 6 koma inakwera nkhungu yotuluka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka. 7 Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo. 8 Ndipo Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakum’maŵa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. 9 Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m’nthaka mitengo yonse yokoma m’maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. 10 Ndipo unatuluka m’Edene mtsinje wakuthirira m’mundamo, mmenemo, ndipo unalekana nuchita miyendo inayi. 11 Dzina la wakuyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, mmene muli golidi; 12 golidi wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. 13 Dzina la mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. 14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidikeli: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum’maŵa kwake kwa Asuri. Mtsinje wachinayi ndi Firate. 15 Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m’munda wa Edene kuti aulime nauyang’anire. 16 Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m’munda udyeko; 17 koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu. 18 Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye. 19 Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m’thengo, ndi mbalame zonse za m’mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina awo. 20 Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m’mlengalenga ndi zamoyo zonse za m’thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye. 21 Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona: ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake: 22 ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. 23 Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. 24 Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. 25 Onse aŵiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.

3 Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu? 2 Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye. 3 Koma zipatso za mtengo umene uli mkati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe. 4 Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; 5 chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa. 6 Ndipo pamene anawona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya nayenso. 7 Ndipo anatseguka maso awo a onse aŵiri, nadziŵa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera. 8 Ndipo anamva mawu a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m’munda nthaŵi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m’munda. 9 Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti? 10 Ndipo anati, Ndinamva mawu anu m’mundamu, ndipo ndinawopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala. 11 Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye? 12 Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya. 13 Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya. 14 Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako: 15 ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake. 16 Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe. 17 Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mawu a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: 18 minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo: 19 m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m’menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera. 20 Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Hava; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse. 21 Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo. 22 Ndipo anati Yehova Mulungu, Tawonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziŵa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthaŵi zonse, 23 Yehova Mulungu anamtulutsa iye m’munda wa Edene, kuti alime nthaka m’mene anamtenga iye. 24 Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi cha kum’maŵa kwake kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.

4 Ndipo mwamunayo anadziŵa mkazi wake Hava: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova. 2 Ndipo anabalanso mphwache Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka. 3 Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova. 4 Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang’anira Abele ndi nsembe yake: 5 koma sanayang’anira Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake. 6 Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? 7 Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye. 8 Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwache. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwache, namupha. 9 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwayi: kodi ndine woyang’anira mphwanga? 10 Ndipo anati, Wachita chiyani? Mawu a mwazi wa mphwako andifuulira ine kunthaka. 11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako: 12 pamene udzalima panthaka ziidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi. 13 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka. 14 Tawonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha. 15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kaŵiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza. 16 Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m’dziko la Nodi, kum’maŵa kwake kwa Edene. 17 Ndipo Kaini anamdziŵa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoke. 18 Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke. 19 Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi aŵiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila. 20 Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wawo wa iwo okhala m’mahema, akuweta ng’ombe. 21 Ndi dzina la mphwache ndilo Yubala; iye ndiye atate wawo wa iwo oyimba zeze ndi chitoliro. 22 Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Nama. 23 Lameke ndipo anati kwa akazi ake: Tamvani mawu anga, Ada ndi Zila; Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine, 24 Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kaŵiri, Koma Lameke makumi asanu ndi aŵiri. 25 Ndipo Adamu anadziŵanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti: Chifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbewu yina m’malo wa Abele amene Kaini anamupha. 26 Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova.

5 Ili ndi bukhu la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m’chifanizo cha Mulungu; 2 anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wawo anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo. 3 Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m’chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti. 4 Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. 5 Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anayi, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira. 6 Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi; 7 ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziŵiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi: 8 masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anayi kudza khumi ndi ziŵiri; ndipo anamwalira. 9 Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anayi, nabala Kenani; 10 ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. 11 Masiku ake onse a Enosi anali mazana asanu ndi anayi kudza zisanu; ndipo anamwalira. 12 Ndipo Kenni anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi aŵiri, ndipo anabala Mahalalele: 13 ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anayi, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi; 14 masiku ake onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anayi kudza khumi; ndipo anamwalira. 15 Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi; 16 ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi: 17 masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anayi ndi zisanu; ndipo anamwalira. 18 Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza maumi asanu ndi limodzi ndi ziŵiri, nabala Enoke; 19 ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoke, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi; 20 masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anayi kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziŵiri: ndipo anamwalira. 21 Ndipo Enoke anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela: 22 ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi; 23 masiku ake onse a Enoke anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu; 24 ndipo Enoke anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga. 25 Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziŵiri, nabala Lameke; 26 ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameke, zaka mazana asanu ndi aŵiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziŵiri, nabala ana aamuna ndi aakazi: 27 masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anayi kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinayi; ndipo anamwalira. 28 Ndipo Lameke anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziŵiri, nabala mwana wamwamuna; 29 namutcha dzina lake, Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova; 30 ndipo Lameke anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anayi ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi: 31 masiku ake onse a Lameke anali zaka mazana asanu ndi aŵiri kudza makumi asanu ndi aŵiri; ndipo anamwalira. 32 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti.

6 Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, 2 kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. 3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthaŵi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi aŵiri. 4 Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka. 5 Ndipo anawona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha. 6 Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake. 7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo. 8 Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova. 9 Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu. 10 Ndipo Nowa anabala ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti. 11 Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. 12 Ndipo Mulungu anawona dziko lapansi, ndipo tawonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi. 13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; tawonani, ndidzawononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi. 14 Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m’chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m’kati ndi kunja. 15 Kupanga kwake ndi kotere: m’litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m’mimba mwake mikono makumi asanu, m’msinkhu mwake mikono makumi atatu. 16 Uike zenera m’chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m’mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiŵiri, ndi yachitatu, 17 Ndine, tawonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chifumula cha madzi pa dziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, m’mene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m’dziko lapansi zidzafa. 18 Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m’chingalamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. 19 Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziŵiri ziŵiri za mtundu wawo ulowetse m’chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi. 20 Za mbalame monga mwa mitundu yawo, ndi zinyama monga mwa mitundu yawo, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yawo, ziŵiri ziŵiri monga mwa mitundu yawo, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo. 21 Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo. 22 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.

7 Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuwona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno. 2 Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziŵiri, zisanu ndi ziŵiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziŵiri ziŵiri yamphongo ndi yaikazi yake. 3 Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziŵiri, zisanu ndi ziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbewu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi. 4 Pakuti akapita masiku asanu ndi aŵiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziwononga pa dziko lapansi. 5 Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova. 6 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali pa dziko lapansi. 7 Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m’chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula. 8 Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi, 9 zinaloŵa ziŵiri ziŵiri kwa Nowa m’chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa. 10 Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi aŵiri, madzi a chigumula anali padziko lapansi. 11 Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiŵiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi aŵiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka. 12 Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku. 13 Tsiku lomwelo analowa m’chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nawo: 14 iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yawo, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yawo, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yawo, ndi mbalame zonse za mitundu mitundu. 15 Ndipo zinalowa kwa Nowa m’chingalawamo ziŵiri ziŵiri zamoyo zonse, mmene muli mpweya wa moyo. 16 Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye. 17 Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anayi: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba pa dziko lapansi. 18 Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu pa dziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi. 19 Ndipo madzi anapambana ndithu padziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse. 20 Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. 21 Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda pa dziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi, ndi anthu onse: 22 zonse zimene m’mphuno zawo munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa. 23 Ndipo zinawonongedwa zamoyo zimene zonse zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m’mlengalenga; ndipo zinawonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m’chingalawa. 24 Ndipo anapambana madzi pa dziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu.

8 Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m’chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi; 2 ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba; 3 ndipo madzi anaphweraphwerabe pa dziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa. 4 Ndipo chingalaŵa chinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi aŵiri la mwezi. 5 Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri. 6 Ndipo panali atapita masiku makumi anayi, Nowa anatsegula pa zenera la chingalaŵa limene analipanga: 7 ndipo anatulutsa khungubwe, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi. 8 Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti awone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi; 9 koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwerera kwa iye kuchingalaŵako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m’chingalaŵamo. 10 Ndipo analinda masiku ena asanu ndi aŵiri; natulutsanso njiwayo m’chingalaŵamo; 11 ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, tawonani, m’kamwa mwake munali tsamba lazitona lothyoledwa: ndipo anadziŵa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi. 12 Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi aŵiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye. 13 Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa chindwi lake pachingalawa, nayang’ana, ndipo tawonani, padauma pa dziko lapansi. 14 Mwezi wachiŵiri tsiku la makumi aŵiri kudza asanu ndi aŵiri la mwezi, lidauma dziko lapansi. 15 Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti, 16 Tulukamoni m’chingalaŵamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. 17 Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse ziri ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi; kuti ziswane pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi. 18 Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye: 19 zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa pa dziko lapansi, monga mwa mitundu yawo, zinatuluka m’chingalaŵamo. 20 Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo. 21 Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m’mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu iri yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. 22 Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthaŵi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekayi.

9 Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi. 2 Kuopsya kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m’mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m’nyanja, zapatsidwa m’dzanja lanu. 3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. 4 Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye. 5 Zowonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. 6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu. 7 Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke mmenemo. 8 Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti, 9 Ndipo ine, tawonani, ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbewu zanu pambuyo panu; 10 ndi zamoyo zonse ziri pamodzi ndi inu, zouluka, ng’ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m’chingalaŵa, zinyama zonse za dziko lapansi. 11 Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula chakuwononga dziko lapansi. 12 Ndipo anati Mulungu, Ichi [ndicho] chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi ine ndi inu, ndi zamoyo zonse ziri pamodzi ndi inu, ku mibadwo mibadwo; 13 ndiika Utaŵaleza wanga m’mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi ine ndi dziko lapansi. 14 Ndipo padzakhala [pophimba] ndi mitambo ine dziko lapansi, utawo udzawoneka m’mtambomo; 15 ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene liri ndi ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuwononga zamoyo zonse. 16 Ndipo utawo udzakhala m’mtambo; ndipo ndidzauyang’anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi. 17 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndicho chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi. 18 Ndi ana aamuna a Nowa amene anatuluka m’chingalaŵa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wake wa Kanani. 19 Ameneŵa ndiwo ana aamuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi. 20 Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa: 21 namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche mkati mwa hema wake. 22 Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauwona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake aŵiri amene anali kunja. 23 Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa awo a onse aŵiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wawo: nkhope zawo zinali chambuyo, osawona umaliseche wa atate wawo. 24 Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziŵa chimene anamchitira iye mwana wake wamng’ono. 25 Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani: Adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo: 26 Ndipo anati: Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake. 27 Mulungu akuze Yafeti, Akhale iye m’mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake. 28 Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu. 29 Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anayi kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.

10 Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija. 2 Ana aamuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Mesheki, ndi Tirasi. 3 Ndi ana aamuna a Gomeri: Asekenazo, ndi Rifata, ndi Togarma. 4 Ndi ana aamuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu. 5 Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m’maiko mwawo, onse amene monga mwa chinenedwe chawo; ndi mwa mabanja awo, ndi m’mitundu yawo. 6 Ndi ana aamuna a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, ndi Puti, ndi Kanani. 7 Ndi ana aamuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedane. 8 Ndipo Kusi anabala Nimrode; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi. 9 Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimrode mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova. 10 Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babele, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m’dziko la Sinara. 11 M’dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Ashuri, namanga Nineve, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala, 12 ndi Resene pakati pa Nineve ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukulu. 13 Mizraimu ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabimu, ndi Nafituhimu, 14 ndi Patrusimu, ndi Kasiluhimu, mmenemo ndipo anatuluka Afilitsi, ndi Kafitorimu. 15 Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti: 16 ndi Ajebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi; 17 ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini; 18 ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira. 19 Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. 20 Ameneŵa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja awo, mwa zinenedwe zawo, m’maiko awo, m’mitundu yawo. 21 Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Ebere, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. 22 Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Ashuri, ndi Aripakasadi, ndi Ludi, ndi Aramu. 23 Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli, ndi Getere, ndi Masi. 24 Aripakasadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Ebere. 25 Kwa Ebere ndipo kunabadwa ana aamuna aŵiri; dzina la wina ndi Pelege; chifukwa kuti m’masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwache ndi Yokitani. 26 Ndipo Yokitani anabala Alamodadi, ndi Selefe, ndi Hazaramaveti, ndi Yera; 27 ndi Hadorimu ndi Uzali, ndi Dikila; 28 ndi Obali, ndi Abimaele, ndi Sheva; 29 ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabi; onse ameneŵa ndi ana a Yokitani. 30 Kwawo kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefere phiri la kum’maŵa. 31 Ameneŵa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja awo, mwa zinenedwe zawo, m’maiko awo, m’mitundu yawo. 32 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yawo, m’mitundu yawo: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula.

11 Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi. 2 Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum’maŵa, anapeza chigwa m’dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. 3 Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziotchetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. 4 Ndipo anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi. 5 Ndipo Yehova anatsikira kudzawona mudzi nd nsanja imene analinkumanga ana a anthu. 6 Ndipo Yehova anati, Tawonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chawo chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nawo kamene akafuna kuchita. 7 Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chawo, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake. 8 Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi. 9 Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi. 10 Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakasadi, chitapita chigumula zaka ziŵiri; 11 ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakasadi, nabala ana aamuna ndi aakazi. 12 Ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu, nabala Sela; 13 ndipo Aripakasadi anakhala ndi moyo zaka mazana anayi kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi. 14 Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Ebere; 15 ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anayi kudza zitatu, atabala Ebere, nabala ana aamuna ndi aakazi. 16 Ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinayi, nabala Pelege; 17 ndipo Ebere anakhala ndi moyo zaka mazana anayi kudza makumi aŵiri, atabala Pelege, nabala ana aamuna ndi aakazi. 18 Ndipo Pelege anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu; 19 ndipo Pelege anakhala ndi moyo zaka mazana aŵiri kudza zisanu ndi zinayi, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi. 20 Ndip Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziŵiri, nabala Serugi: 21 ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana aŵiri kudza zisanu ndi ziŵiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi. 22 Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori: 23 ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana aŵiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi. 24 Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi aŵiri kudza zisanu ndi zinayi, nabala Tera: 25 ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinayi, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi. 26 Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi aŵiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harana. 27 Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harana; ndipo Harana anabala Loti. 28 Ndipo anafa Harana pamaso pa atate wake Tera m’dziko la kubadwa kwake, m’Uri wa kwa Akaldayo. 29 Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harana, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Yisika. 30 Koma Sarai anali wouma; analibe mwana. 31 Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harana, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nawo ku Uri wa kwa Akaldayo kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harana, nakhala kumeneko. 32 Masiku a Tera anali zaka mazana aŵiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera m’Harana.

12 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; 2 ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; 3 ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi. 4 Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi aŵiri kudza zisanu, pamene anatuluka m’Harana. 5 Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwache, ndi chuma chawo chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m’Harana; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani. 6 Ndipo Abramu anapitira m’dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m’dzikomo nthaŵi yomweyo. 7 Ndipo Yehova anawonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbewu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuwonekera iye. 8 Ndipo iye anachoka kumeneko kunka ku phiri la kum’maŵa kwa Beteli, namanga hema wake; Beteli anali kumadzulo, ndi Ai anali kum’maŵa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova. 9 Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera. 10 Ndipo munali njala m’dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Aigupto kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m’dziko mmenemo. 11 Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m’Aigupto, anati kwa Sarai mkazi wake, Tawonani, ndidziŵa kuti ndiwe mkazi wokongola mawonekedwe ako; 12 ndipo padzakhala pamene adzakuwona iwe Aaigupto, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. 13 Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa chake iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe. 14 Ndipo panali pamene Abramu analowa m’Aigupto, Aaigupto anawona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. 15 Ndipo akaronga ake a Farao anamuwona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao. 16 Ndipoanamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu aakazi, ndi ngamila. 17 Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu. 18 Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? chifukwa chanji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako? 19 Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke. 20 Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m’njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

13 Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Aigupto, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera. 2 Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng’ombe ndi siliva ndi golidi. 3 Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Beteli, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja, pakati pa Beteli ndi Ai; 4 kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova. 5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng’ombe ndi mahema. 6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chawo chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi. 7 Ndipo panali ndewu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperezi ndipo analinkukhala nthaŵi yomweyo m’dzikomo. 8 Ndipo Abramu anatikwa Loti, Tisachite ndewu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. 9 Dziko lonse siliri pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere. 10 Ndipo Loti anatukula maso ake nayang’ana chigwa chonse cha Yordano kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanawononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakunka ku Zoari. 11 Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordano; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum’maŵa: ndipo analekana wina ndi mnzake. 12 Ndipo Abramu anakhala m’dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m’midzi ya m’chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu. 13 Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova. 14 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang’ane kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kum’mwera, ndi kum’maŵa, ndi kumadzulo: 15 chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuwona, ndidzakupatsa iwe ndi mbewu yako nthaŵi yonse. 16 Ndipo ndizayesa mbewu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuŵerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbewu yako idzaŵerengedwa. 17 Tauka, nuyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo. 18 Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre, imene iri m’Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.

14 Ndipo panali masiku a Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara, ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, 2 iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabi mfumu ya Adima, ndi pa Semebere mfumu ya Ziboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zoari). 3 Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa nyanja yamchere). 4 Zaka khumi ndi ziŵiri iwo anamtumikira Kedorelaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka. 5 Chaka chakhumi ndi chinayi ndipo anadza Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefai m’Aseteroti-karnaimu, ndi Azuzi m’Hamu, ndi Aemi m’Savekiriataimu, 6 ndi Ahori pa phiri lawo Seiri kufikira ku Eliparana, kumene kuli pachipululu. 7 Ndipo anabwera nafika ku Eni-Misipati (kumeneko ndi ku Kadese), nakantha dziko lonse la Aamaleki, ndiponso Aamori amene akhala m’Hazezoni-tamara. 8 Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zoari) ndipo anawathira nkhondo m’chigwa cha Sidimu; 9 ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara; mafumu anayi kugwirana ndi asanu. 10 Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge tho; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa mmenemo: amene anatsala anathawira kuphiri. 11 Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zawo zonse, namuka. 12 Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m’Sodomu, ndi chuma chake, namuka. 13 Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundi ya pa Mamre M-amori, mkulu wake wa Esakolo, ndi mkulu wake wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu. 14 Pamene anamva Abramu kuti mphwache anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani. 15 Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko. 16 Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe. 17 Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu), 18 Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anatuluka nawo mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu. 19 Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi; 20 ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m’dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse. 21 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. 22 Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, 23 kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu; 24 koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lawo la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Aneri, Esikolo, ndi Mamre, iwo atenge gawo lawo.

15 Zitapita izo, mawu a Yehova anadza kwa Abramu m’masomphenya, kuti, Usawope, Abramu, ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu. 2 Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliezere wa ku Damasiko? 3 Ndipo Abramu anati, Tawonani, simunandipatse ine mbewu; ndipo, tawonani, wobadwa m’nyumba mwanga adzalowa m’malo mwanga. 4 Ndipo, tawonani, mawu a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m’malo mwako; koma iye amene adzatuluka m’chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m’malo mwako. 5 Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang’anatu kumwamba, uŵerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziŵerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbewu zako. 6 Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo. 7 Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe m’Uri wa kwa Akaldayo, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako. 8 Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziŵa bwanji kuti lidzakhala choloŵa changa? 9 Ndipo anati kwa iye, Kanditengere ine ng’ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda. 10 Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidula. 11 Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo. 12 Ndipo linalinkuloŵa dzuŵa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo tawonani, kuwopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye. 13 Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbewu zako zidzakhala alendo m’dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anayi; 14 ndiponso mtunduwo adzautumikira, ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri. 15 Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m’mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino. 16 Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinayi: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe. 17 Ndipo panali pamene litaloŵa dzuŵa ndi kudza mdima, tawonani, ng’anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo. 18 Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbewu zako dziko ili, kuyambira pa nyanja ya Aigupto kufikira pa nyanja yaikulu, nyanja ya Firate: 19 Akeni ndi Akenizi, Akadimoni, ndi Ahiti, ndi Aperezi, ndi Arefai, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ajebusi. 20 ... 21 ...

16 Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Aigupto, dzina lake Hagara. 2 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Tawonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mawu a Sarai. 3 Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Aigupto, Abramu atakhala m’dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake. 4 Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anawona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m’maso mwake. 5 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuwona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m’maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine. 6 Koma Abramu anati kwa Sarai, Tawona, mdzakazi wako ali m’dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m’maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake. 7 Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m’chipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri. 8 Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake wa wakuka wanga Sarai. 9 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake. 10 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndzidzachulukitsa ndithu mbewu zako, kuti unyinji wawo sudzawerengeka. 11 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Tawona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismayeli; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako. 12 Ndipo iye adzakhala munthu wa m’thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse. 13 Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiwona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang’ana pambuyo pake pa iye amene wakundiwona ine? 14 Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beerelahai-roi; tawonani chiri pakati pa Kadese ndi Berede. 15 Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna, ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismayeli. 16 Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismayeli.

17 Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi zinayi, Yehova anamuwonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro. 2 Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi ine ndi iwe, ndipo ndidzachulukitsa iwe kwambiri. 3 Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti, 4 Koma ine, tawona, pangano langa liri ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu. 5 Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu. 6 Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe. 7 Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi ine ndi iwe pa mbewu zako za pambuyo pako m’mibadwo yawo, kuti likhale pangano la nthaŵi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbewu zako za pambuyo pako. 8 Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbewu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthaŵi zonse: ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo. 9 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangalo langa, iwe ndi mbewu zako za pambuyo pako m’mibadwo yawo. 10 Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa ine ndi iwe ndi mbewu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu. 11 Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi inu. 12 A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m’mibadwo mwanu, amene abadwa m’nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbewu zako. 13 Azidulidwatu amene abadwa m’nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m’thupi mwako pangano losatha. 14 Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa. 15 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamatcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. 16 Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake a mitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye. 17 Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m’mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anayi adzabala? 18 Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismayeli akhale ndi moyo pamaso panu! 19 Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isake; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthaŵi zonse, la ku mbewu zake za pambuyo pake. 20 Koma za Ismayeli, ndamvera iwe: tawona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi aŵiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. 21 Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isake, amene Sara adzakubalira iwe nthaŵi yomwe yino chaka chamawa. 22 Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu. 23 Ndipo Abrahamu anatenga Ismayeli mwana wake ndi onse amene anabadwa m’nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lawo tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye. 24 Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anayi kudza zisanu ndi zinayi, pamene anadulidwa m’khungu lake. 25 Ndipo Ismayeli mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m’khungu lake. 26 Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismayeli mwana wake. 27 Ndipo amuna onse a m’nyumba mwake obadwa m’nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye.

18 Ndipo Yehova anamuwonekera iye pa [mitengo] yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuŵa. 2 .Ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, tawonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anawona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nawo, nawerama pansi, nati, 3 Mbuyanga, ngatitu ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu; 4 nditengetu madzi pang’ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; 5 ndipo ndidzatenga chakudya pang’ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena. 6 Ndipo Abrahamu analowa msanga m’hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate. 7 Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng’ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika. 8 Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng’ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pawo; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya. 9 Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Tawonani m’hemamo. 10 Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; tawonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake. 11 Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku awo; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi; 12 ndipo Sara anaseka m’mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? 13 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? 14 Kodi chiripo chinthu chomlaka Yehova? Pa nthaŵi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. 15 Koma Sara anakana, nati, Sindinasekayi; chifukwa anawopa. Ndipo anati, Iyayi; koma unaseka. 16 Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang’ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nawo kuwaperekeza. 17 Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita? 18 Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye? 19 Chifukwa ndamdziŵa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye. 20 Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwawo kuli kulemera ndithu, 21 ndidzatsikatu ndikawone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziŵa. 22 Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu, Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. 23 Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa? 24 Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi; kodi mudzawononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? 25 Musamatero ayi, kupha olungama pamodzi ndi oipa, [kuti] olungama akhale monga oipa; musamatero ayi; kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi? 26 Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m’Sodomu olungama makumi asanu mkati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo. 27 Ndipo anayankha Abrahamu nati, Tawonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: 28 kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzawononga mudzi wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anayi ndi asanu sindidzauwononga. 29 Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anayi m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anayi. 30 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m’menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m’menemo sindidzachita. 31 Ndipo anati, Tawonanitu, ndidziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi aŵiri m’menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi aŵiri. 32 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m’menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi. 33 Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.

19 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga aŵiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anawona iwo, nauka kuti akakomane nawo, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake. 2 Ndipo anati, Tawonanitu, ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m’nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m’maŵa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iyayi; koma tigone m’khwalalamu usiku wonse. 3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m’nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya. 4 Koma asanagone, anthu a m’mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m’mbali zonse; 5 ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe. 6 Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake. 7 Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere. 8 Tawonanitu, ndiri ndi ana aakazi aŵiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nawo chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa. 9 Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko. 10 [Koma] anthu aja anatulutsa dzanja lawo, namlowetsa Loti momwe anali iwo m’nyumba, natseka pakhomo. 11 Ndipo anachititsa khungu m’maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang’ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. 12 Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nawo ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nawo m’mudzi muno, utuluke nawo m’malo muno: 13 popeza ife tidzawononga malo ano, chifukwa kulira kwawo kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuwononge. 14 Ndipo anatuluka Loti nanena nawo akamwini ake amene anakwata ana ake aakazi, nati, Taukani, tulukani m’malo muno; popeza Yehova adzawononga mudziwu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. 15 Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako aakazi aŵiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m’mphulupulu ya mudzi. 16 Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake aakazi aŵiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipoanamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi. 17 Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke. 18 Ndipo Loti anati kwa iwo, Iyayitu, mfumu; 19 tawonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe: 20 tawonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung’ono; ndithawiretu kumeneko, suli [waung’ono] nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo. 21 Ndipo anati kwa iye, Tawona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzawononga mudzi uwu umene wandiuza. 22 Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithayi kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mudziwo Zoari. 23 Ndipo dzuŵa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari. 24 Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba; 25 ndipo anawononga midziyo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m’midzimo, ndi zimene zimera panthaka. 26 Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere. 27 Ndipo Abrahamu analawira m’mamaŵa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova: 28 ndipo anayang’anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, tawonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng’anjo. 29 Ndipo panali pamene Mulungu anawononga midzi ya m’chigwa, Mulungu nakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chiwonongeko, pamene anawononga midzi m’mene anakhalamo Loti. 30 Ndipo Loti anabwera kutuluka m’Zoari nakhala m’phiri ndi ana aakazi aŵiri pamodzi naye: chifukwa anawopa kukhala m’Zoari, ndipo anakhala m’phanga, iye ndi ana ake aakazi. 31 Woyamba ndipo anati kwa wamng’ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita pa dziko lonse lapansi: 32 tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbewu za atate wathu. 33 Ndipo anamwetsa atate wawo vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziŵa pomwe anagona ndi pomwe anauka. 34 Ndipo panali m’mamawa, woyamba anati kwa wamng’ono, Tawona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbewu za atate wathu. 35 Ndipo anamwetsa vinyo atate wawo usiku womwenso; wamng’ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziŵa pomwe anagona ndi pomwe anauka. 36 Ndipo ana aakazi aŵiri a Loti anali ndi pakati pa atate wawo. 37 Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake; Moabu, yemweyo ndi atate wa Amoabu kufikira lero. 38 Wamng’ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benammi; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.

20 Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kedesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo m’Gerari. 2 Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleke mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara. 3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleke m’kulota kwa usiku, nati kwa iye, Tawona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini. 4 Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama? 5 Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi. 6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m’kulota, Inde ndidziŵa ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo. 7 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nawo. 8 Ndipo Abimeleke analawira m’mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m’makutu mwawo, ndipo anthu anawopa kwambiri. 9 Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita. 10 Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Unawona chiyani iwe kuti wachita Ichi? 11 Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga. 12 Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amayi wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga. 13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga. 14 Ndipo Abimeleke anatenga nkhosa ndi ng’ombe [ndi] akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake. 15 Ndipo Abimeleke anati, Tawona dziko langa liri pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko. 16 Kwa Sara ndipo anati, Tawona, ndapatsa mlongo wako ndalama za siliva mazana khumi; tawona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama. 17 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleke, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana. 18 Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m’nyumba ya Abimeleke, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.

21 Ndipo Yehova anayang’anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena. 2 Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m’ukalamba wake mwana wamwamuna, nthaŵi yomweyo Mulungu anamuuza iye. 3 Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isake. 4 Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isake pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye. 5 Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isake mwana wake. 6 Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. 7 Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m’ukalamba wake. 8 Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero aakulu tsiku lomwe analetsedwa Isake kuyamwa. 9 Ndipo Sara anawona mwana wake wamwamuna wa Hagara M-aigupto, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka. 10 Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m’nyumba pamodzi naye mwana wanga Isake. 11 Ndipo mawuwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake. 12 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nawo, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mawu ake; chifukwa kuti mwa Isake zidzaitanidwa mbewu zako. 13 Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbewu yako. 14 Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m’chipululu cha Beereseba. 15 Ndipo anatha madzi a m’mchenje ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba. 16 Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa mubvi: chifukwa anati, Ndisawone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mawu ake nalira. 17 Ndipo Mulungu anamva mawu a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mawu odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usawope; chifukwa Mulungu anamva mawu a mnyamata kumene ali. 18 Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m’dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. 19 Ndipo Mulungu anamtsegula m’maso mwake, ndipo anawona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe. 20 Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m’chipululu, nakhala wauta. 21 Ndipo anakhala m’chipululu cha Parana; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Aigupto. 22 Ndipo panali nthaŵi yomweyo, Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m’zonse uzichita iwe; 23 tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo. 24 Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira. 25 Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleke chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleke anachilanda. 26 Ndipo anati Abimeleke, Sindinadziwe amene anachita icho; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino. 27 Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng’ombe, nampatsa Abimeleke, ndipo anapangana pangano onse aŵiriwo. 28 Ndipo Abrahamu anapatula ana a nkhosa aakazi asanu ndi aŵiri pa okha. 29 Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Nanga ana a nkhosa aakazi asanu ndi aŵiri amene wapatula pa okha? 30 Ndipo anati, Ana a nkhosa aakazi asanu ndi aŵiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi. 31 Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse aŵiri. 32 Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleke ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilitsi. 33 Ndipo Abrahamu anawoka mtengo wabwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova Mulungu wa nthaŵi zonse. 34 Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m’dziko la Afilitsi.

22 Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano. 2 Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isake, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe. 3 Ndipo Abrahamu analawira m’mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake aŵiri pamodzi naye, ndi Isake mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye. 4 Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake nawona malowo patali. 5 Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno nd bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu. 6 Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isake mwana wake; natenga moto m’dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse aŵiri. 7 Ndipo Isake ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Tawonani moto ndi nkhuni; koma mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza ali kuti? 8 Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwana wa nkhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse aŵiri. 9 Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isake mwana wake, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni. 10 Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lake, natenga mpeni kuti amuphe mwana wake. 11 Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mawu odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano. 12 Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziŵa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha. 13 Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang’ana tawonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m’chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m’malo mwa mwana wake. 14 Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M’phiri la Yehova chidzaoneka. 15 Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mawu odzera kumwamba kachiŵiri, 16 nati, Pa ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wa yekha, 17 kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo; 18 m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga. 19 Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba. 20 Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Tawonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana; 21 Huzi woyamba ndi Buzi mphwache, ndi Kemueli atate wake wa Aramu; 22 ndi Kesede, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele. 23 Ndipo Betuele anabala Rebeka: ameneŵa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwache wa Abrahamu. 24 Ndipo mkazi wake wamng’ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka.

23 Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi aŵiri ndi zisanu ndi ziŵiri: ndizo zaka za moyo wa Sara. 2 Ndipo Sara anafa m’Kiriyati-araba (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire. 3 Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Heti, nati, 4 Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso. 5 Ndipo ana a Heti anayankha Abrahamu nati kwa iye, 6 Mutimvere ife mfumu, ndinu karonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m’manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu. 7 Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m’dzikomo, ana a Heri. 8 Ndipo ananena nawo, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efroni mwana wake wa Zohari, 9 kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene liri pansonga pa munda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nawo manda. 10 Ndipo Efroni anakhala pakati pa ana a Heti: ndipo Efroni Mhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Heti, onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake, kuti, 11 Iyayi. mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga liri m’menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu. 12 Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m’dzikomo. 13 Ndipo ananena kwa Efroni alinkumva anthu a m’dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m’menemo. 14 Ndipo Efroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye, 15 Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekele a siliva mazana anayi, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? ikani wakufa wanu. 16 Ndipo Abrahamu anamvera Efroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Heti, masekele a siliva mazana anayi, ndalama zomwezo agulana nazo malonda. 17 Ndipo munda wa Efroni umene unali m’Makipela, umene unali patsogolo pa Mamre, munda ndi phanga liri momwemo, ndi mitengo yonse inali m’mundamo, yokhala m’malire monse mozungulira momwemo, 18 inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Heti, pa onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake. 19 Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m’phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamre (ndiwo Hebroni), m’dziko la Kanani. 20 Ndipo ana a Heti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga liri m’menemo, likhale lake lamanda.

24 Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m’zinthu zonse. 2 Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga: 3 ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana aakazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pawo. 4 Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi. 5 Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu kudziko komwe mwachokera inu? 6 Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko. 7 Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine ku nyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbewu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko. 8 Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko. 9 Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho. 10 Ndipo mnyamatayo anatenga ngamila khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m’dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, ku mudzi wa Nahori. 11 Ndipo anagwaditsa ngamila zake kunja kwa mudzi, ku chitsime cha madzi nthaŵi yamadzulo, nthaŵi yotuluka akazi kudzatunga madzi. 12 Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu. 13 Tawonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mudzi atuluka kudzatunga madzi; 14 ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo chotero ndidzadziŵa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu. 15 Ndipo panali, asanathe kunena, tawonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwache wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake. 16 Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m’mawonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziŵa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera. 17 Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako. 18 Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m’manja mwake namwetsa iye. 19 Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse. 20 Ndipo anafulumira nathira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamila zake zonse. 21 Munthuyo ndipo anamyang’anira iye, nakhala chete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iyayi. 22 Ndipo panali zitatha kumwa ngamila, munthuyo anatenga mphete yagolidi ya kulemera kwake sekele latheka, ndi zingwinjiri ziŵiri za m’manja ake, kulemera kwake masekele khumi a golidi. 23 Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi ku nyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife? 24 Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori. 25 Natinso kwa iye, Tiri nawo maudzu ndi zakudya zambiri ndi malo ogona. 26 Munthuyo ndipo anawerama mutu namyamika Yehova. 27 Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu amene sanasiya mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zowona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m’njira ya ku nyumba ya abale ake a mbuyanga. 28 Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo ku nyumba ya amake. 29 Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe. 30 Ndipo panali, pamene anawona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mawu a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; tawonani, anaimirira pa ngamila pakasupe. 31 Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamila. 32 Munthuyo ndipo analowa m’nyumba, namasula ngamila, napatsa ngamila maudzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye. 33 Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu. 34 Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu. 35 Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo anakula kwakukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng’ombe, ndi siliva ndi golidi, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamila ndi abulu. 36 Ndipo Sara mkazi wake wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo. 37 Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana aakazi a Kanani, m’dziko mwawo m’mene ndikhala ine; 38 koma udzanke ku nyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi. 39 Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanditsara ine. 40 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m’njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi ku nyumba ya atate wanga; 41 ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako; pofika iwe kwa abale anga; ndipo sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako. 42 Ndipondinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m’mene ndinkamo ine; 43 tawonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi, ndikati kwa iye, Ndipatse madzi ndimwe pang’ono m’mtsuko mwako; 44 ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamila zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga. 45 Ndisanathe kunena m’mtima mwanga, tawonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira kukasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu. 46 Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lake, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamila. 47 Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pamphuno pake ndi zingwinjiri pa manja ake. 48 Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m’njira yakuwona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wamkazi wa mphwache wa mbuyanga. 49 Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zowonadi, mundiuze, ngati iyayi, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere. 50 Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino. 51 Tawonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova. 52 Ndipo panali pamene anamva mawuwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi. 53 Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zokometsera zagolidi, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake. 54 Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m’mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. 55 Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuŵerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka. 56 Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m’njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. 57 Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pake. 58 Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka. 59 Ndipo anamlola Rebeka mlongo wawo ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake. 60 Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amayi wa anthu zikwizikwi, mbewu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nawo. 61 Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamila natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka. 62 Ndipo Isake anadzera njira ya Beerelahai-roi; chifukwa kuti anakhala iye m’dziko la kumwera. 63 Ndipo Isake anatuluka kulingalira m’munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, tawona, ngamila zinalinkudza. 64 Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anawona Isake anatsika pa ngamila. 65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m’munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba. 66 Mnyamatayo ndipo anamuuza Isake zonse anazichita. 67 Ndipo Isake anamlowetsa mkaziyo m’hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isake anatonthozedwa mtima atafa amake.

25 Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura. 2 Ndipo anambalira iye Zimerani ndi Yokesani ndi Medani, ndi Midyani, ndi Yisebaki, ndi Sua. 3 Ndipo Yokesani anabala Seba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi. 4 Ana a Midyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse ameneŵa ndi ana a Ketura. 5 Ndipo Abrahamu anampatsa Isake zonse anali nazo. 6 Koma kwa ana a akazi ake aang’ono amene Abrahamu anali nawo Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isake mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum’maŵa, ku dziko la kum’maŵa. 7 Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu. 8 Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m’ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake. 9 Ndipo ana ake Isake ndi Ismayeli anamuika iye m’phanga la Makipela, m’munda wa Efroni mwana wake wa Zohari Mhiti, umene uli patsogolo pa Mamre; 10 munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Heti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake. 11 Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isake mwana wake; ndipo Isake anakhala pa Beere-lahai-roi. 12 Mibadwo ya Ismayeli mwana wamwamuna wake wa Abrahamu, amene Hagara M-aigupto mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: 13 ndipo maina a ana a Ismayeli, maina awo m’mibadwo yawo ndi awa: woyamba wa Ismayeli ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Abideele, ndi Mibisamu, 14 ndi Misima, ndi Duma, ndi Masa; 15 ndi Hadada, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema; 16 ana a Ismayeli ndi awa: maina awo m’midzi yawo, m’misasa yawo ndi awa: akaronga khumi ndi aŵiri m’mitundu yawo. 17 Zaka za moyo wa Ismayeli ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziŵiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake. 18 Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum’mawa kwake kwa Aigupto, pakunka ku Asuri: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse. 19 Mibadwo ya Isake mwana wake wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isake: 20 ndipo Isake anali wa zaka makumi anayi pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Msuriya wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Msuriya. 21 Ndipo Isake anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati. 22 Ndipo ana analimbana mkati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova. 23 Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri iri m’mimba mwako, Magulu aŵiri a anthu adzatuluka m’mimba mwako; Gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono. 24 Atatha masiku ake akubala, tawonani, amapasa anali m’mimba mwake. 25 Ndipo woyamba anabadwa wofiira, monse mwake monga malaya aubweya: ndipo anamutcha dzina lake Esau. 26 Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwache ndipo dzanja lake linagwira chitende cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isake anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo. 27 Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziŵa zakusaka nyama, munthu wa m’thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m’mahema. 28 Ndipo Isake anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m’thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo. 29 Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka: 30 ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu. 31 Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako. 32 Ndipo Esau anati, Tawona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanji nawo? 33 Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake. 34 Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake.

26 Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isake ananka kwa Abimeleke mfumu ya Afilitsi ku Gerari. 2 Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Aigupto, khala m’dziko m’mene ndidzakuuza iwe; 3 khala mlendo m’dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbewu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako; 4 ndipo ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbewu zako maiko onsewa; m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; 5 chifukwa kuti Abrahamu anamvera mawu anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga. 6 Ndipo Isake anakhala m’Gerari; 7 ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuwona. 8 Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang’ana kunja kwa zenera, napenya, tawona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake. 9 Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Tawona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye. 10 Ndipo Abimeleke anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? panatsala pang’ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife. 11 Ndipo Abimeleke anauza anthu ake, nati, Ali yense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zowonatu adzaphedwa. 12 Ndipo Isake anabzala m’dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye. 13 Ndipo anakula munthuyo, nakulakula kufikira kuti anakhala wamkulukulu: 14 ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitire iye nsanje. 15 Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi. 16 Ndipo Abimeleke anati kwa Isake, Ochoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamkulu wopambana ife. 17 Ndipo Isake anachoka kumeneko, namanga hema wake m’chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko. 18 Ndipo Isake anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake. 19 Ndipo anyamata a Isake anakumba m’chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka. 20 Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isake kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye. 21 Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina. 22 Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangana nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m’dziko muno. 23 Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba. 24 Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndiri ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbewu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga. 25 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isake anakumba chitsime. 26 Ndipo ananka kwa iye Abimeleke kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake. 27 Ndipo Isake anati kwa iwo, Mwandidzera chifukwa chiyani, inu akundida ine, ndi kundichotsa kwanu? 28 Ndipo iwo anati, Kuwona tiwona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse aŵiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe; 29 kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakuchitira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova. 30 Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa. 31 Ndipo analawira m’mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isake anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m’mtendere. 32 Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isake anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi. 33 Ndipo anatcha dzina lake Seba, chifukwa chake dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino. 34 Pamene Esau anali wa zaka makumi anayi, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Mhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Elone Mhiti: 35 ndipo iwo anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.

27 Ndipo panali atakalamba Isake, ndi maso ake anali a khungu losawona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano. 2 Ndipo anati, Tawonatu, ndakalamba, sindidziŵa tsiku la kufa kwanga: 3 tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama; 4 nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe. 5 Ndipo anamva Rebeka pamene Isake ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo. 6 Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Tawona ndinamva atate wako alinkunena ndi Esau mkulu wako kuti, 7 Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe. 8 Tsopanotu mwana wanga, tamvera mawu anga monga momwe nditi ndikuuze iwe. 9 Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino ta mbuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda: 10 ndipo udzapita nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe. 11 Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Tawonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala. 12 Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzawoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso. 13 Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mawu anga, kazimuka kunditengera timeneto. 14 Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake. 15 Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m’nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng’ono; 16 ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ake ndi pakhosi pake posalala; 17 ndipo anapereka m’dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga. 18 Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga? 19 Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine. 20 Ndipo Isake anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino. 21 Ndipo Isake anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina. 22 Ndipo Yakobo anasendera kwa Isake atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mawu ndi mawu a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau. 23 Ndipo sanazindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye. 24 Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? ndipo anati, Ndine amene. 25 Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye. 26 Ndipo Isake atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga. 27 Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Tawona, kununkhira kwa mwana wanga, Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova; 28 Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, Ndi zonenepa za dziko lapansi, Ndi tirigu wambiri ndi vinyo; 29 Anthu akutumikire iwe, Mitundu ikuweramire iwe; Uchite ufumu pa abale ako, Ana a amako akuweramire iwe; Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, Wodalitsika aliyense akudalitsa iwe. 30 Ndipo panali atatha Isake kumdalitsa Yakobo, atatuluka Yakobo pamaso pa Isake atate wake, Esau mkulu wake analowa kuchokera kuthengo. 31 Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine. 32 Ndipo Isake atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau. 33 Ndipo Isake ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? inde, adzadalitsika. 34 Pamene Esau anamva mawu a atate wake Isake, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. 35 Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako. 36 Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? kuti wandinyenga ine kaŵiri aka; analanda ukulu wanga ndipo tawonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungira ine mdalitso? 37 Ndipo anayankha Isake nati kwa Esau, Tawona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani? 38 Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nawo mdalitso umozi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mawu ake nalira. 39 Ndipo Isake atate wake anayankha nati kwa iye, Tawona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, Mpa mame a kumwamba akudzera komwe; 40 Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako; Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, Udzachotsa goli lake pakhosi pako. 41 Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nawo: ndipo Esau anati m’mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo. 42 Ndipo anauza Rebeka mawu a Esau mwana wake wamkulu; ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng’ono, nati kwa iye, Tawona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe. 43 Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mawu anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harana; 44 ukhale naye masiku akuŵerengeka, mpaka wamchokera ukali wa mkulu wako; 45 mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse aŵiri tsiku limodzi? 46 Ndipo anati Rebeka kwa Isake, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Heti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?

28 Ndipo Isake anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenga mkazi wa ana aakazi a Kanani. 2 Tauka, nupite ku Padanaramu, ku nyumba ya Betuele, atate wa amayi ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana aakazi a Labani mlongo wake wa amako. 3 Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: 4 akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbewu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m’dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu. 5 Ndipo Isake anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Msuriya, mlongo wake wa Rebeka, amayi wawo wa Yakobo ndi Esau. 6 Ndipo anawona Esau kuti Isake anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; 7 ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani; ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu; 8 ndipo Esau anawona kuti ana aakazi a Kanani sanakondweretsa Isake atate wake: 9 ndipo ananka kwa Ismayeli, nawonjezera kwa akazi amene anali nawo, natanga Mahalati mwana wamkazi wa Ismayeli mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake. 10 Ndipo Yakobo anachoka m’Beereseba, nanka ku Harana. 11 Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuŵa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wake, nagona tulo kumeneko. 12 Ndipo analota, tawonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, tawonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo. 13 Tawonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isake; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbewu zako; 14 mbewu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum’amawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbewu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. 15 Tawonani, Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufukira kuti nditachita chimene ndanena nawe. 16 Ndipo Yakobo anauka m’tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe. 17 Ndipo anawopa, nati Poopsya pompano! pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penayi, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba. 18 Yakobo ndipo anauka m’mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pake. 19 Ndipo anatcha dzina la pamenepo Beteli; pakuyamba dzina la mudziwo ndi Luzi. 20 Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m’njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala, 21 kuti ndibwerenso ku nyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga, 22 ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani inu limodzi la magawo khumi

29 Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum’maŵa. 2 Ndipo anayang’ana, tawonani, chitsime m’dambo, ndipo, tawonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu. 3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake. 4 Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana. 5 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziŵa Labani mwana wake wa Nahori? nati, Timdziŵa. 6 Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: tawonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa. 7 Ndipo iye anati, Tawonani, kukali msana, si nthaŵi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni. 8 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa. 9 Ali chilankhulire nawo, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta. 10 Ndipo panali pamene Yakobo anawona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake. 11 Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mawu ake, nalira. 12 Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake. 13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangita kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m’nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo. 14 Ndipo Labani anati kwa iye, Etu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthaŵi ya mwezi umodzi. 15 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani? 16 Ndipo Labani anali ndi ana aakazi aŵiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng’ono ndi Rakele. 17 Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola. 18 Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng’ono. 19 Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine. 20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku oŵerengeka chifukwa cha chikondi chimene anmkonda iye nacho. 21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye. 22 Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero. 23 Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wake wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo. 24 Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya. 25 Ndipo panali m’mamawa, anawona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? wandinyenga ine bwanji? 26 Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng’ono asanaptse wamkulu. 27 Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziŵiri. 28 Yakobo ndipo anachita chotero namaliza sabata lake; ndipo Labani anmpatsa iye Rakele mwana wake wamkazi kuti akwatire iyesnso. 29 Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Rakele. 30 Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziŵiri zinanso. 31 Pamene Yehova anawona kuti anamuda Leya, anatsgula m’mimba mwake; koma Rakele anali wouma. 32 Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine. 33 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni. 34 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadzipatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana aamuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi. 35 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.

30 Pamene Rakele anawona kuti sanambalira Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe. 2 Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m’malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba? 3 Ndipo Rakele anati, Tawonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye. 4 Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye. 5 Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna. 6 Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mawu anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani. 7 Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiŵiri. 8 Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafitali. 9 Pamene Leya anawona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake. 10 Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. 11 Ndipo Leya anati, Wamwai ine! ndipoanamutcha dzina lake Gadi. 12 Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiŵiri. 13 Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! chifukwa kuti ana aakazi adzanditcha ine wokondwa; ndipo anamutcha dzina lake Aseri. 14 Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m’thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako. 15 Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako. 16 Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipirira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. 17 Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu. 18 Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara. 19 Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. 20 Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana aamuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni. 21 Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina. 22 Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m’mimba mwake. 23 Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga; 24 namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina. 25 Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa. 26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziŵa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe. 27 Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe. 28 Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa. 29 Ndipo iye anati kwa Labani, Udziŵa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine. 30 Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zoŵerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kuli konse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa? 31 Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako. 32 Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse ndi kusankhasankha mmenemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamaangamaanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamaangamaanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga. 33 Chotero chilungamo changa chidzandivomereza mtsogolomo, pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iriyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamaangamaanga ya mbuzi, ndi iriyonse ya mbuzi yosakhala yakuda, ikupezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba. 34 Ndipo Labani anati, Tawona, kukhale monga mawu ako. 35 Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololo mipyololo ndi amathotho-mathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamaanga-maanga ndi zamathotho-mathotho zonse zinali zoyera pang’ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m’dzanja la ana ake aamuna. 36 Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani. 37 Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo [wauwisi] walibne, ndi za mtengo wakatungulume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula mmenemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m’nthyolemo. 38 Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m’mitchera yakumwera, m’mene ziweto zinafika kumweramo, ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa. 39 Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololo-mipyololo, ndi mathotho-mathotho, ndi zamaanga-maanga. 40 Ndipo Yakobo analekanitsa ana a nkhosa naziika nkhope za zoweta kuti ziyang’anire zamipyololo-mipyololo, ndi zakuda zonse za m’zoweta za Labani, ndipo anaika magulu ake pa okha; sanaziika pa zoweta za Labani. 41 Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m’mitcheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo. 42 Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziika zimenezo: ndipo zofooka zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo. 43 Munthuyo ndipo anakula kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamila, ndi abulu.

31 Ndipo anamva mawu a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m’zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse. 2 Ndipo Yakobo anawona nkhope ya Labani, tawonani, siinamuonekere iye monga kale. 3 Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe. 4 Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake, 5 ndipo anati kwa iwo, Ndiwona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine. 6 Ndipo inu mudziŵa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu. 7 Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa. 8 Akati chotero, Zamathotho-mathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathotho-mathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololo-mipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololo-mipyololo. 9 Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine. 10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m’kulota, tawonani, atonde okwera ziwero anali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaanga-maanga. 11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m’kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano. 12 Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaanga-maanga: chifukwa ndawona zonse zimene Labani akuchitira iwe. 13 Ine ndine Mulungu wa ku Beteli, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m’dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako. 14 Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tiri nalonso gawo kapena cholowa m’nyumba ya atate wathu? 15 Kodi satiyesa ife alendo? chifukwa anatigultsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu. 16 Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite. 17 Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pa ngamila; 18 ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziwona m’Padanaramu, kuti anke kwa Isake atate wake ku dziko la Kanani. 19 Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake. 20 Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Msuriya mobisika, m’mene sanamuuze iye kuti analinkuthawa. 21 Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang’anire ku phiri la Gileadi. 22 Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa. 23 Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi aŵiri: nampeza iye pa phiri la Gileadi. 24 Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Msuriya usiku, nati kwa iye, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. 25 Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m’phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m’phiri la Gileadi. 26 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga. 27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kutseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze? 28 Ndipo sunandiloleza ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? wapusa iwe pakuchita chotero. 29 M’dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang’anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. 30 Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga? 31 Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi. 32 Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang’anira zako ziri ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba. 33 Ndipo Labani analowa m’hema wa Yakobo, ndi m’hema wa Leya, ndi m’mahema a adzakazi aŵiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m’hema wa Leya nalowa m’hema wa Rakele. 34 Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamila, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m’hema monse, koma sanawapeze. 35 Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo. 36 Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga? 37 Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m’nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse aŵiri. 38 Zaka makumi aŵiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye. 39 Chimene chinazomoledwa ndi chirombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana. 40 Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m’maso mwanga. 41 Ndinakhala chotere zaka makumi aŵiri m’nyumba mwako; zaka khumi ndi zinayi ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako aakazi aŵiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi. 42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isake zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m’manja. Mulungu anakuwona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero. 43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziwona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga aakazi ameneŵa, kapena ana awo amene anabala? 44 Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe. 45 Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa. 46 Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo. 47 Ndipo Labani anatcha pamenepo Yegara-sahaduta; koma Yakobo anatcha Galeeda. 48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galeeda; 49 ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang’anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake. 50 Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; tawonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako. 51 Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Tawona muluwu, tawona choimiritsachi, ndachiimiritsa pakati pathu. 52 Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa. 53 Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wawo aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isake. 54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse. 55 M’mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna di aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake.

32 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye. 2 Pamene Yakobo anawawona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu. 3 Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, ku dera la ku Edomu. 4 Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino: 5 ndipo ndiri nazo ng’ombe ndi abulu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako. 6 Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nawo anthu mazana anayi. 7 Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nawo ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamila, zikhale makamu aŵiri; 8 ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka. 9 Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isake, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino: 10 sindiyenera zazing’ono za zifundo zonse, ndi zowona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndi ndodo yanga ndinaoloka pa Yordano uyu; ndipo tsopano ndiri makamu aŵiri. 11 Mundipulumutsetu ine m’dzanja la mkulu wanga, m’dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amayi pamodzi ndi ana. 12 Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbewu yako monga mchenga wa pa nyanja yaikulu, umene sungathe kuŵerengeka chifukwa cha unyinji wake. 13 Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkulu wake: 14 mbuzi zazikazi mazana aŵiri, atonde makumi aŵiri, nkhosa zazikazi mazana aŵiri, ndi zazimuna makumi aŵiri, 15 ngamila zamkaka makumi atatu ndi ana awo, ng’ombe zazikazi makumi anayi, zazimuna khumi, abulu aakazi makumi aŵiri ndi ana khumi. 16 Ndipo anazipereka zimenezo m’manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyama ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina. 17 Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? za yani zimenezi patsogolo pako? 18 pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; tawonani ali pambuyo pathu. 19 Ndipo anauzanso wachiŵiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: 20 ndiponso muziti, Ndiponso, tawonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzawona nkhope yake; kapena adzandilandira ine. 21 Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono. 22 Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri, ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa doko la Yaboki. 23 Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonse anali nazo. 24 Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha. 25 Ndipo pamene anawona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye. 26 Ndipo iye anati, Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine. 27 Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo. 28 Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israyeli, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana. 29 Yakobo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo. 30 Ndipo anatcha dzina la malo amenewo, Penieli: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga. 31 Ndipo kudamchera iye pamene [anaoloka] pa Penieli, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake. 32 Chifukwa chake ana a Israyeli samadya ntsempha ya thako iri pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa ntsempha ya thako.

33 Ndipo Yakobo anatukula maso ake, tawonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anayi. Ndipo anagaŵira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi aŵiri aja. 2 Ndipo anaika adzakazi ndi ana awo patsogolo, ndi Leya ali ndi ana ake pambuyo pawo, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse. 3 Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pawo, nawerama pansi kasanu ndi kaŵiri mpaka anayandikira mkulu wake. 4 Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo. 5 Ndipo anatukula maso ake nawona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu. 6 Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana awo, nawerama pansi. 7 Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi. 8 Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga. 9 Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha. 10 Ndipo Yakobo anati, Iyayitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinawona nkhope yanu, monga anthu awona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine. 11 Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira. 12 Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine. 13 Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziŵa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndiri nazo zirinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. 14 Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang’ono pang’ono monga mwa mayendedwe a zoweta ziri pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri. 15 Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga. 16 Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. 17 Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namganga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti. 18 Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere ku mudzi wa Sekemu umene uli m’dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo. 19 Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, pa dzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu. 20 Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo Elelohe-Israyeli.

34 Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukawona akazi a kumeneko. 2 Pamene anamuwona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Mhivi, karonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa. 3 Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo. 4 Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga. 5 Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake aamuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo. 6 Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye. 7 Ndipo pakumva icho ana ake aamuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita. 8 Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatseru kuti akhale mkazi wake. 9 Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu aakazi, ndiponso dzitengereni ana athu aakazi. 10 Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m’menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m’menemo. 11 Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka. 12 Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanene kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga. 13 Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wawo, 14 nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiku kutichepetsa ife. 15 Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse; 16 pamenepo tsidzakupatsani inu ana athu aakazi, ndipo tidzadzitengera ana anu aakazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi. 17 Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye. 18 Mawu awo ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori. 19 Ndipo mnyamatayo sanachedwa kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake. 20 Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mudzi wawo, nalankhulana ndi anthu a mudzi wawo, kuti, 21 Anthu ameneŵa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m’dzikomo, achite malonda m’menemo: pakuti tawonani dzikolo liri lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana awo aakazi akhale akazi athu, tiwapatse ameneŵa ana athu aakazi. 22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nawo anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa. 23 Kodi ng’ombe zawo ndi chuma chawo ndi zoweta zawo sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nawo ndipo adzakhala pamodzi ndi ife. 24 Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mudzi wawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse anatuluka pa chipata cha mudzi wawo. 25 Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana aamuna aŵiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m’mudzi napha amuna onse. 26 Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m’nyumba ya Sekemu nachoka naye. 27 Ndipo ana aamuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mudzi chifukwa anamuipitsa mlongo wawo. 28 Ndipo analanda nkhosa zawo ndi zoweta zawo ndi abulu awo, ndi za m’mudzi, ndi za m’munda; 29 ndi chuma chawo chonse ndi ana awo ndi akazi awo anawagwira, nafunkha zonse za m’nyumba. 30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu oŵerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga. 31 Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?

35 Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Beteli nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako. 2 Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo iri mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu: 3 tinyamuke, tikwere tinke ku Beteli: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m’njira m’mene ndinapitamo. 4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m’manja mwawo, ndi mphete zinali m’makutu mwawo: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu. 5 Ndipo anapita, ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondola ana a Yakobo. 6 Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Beteli), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye. 7 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Beteli: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake. 8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Beteli, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Alioni-Bakuti. 9 Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera m’Padanaramu, namdalitsa iye. 10 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israyeli: ndipo anamutcha dzina lake Israyeli. 11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m’chuuno mwako; 12 ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isake ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbewu zako za pambuyo pako dzikoli. 13 Ndipo Mulungu anakwera kumchokera iye kumene ananena naye. 14 Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta. 15 Ndipo anatcha dzina lake la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Beteli. 16 Ndipo anachokera ku Beteli: ndipo panatsala nthaŵi asanafike ku Efrati: ndipo Rakele anabala navutidwa. 17 Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna. 18 Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini. 19 Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira ya ku Efrati (ndipo Betelehemu). 20 Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero. 21 Ndipo Israyeli anapita namanga hema wake patseri pa nsanja ya Edere. 22 Ndipo panali pamene Israyeli anakhala m’dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng’ono wa atate wake: ndipo Israyeli anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi aŵiri: 23 ana aamuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara; 24 ana aamuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini; 25 ana aamuna a Biliha mdzakazi wake wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafitali; 26 ndipo ana aamuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Aseri: amenewo ndi ana aamuna a Yakobo amene anabala iye m’Padanaramu. 27 Ndipo Yakobo anafika kwa Isake atate wake ku Mamre, ku Kririyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isake. 28 Ndipo masiku a Isake anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu. 29 Ndipo Isake anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake aamuna anamuika iye.

36 Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi: 2 Esau anatenga akazi ake a ana aakazi a m’Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Mhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni Mhivi; 3 ndi Basemati mwana wamkazi wa Ismayeli, mlongo wake wa Nabayoti. 4 Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reueli; 5 ndipo Oholibama anabala Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora; ameneŵa ndi ana aamuna a Esau, amene anambadwira m’dziko la Kanani. 6 Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m’banja mwake, ndi ng’ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m’dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwache. 7 Chifukwa chuma chawo chinali chambiri chotero kuti sanakhoza kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira chifukwa cha ng’ombe zawo. 8 Ndipo Esau anakhala m’phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu. 9 Mibadwo ya Esau atate wawo wa Aedomu m’phiri la Seiri ndi iyi: 10 ameneŵa ndi maina a ana aamuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wake wa Esau, Reueli mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wake wa Esau. 11 Ndipo ana aamuna a Elifazi ndiwo Temani, Omari, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi. 12 Ndipo Timna anali mkazi wake wamng’ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleki: ameneŵa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau . 13 Ndi ana aamuna a Reueli: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; ameneŵa ndi ana a Basemati mkazi wake wa Esau. 14 Ana aamuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora. 15 Ameneŵa ndi mafumu a ana aamuna a Esau: ana aamuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi, 16 mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleki: ameneŵa ndi mafumu a kwa Elifazi m’dziko la Edomu: ameneŵa ndi ana aamuna a Ada. 17 Ameneŵa ndi ana aamuna a Reueli mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; ameneŵa ndi mafumu obadwa kwa Reueli m’dziko la Edomu: ameneŵa ndi ana aamuna a Basemati mkazi wake wa Esau. 18 Ameneŵa ndi ana aamuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Jeusi, mfumu Jalamu, mfumu Kora, ameneŵa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau. 19 Ameneŵa ndi ana aamuna a Esau, ameneŵa ndi mafumu awo; yemweyo ndi Edomu. 20 Ameneŵa ndi ana aamuna a Seiri Mhori, okhala m’dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana, 21 ndi Disoni ndi Ezeri ndi Disani; ameneŵa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m’dziko la Edomu. 22 Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu: mlongo wake wa Lotani anali Timna. 23 Ana a Sobali ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebali, Sefo ndi Onamu. 24 Ana a Zibeoni ndi ameneŵa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m’chipululu, pakudyetsa abulu a Zibeoni atate wake. 25 Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana. 26 Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana. 27 Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani. 28 Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana. 29 Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotai, mfumu Sobali, mfumu Zibeoni, mfumu Ana, 30 mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; ameneŵa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu awo m’dziko a Seiri. 31 Amenewo ndi mafumu analamulira m’dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu aliyense. 32 Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m’Edomu, ndipo dzina la mudzi wake ndilo Dinaba. 33 Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m’malo mwake. 34 Ndipo Jobabi anamwalira, ndipo Husami wa ku dziko la Atemani analamulira m’malo mwake. 35 Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m’dambo la Moabu, analamulira m’malo mwake: dzina la mudzi wake ndi Avita. 36 Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masereka analamulira m’malo mwake. 37 Ndipo Samila anamwalira, ndipo Sauli wa ku Rehoboti pambali pa Nyanja analamulira m’malo mwake. 38 Ndipo Sauli anamwalira, ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m’malo mwake. 39 Ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m’malo mwake; dzina la mudzi wake ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wake ndi Mehetabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-zahabi. 40 Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja awo, monga malo awo, monga maina awo ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Jeteti: 41 mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni; 42 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari; 43 mfumu Magidieli, mfumu Iramu; ameneŵa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwawo m’dziko lokhala lawolawo. Uyo ndiye Esau atate wawo wa Aedomu.

37 Ndipo Yakobo anakhala m’dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m’dziko la Kanani. 2 Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziŵiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yawo yoipa. 3 Koma Israyeli anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro. 4 Ndipo abale ake anawona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere. 5 Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa. 6 Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: 7 pakuti tawonani, ndinalinkumanga mitolo m’munda, ndipo tawonani, mtolo wanga unauka nuima chiriri! ndipo tawonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga. 8 Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mawu ake. 9 Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Tawonani, ndalotanso loto lina: ndipo tawonani, dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine. 10 Ndipo iye anafokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amayi ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi? 11 Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mawu amene m’mtima mwake. 12 Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wawo m’Sekemu. 13 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta m’Sekemu? tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano. 14 Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukawone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino; nundibwezere ine mawu. Ndipo anamtuma iye kuchokera m’chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu. 15 Ndipo anampeza munthu, tawonani, analinkusokera m’thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani? 16 Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta. 17 Munthuyo ndipo anati, Anachoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotana. Yosefe ndipo anatsata abale ake, nawapeza ali ku Dotana. 18 Ndipo iwo anamuwona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe. 19 Ndipo anati wina ndi mnzake, Tawonani, alinkudza mwini maloto uja. 20 Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m’dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chirombo; ndipo tidzawona momwe adzachita maloto ake. 21 Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m’manja mwawo; nati, Tisamuphe iye. 22 Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m’dzenjemo m’chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m’manja mwawo, ambwezenso kwa atate wake. 23 Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye; 24 ndipo anamtenga iye, namponya m’dzenjemo; m’dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m’menemo. 25 Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula mawo awo, nayang’ana, ndipo tawonani, ulendo wa Aismayeli anachokera ku Gileadi ndi ngamila zawo, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto. 26 Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake? 27 Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayeli, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake. 28 Ndipo anapita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m’dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama zasiliva makumi aŵiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto. 29 Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo tawonani, Yosefe mulibe m’dzenjemo: ndipo iye anang’amba nsalu yake. 30 Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti? 31 Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m’mwazi wake: 32 natumiza malaya amwinjiro, nadza nawo kwa atate wawo: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena. 33 Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chirombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu. 34 Yakobo ndipo anang’amba malaya ake, navala chiguduli m’chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri. 35 Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira. 36 Amidyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Aigupto kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.

38 Ndipo panali nthaŵi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa M-adulami, dzina lake Hira. 2 Ndipo Yuda anawona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Sua: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye. 3 Ndipo anatenga pakati, nabala mwaba wamwamuna, namutcha dzina lake Eri. 4 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani. 5 Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibi pamene mkazi anambala iye. 6 Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara. 7 Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye. 8 Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwache wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbewu. 9 Ndipo Onani anadziŵa kuti mbewu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbewu kwa mkulu wake. 10 Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Mulungu, ndipo anamupha iyenso. 11 Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiya m’nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna; chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m’nyumba ya atate wake. 12 Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Sua, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, M-adulami. 13 Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Tawona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake. 14 Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chiri pa njira ya ku Timna; pakuti anawona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatsa iye kuti akhale mkazi wake. 15 Pamene Yuda anamuwona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake. 16 Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu ndilowane nawe; chifukwa sanamdziŵa kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine. 17 Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m’ziweto. Ndipo mkazi anati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza? 18 Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo iri m’dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye. 19 Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chovunda chake, navala zovala zamasiye zake. 20 Ndipo Yuda anatumiza kamwana ka mbuzi ndi dzanja la bwenzi lake M-adulami, kuti alandire chikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeza iye. 21 Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali [pambali] pa njira pa Enaimu? ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano. 22 Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano. 23 Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: tawona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye. 24 Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso tawonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti aponyedwe pamoto. 25 Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang’anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo? 26 Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziŵanso mkaziyo. 27 Ndipo panali nthaŵi ya kubala kwake, tawonani, amapasa anali m’mimba mwake. 28 Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga pa dzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa. 29 Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, tawona, mbale wake anabadwa, ndipo namwina anati, Wadziposolera wekha bwanji? chifukwa chake dzina lake linatchedwa Pereze. 30 Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera.

39 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, M-aigupto, anamgula iye m’manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka kumeneko. 2 Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m’nyumba ya mbuyake M-aigupto. 3 Ndipo mbuyake anawona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m’dzanja lake zonse anazichita. 4 Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yake, naika m’manja mwake zonse anali nazo. 5 Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang’anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m’nyumba ndi m’munda. 6 Ndipo iye anasiya zake zonse m’manja a Yosefe: osadziŵa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola. 7 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang’anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. 8 Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Tawonani, mbuyanga sadziŵa chimene chiri ndi ine m’nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m’manja anga; 9 mulibe wina m’nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu? 10 Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye. 11 Ndipo panali, nthaŵi yomweyo, iye analowa m’nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m’nyumba mkatimo. 12 Ndipo mkazi anagwira iye chofunsa chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m’dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo. 13 Ndipo panali pamene mkazi anawona kuti anasiya chofunda chake m’dzanja lake, nathawira kubwalo, 14 anaitana amuna a m’nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Tawonani, walowetsa kwa ife Mhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mawu aakulu: 15 ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mawu anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo. 16 Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwawo mbuyake. 17 Ndipo ananena kwa iye monga mawu awa, nati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine: 18 ndipo panali pamene ndinakweza mawu anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja. 19 Ndipo panali pamene mbuyake anamva mawu a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsya mtima. 20 Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m’kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m’mwemo m’kaidimo. 21 Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang’anira kaidi. 22 Ndipo woyang’anira kaidi anapereka m’manja a Yosefe akaidi onse okhala m’kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m’menemo, iye ndiye wozichita. 23 Woyang’anira m’kaidi sanayang’anira kanthu kalikonse kamene kanali m’manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa.

40 Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aigupto ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wawo mfumu ya Aigupto. 2 Ndipo Farao anakwiyira akulu ake aŵiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate. 3 Ndipo anaika iwo asungidwe m’nyumba ya kazembe wa alonda, m’kaidi, umo anamangidwa Yosefe. 4 Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthaŵi mosungidwamo. 5 Ndipo analota maloto onse aŵiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aigupto, amene anamangidwa m’kaidi. 6 Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m’maŵa, nawawona iwo, tawonani, anali oziya. 7 Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m’nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero? 8 Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tiribe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu. 9 Ndipo wopereka chikho wamkulu anafotokozera Yosefe loto lake, nati kwa iye, M’kulota kwanga, tawona, mpesa unali pamaso panga: 10 ndipo m’mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha: 11 ndipo chikho cha Farao chinali m’dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m’chikho cha Farao ndi kupereka chikho m’dzanja la Farao. 12 Ndipo Yosefe anati kwa iye, Mmasuliro wake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu; 13 akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako, ndipo udzapereka chikho cha Farao m’dzanja lake, monga kale lomwe mmene unali wopereka chikho chake. 14 Koma undikumbukire ine mmene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m’nyumbamu: 15 chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m’dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m’dzenjemu. 16 Pamene wophika mkate anawona kuti mmasuliro wake unali wabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, tawonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga; 17 m’lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundu mitundu; ndipo mbalame zinadya ya m’lichero a pamutu panga. 18 Ndipo Yosefe anayankha nati, Mmasuliro wake ndi uwu: malichero atatu ndiwo masiku atatu; 19 akali masiku atatu Farao adzakeza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako. 20 Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu, ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. 21 Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m’manja a Farao. 22 Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira. 23 Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukira Yosefe, koma anamuiwala.

41 Ndipo panali zitapita zaka ziŵiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, tawonani, anaima panyanja. 2 Ndipo, tawonani, zinatuluka m’nyanja ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango. 3 Ndipo, tawonani ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zinatuluka m’nyanjamo pambuyo pawo, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng’ombe zinazo m’mphepete mwa nyanja. 4 Ndipo ng’ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka. 5 Ndipo anagona nalotanso kachiŵiri: ndipo tawonani, ngala zisanu ndi ziŵiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino. 6 Ndipo, tawonani, ngala zisanu ndi ziŵiri, zoonda zopsyerera ndi mphepo ya kum’maŵa, zinamera pambuyo pawo. 7 Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziŵiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, tawonani, analota. 8 Ndipo panali m’mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m’Aigupto, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao. 9 Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero. 10 Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m’nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: 11 ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lake. 12 Ndipo panali ndi ife mnyamata, Mhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga mwa loto lake anatimasulira. 13 Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika. 14 Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m’dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ake, nalowa kwa Farao. 15 Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziŵa kumasulira. 16 Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere. 17 Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M’loto langa tawona, ndinaima m’mphepete mwa nyanja; 18 ndipo tawona, zinatuluka m’nyanjamo ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m’mabango; 19 ndipo, tawona, ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zina zinatuluka pambuyo pawo zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m’dziko la Aigupto; 20 ndipo ng’ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zonenepa. 21 Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m’maonekedwe awo monga poyamba. 22 Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinawona m’kulota kwanga, tawona, ngala zisanu ndi ziŵiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino; 23 ndipo, tawona, ngala zisanu ndi ziŵiri zina zofota, zoonda, zopsyerera ndi mphepo ya kum’maŵa, zinamera pambuyo pawo; 24 ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziŵiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga; koma panalibe wondimasulira ine. 25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao liri limodzi: chimene Mulungu ati achite wammasulira Farao. 26 Ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziŵiri, ndi ngala zisanu ndi ziŵiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziŵiri: loto liri limodzi. 27 Ng’ombe zazikazi zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pawo ndizo zaka zisanu ndi ziŵiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziŵiri zopanda kanthu zopsyerera ndi mphepo ya kum’maŵa, ndizo zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. 28 Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao. 29 Tawonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziŵiri zakuchuluka chakudya m’dziko lonse la Aigupto; 30 ndipo pambuyo pawo zidzauka zaka zisanu ndi ziŵiri za njala; ndipo anthu adzaiŵala zochuluka zonsezo m’dziko la Aigupto; ndipo njala idzapululutsa dziko; 31 ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m’mbuyoyo, pakuti idzavuta. 32 Ndipo lotolo linabwerezedwa kaŵiri kwa Farao, chifukwa chinthu chiri chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita. 33 Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang’anire dziko la Aigupto. 34 Farao achite chotere, alembe woyang’anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Aigupto m’zaka zisanu ndi ziŵiri zakuchuluka dzinthu. 35 Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zirinkudzazo, aunjike tirigu m’manja a Farao akhale chakudya m’midzi, namsunge. 36 Ndipo chakudyacho chidzakhala m’dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziŵiri za njala imene idzakhala m’dziko la Aigupto; kuti dziko [lisawonongedwe] ndi njala. 37 Ndipo chinthucho chinali chabwino m’maso mwa Farao, ndi m’maso mwa anyamata ake. 38 Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m’mtima mwake? 39 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe. 40 Uziyang’anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mawu ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe. 41 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Tawona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Aigupto. 42 Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake pa dzanja lake, naiveka pa dzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolidi pakhosi pake; 43 ndipo anamkweza iye m’gareta wake wachiŵiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Aigupto. 44 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m’dziko lonse la Aigupto. 45 Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m’dziko la Aigupto. 46 Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Aigupto. 47 Ndipo zaka zisanu ndi ziŵiri zakuchuluka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri. 48 Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziŵiri chimene chinali m’dziko la Aigupto, nasunga chakudyacho m’midzi; chakudya cha m’minda, yozinga midzi yonse, anachisunga m’menemo. 49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuŵerenga; chifukwa nali wosaŵerengeka. 50 Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana aamuna aŵiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. 51 Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga. 52 Ndipo dzina la wachiŵiri anamutcha Efraimu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m’dziko la kusauka kwanga. 53 Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziŵiri za m’dziko la Aigupto, zinatha. 54 Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m’maiko monse; koma m’dziko lonse la Aigupto munali chakudya. 55 Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anafuulira Farao wapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani. 56 Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aaigupto: ndipo njala inakula m’dziko la Aigupto. 57 Ndipo maiko onse anafika ku Aigupto kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m’dziko lonse lapansi.

42 Ndipo anawona Yakobo kuti m’Aigupto munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang’anana? 2 Ndipo iye anati, Tawonani, ndamva kuti m’Aigupto muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe. 3 Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu m’Aigupto. 4 Koma Yakobo sanamtuma Benjamini mphwache wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingamgwere iye. 5 Ndipo ana aamuna a Israyeli anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m’dziko la Kanani munali njala. 6 Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m’dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zawo pansi. 7 Ndipo Yosefe anawona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya. 8 Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikira iye. 9 Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo Ozonda inu; mwadzera kudzawona usiwa wa dziko. 10 Ndipo iwo anati kwa iye, Iyayi, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya. 11 Tonse tiri ana aamuna a munthu mmodzi; tiri oona, akapolo anu, sitiri ozonda. 12 Ndipo iye anati kwa iwo, Iyayi, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko. 13 Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m’dziko la Kanani; ndipo, tawonani, wamng’ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi. 14 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda. 15 Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko. 16 Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mawu anu ayesedwe, ngati zowona ziri mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu. 17 Ndipo anaika onse m’kaidi masiku atatu. 18 Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu; 19 ngati muli owona, mmodzi wa abale anu amangidwe m’kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu; 20 koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mawu anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho. 21 Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinawona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira. 22 Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? chifukwa chakenso, tawonani mwazi wake ufunidwa. 23 Ndipo sanadziŵa kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira. 24 Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nawo, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pawo. 25 Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zawo ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zawo, aliyense m’thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero. 26 Ndipo anasenzetsa abulu awo tirigu wawo nachokapo. 27 Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; tawonani, zinali kukamwa kwa thumba lake. 28 Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, tawonani, ziri kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yawo inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife? 29 Ndipo anadza kwa Yakobo atate wawo ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinawonekera kwa iwo; 30 kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko. 31 Koma ife tinati kwa iye, [Tiri] anthu owona; sitiri ozonda; 32 tiri abale khumi ndi aŵiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng’ono ali ndi atate wathu m’dziko la Kanani. 33 Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziŵa kuti muli anthu owona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani; 34 idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziŵa kuti simuli ozonda koma anthu owona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m’dziko muno. 35 Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba awo, tawonani, phukusi la ndalama la yense linali m’thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate awo anawona mapuksi a ndalama anawopa. 36 Ndipo Yakobo atate wawo anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera. 37 Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna aŵiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m’manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu. 38 Ndipo iye anati, Mwana wanga zadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m’njira m’mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.

43 Ndipo njala inakula m’dzikomo. 2 Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Aigupto atate wawo anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang’ono. 3 Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mawu kuti, Simudzawonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko. 4 Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya. 5 Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzawona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu. 6 Ndipo Israyeli anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu? 7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mawu amenewo: ngati tinadziŵa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu? 8 Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu aang’ono. 9 Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse: 10 pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kaŵiri. 11 Ndipo Israyeli atate wawo anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m’dziko muno m’zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang’ono, ndi uchi pang’ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungulume; 12 nimutenge ndalama zowirikiza m’manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m’manja mwanu; kapena sanachita dala; 13 mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja: 14 Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu. 15 Amunawo ndipo anatenga mphatso, natenga ndalama zowirikiza m’manja mwawo, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Aigupto, naima pamaso pa Yosefe. 16 Ndipo pamene anawona Benjamini pamodzi nawo, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nawo anthuwo m’nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno. 17 Munthuyo anachita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nawo anthuwo m’nyumba ya Yosefe. 18 Anthuwo ndipo anawopa, chifukwa analowezedwa m’nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m’matumba athu nthaŵi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti awone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu. 19 Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati, 20 Mfumu, tinatsikira ndithu nthaŵi yoyamba kudzagula chakudya: 21 ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo tawonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m’manja mwathu. 22 Ndalama zina tatenga m’manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziŵa amene anaika ndalama zathu m’matumba athu. 23 Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu, ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m’matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni. 24 Ndipo munthuyo analowetsa anthu m’nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi awo, napatsa abulu awo chakudya. 25 Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo. 26 Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m’nyumba mphatso zinali m’manja mwawo, namweramira iye pansi. 27 Ndipo anafunsa iwo za ubwino wawo, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo? 28 Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye. 29 Ndipo iye anatukula maso ake nawona Benjamini mphwache, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng’ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga. 30 Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwache, ndipo anafuna polirira; nalowa m’chipinda chake naliramo. 31 Ndipo anasamba nkhope yake, natuluka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani chakudya. 32 Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chawo pa okha, ndi Aaigupto akudya naye chawo pa okha; chifukwa Aaigupto sanatheyi kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aaigupto. 33 Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng’ono monga ung’ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina. 34 Ndipo anawagaŵira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.

44 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake. 2 Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng’ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mawu ananena Yosefe. 3 Pamene kudacha, anamukitsa anthu iwo ndi abulu awo. 4 Atatuluka m’mudzi asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nawo, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m’malo mwa zabwino? 5 Kodi sindicho chomwera nacho mbuyanga, nawombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero. 6 Ndipo anapeza iwo, nanena nawo mawu omwewo. 7 Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mawu otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu achite chotero? 8 Tawonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m’dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m’nyumba ya mbuyanga siliva kapena golidi? 9 Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga. 10 Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mawu anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa. 11 Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake. 12 Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng’ono; nachipeza chikho m’thumba la Benjamini: 13 ndipo anang’amba zovala zawo, nasenzetsa yense bulu wake, nabwera kumudzi. 14 Yudanso ndi abale ake anadza ku nyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake. 15 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziŵa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu? 16 Ndipo Yuda anati, Kodi tsati bwanji kwa mbuyanga? kodi tidzanenanji? kapena tidzaŵiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; tawonani, tiri akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m’dzanja lake. 17 Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m’dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu. 18 Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m’makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao. 19 Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu? 20 Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tiri ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng’ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye. 21 Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m’maso mwanga. 22 Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangatheyi kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa. 23 Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzawonanso konse nkhope yanga. 24 Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanu atate wanga, tinamfotokozere iye mawu a mbuyanga. 25 Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife chakudya pang’ono. 26 Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng’ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingawone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng’ono akapanda kukhala ndi ife. 27 Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziŵa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana aamuna aŵiri; 28 wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zowonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuwonanso iye; 29 ndipo ngati mukandichotsera ameneyonso, ndipo ngati chimgwera choipa, mudzanditsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda. 30 Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wake uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo; 31 kudzakhala pakuwona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda. 32 Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthaŵi zonse. 33 Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m’malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake. 34 Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? ndingawone choipa chidzagwera atate wanga.

45 Ndipo Yosefe sanakhoza kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake. 2 Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aaigupto, ndipo anamva a m’nyumba ya Farao. 3 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoza kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuwona iye. 4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m’Aigupto. 5 Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo. 6 Zaka ziwirizi muli njala m’dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga. 7 Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m’dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu. 8 Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anadiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto. 9 Fulumirani, kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. 10 Ndipo mudzakhala m’dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo; 11 ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nawo. 12 Tawonani, maso anu awona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m’kamwa mwanga ndirikulankhula ndi inu. 13 Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m’Aigupto, ndi zonse mwaziwona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga. 14 Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake. 15 Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalilira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye. 16 Ndipo mbiri yake inamveka m’nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake. 17 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani; 18 katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Aigupto, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli. 19 Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magareta a m’dziko la Aigupto; nimubwere naye atate wanu. 20 Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Aiguto ndi zanu. 21 Ndipo ana a Israyeli anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magareta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira. 22 Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa ndalama zasiliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu. 23 Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za m’Aigupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira. 24 Ndipo anamukitsa abale ake, ndipo anachoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira. 25 Ndipo anakwera natuluka m’Aigupto, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wawo. 26 Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m’dziko lonse la Aigupto. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirira iwo. 27 Ndipo anamfotokozera iye mawu onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anawona magareta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wawo unatsitsimuka; 28 ndipo Israyeli anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe.

46 Ndipo Israyeli anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isake atate wake. 2 Ndipo Mulungu ananena kwa Israyeli, m’masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo. 3 Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu; 4 Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Aigupto; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako. 5 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israyeli anamnyamula Yakobo atate wawo, ndi ana awo aang’ono, ndi akazi awo, m’magareta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye. 6 Ndipo anatenga ng’ombe zawo ndi chuma chawo anachipeza m’dziko la Kanani, nadza ku Aigupto, Yakobo ndi mbewu zake zonse pamodzi ndi iye; 7 ana ake aamuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana aakazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbewu zake zonse anadza nazo m’Agupto. 8 Maina a ana a Israyeli amene anadza m’Aigupto ndi awa: Yakobo ndi ana aamuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo. 9 Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezroni, ndi Karmi. 10 Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemueli ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani. 11 Ndi ana aamuna a Levi: Gerisoni, Kohati, ndi Merai. 12 Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m’dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezroni ndi Hamuli. 13 Ndi ana aamuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Yabi, ndi Simroni. 14 Ndi ana aamuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleeli. 15 Amenewo ndi ana aamuna a Leya, amene anambalira Yakobo m’Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu. 16 Ndi ana aamuna a Gadi: Zifioni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Ezboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli. 17 Ndi ana aamuna a Aseri: Yimna, ndi Yisiva, ndi Yisivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wawo; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikieli. 18 Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi. 19 Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini. 20 Kwa Yosefe kunabadwa m’dziko la Aigupto Manase ndi Efraimu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. 21 Ndi ana aamuna a Benjamini: Bela ndi Bekeri, ndi Asibeli, ndi Gera, ndi Namani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi. 22 Amenewo ndi ana a Rakele, amene anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anayi. 23 Ndi ana aamuna a Dani: Husimu. 24 Ndi ana aamuna a Nafitali: Yazeeli, ndi Guni, ndi Yezera ndi Silemu. 25 Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi aŵiri. 26 Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m’Aigupto, amene anatuluka m’chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana aamuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi; 27 ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye m’Aigupto ndiwo anthu aŵiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m’Aigupto anali makumi asanu ndi aŵiri. 28 Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pake kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yonka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni. 29 Ndipo Yosefe anamanga gareta lake nakwera kunka kukakomana naye Israyeli atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake. 30 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndawona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo. 31 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m’dziko la Kanani, afika kwa ine; 32 ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng’ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo ndi zonse ali nazo. 33 Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani? 34 mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng’ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m’dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aaigupto.

47 Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, tawonani, ali m’dziko la Goseni. 2 Ndipo mwa abale ake anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao. 3 Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu. 4 Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m’dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m’dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m’dziko la Goseni. 5 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe; 6 dziko la Aigupto liri pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m’dziko la Goseni; ndipo ngati udziŵa anthu anzeru mwa iwo, uwaike iwo ayang’anire ng’ombe zanga. 7 Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Faro. 8 Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati? 9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali oŵerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m’masiku a ulendo wawo. 10 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao. 11 Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m’dziko la Aigupto, m’dera lokometsetsa la m’dziko, m’dziko la Ramese, monga analamulira Farao. 12 Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja awo. 13 Ndipo munalibe chakudya m’dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Aigupto ndi dziko la Kanani linalefuka chifukwa cha njalayo. 14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m’dziko la Aigupto ndi m’dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama ku nyumba ya Farao. 15 Ndipo zitatha ndalama zonse m’dziko la Aigupto ndi m’dziko la Kanani, Aaigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? zatsirizika ndalama. 16 Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng’ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng’ombe zanu ngati ndalama zatsirizika. 17 Ndipo anadza nazo ng’ombe zawo kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zawo zonse chaka chimenecho. 18 Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiŵiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng’ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu; 19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbewu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja. 20 Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Aigupto, chifukwa Aaigupto anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao. 21 Tsono anthu, anasunthira iwo ku midzi kuchokera kumphepete kwa malire a Aigupto kufikira kumphepete kwina kwake. 22 Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lawo kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitsa dziko lawo. 23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Tawonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, tawonani, mbewu zanu sizi, mubzale m’dziko. 24 Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anayi ndi anu, mbewu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu. 25 Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao. 26 Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Aigupto kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao. 27 Ndipo Israyeli anakhala m’dziko la Aigupto, m’dziko la Goseni; nakhala nazo zawozawo m’menemo, nabalana nachuluka kwambiri. 28 Ndipo Yakobo anakhala m’dziko la Aigupto zaka khumi mphambu zisanu ndi ziŵiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anayi kudza zisanu ndi ziŵiri. 29 Ndipo nthaŵi inayandikira kuti Israyeli adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zowona: usandiikatu ine m’Aigupto; 30 koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m’dziko la Aigupto, ukandiike ine m’manda mwawo. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena. 31 Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israyeli anawerama kumutu kwa akam.

48 Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Tawonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna aŵiri, Manase ndi Efraimu, apite naye. 2 Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Tawonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Yakobo anadzilimbitsa, nakhala tsonga pakama. 3 Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anawonekera kwa ine pa Luzi m’dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine, 4 Tawona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbewu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale lawolawo chikhalire. 5 Tsopano ana ako aamuna aŵiri, amene anakubadwira iwe m’dziko la Aigupto, ndisanadze kwa iwe ku Aigupto, ndiwo anga; Efraimu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga. 6 Koma obala iwe udzawabala pambuyo pawo, ndiwo ako; awatche dzina la abale awo m’cholowa chawo. 7 Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m’dziko la Kanani m’njira, itatsala nthaŵi yaing’ono tisadafike ku Efrati; ndipo ndindamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efrati (ndiwo Betelehemu). 8 Ndipo Israyeli anayang’ana ana aamuna a Yosefe, nati, Ndani awa? 9 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Ameneŵa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze nawotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa. 10 Koma maso a Israyeli anali akhungu m’ukalamba wake, ndipo santheyi kuwona. Ndipo anadza nawo pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira. 11 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndiwone nkhope yako: ndipo, tawona, Mulungu wandiwonetsa ine mbewu zako zomwe. 12 Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa mawondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi. 13 Ndipo Yosefe anatenga iwo onse aŵiri, Efraimu m’dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m’dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israyeli, nadza nawo pafupi ndi iye. 14 Ndipo Israyeli anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pa mutu wa Efraimu, amene ndiye wamng’ono, ndi dzanja lake lamanzere pa mutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba. 15 Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isake, Mulungu amene anandidyetsa ine nthaŵi zonse za moyo wanga kufikira lero, 16 mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isake; iwo akule, nakhale khamu pakati a dziko lapansi. 17 Ndipo pamene Yosefe anawona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pa mutu wa Efraimu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pa mutu wa Efraimu ndi kuliika pa [mutu] wa Manase. 18 Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wake. 19 Koma anakana atate wake, nati, Ndidziŵa mwananga, ndidziŵa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwache adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbewu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri. 20 Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israyeli adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efraimu ndi monga Manase; ndipo anaika Efraimu woyamba wa Manase. 21 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Tawona, ndirinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, akubwezanso iwe ku dziko la makolo ako. 22 Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m’dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.

49 Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo. 2 Sonkhanani, tamvani, ana aamuna a Yakobo: Tamverani Israyeli atate wanu: 3 Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; Ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana. 4 Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; Chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; Pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo. 5 Simeoni ndi Levi ndiwo abale; Zida za mphulupulu ndizo malupanga awo. 6 Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chawo; Ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano awo; Chifukwa m’kukwiya kwawo anapha munthu, M’kufuna kwawo anapundula ng’ombe. 7 Kutembereredwe kukwaiya kwawo, chifukwa kunali kowopsa; Ndi kupsya mtima kwawo, chifukwa kunali kwankhalwe; Ndidzawagawanitsa m’Yakobo Ndidzabalalitsa iwo m’Israyeli. 8 Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; Dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; Ana aamuna a atate wako adzakuweramira. 9 Yuda ndi mwana wa mkango, Kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; Anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, Ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye? 10 Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, Kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, Kufikira atadza Silo; Ndipo anthu adzamvera iye. 11 Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; Natsuka malaya ake m’vinyo, ndi chofunda chake m’mwazi wa mphesa. 12 Maso ake adzafiira ndi vinyo, Ndipo mano ake adzayera ndi mkaka. 13 Zebuloni adzakhala m’doko la kunyanja; Ndipo iye adzakhala doko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Zidoni. 14 Isakara ndiye bulu wolimba, Alinkugona pakati pa makola; 15 Ndipo anawona popumulapo kuti panali pabwino, Ndi dziko kuti linali lokondweretsa; Ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, Nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho. 16 Dani adzaweruza anthu ake, Monga limodzi la mafuko a Israyeli. 17 Dani adzakhala njoka m’khwalala, Songo panjira, Imene iluma zitende za akavalo, Kuti womkwera wake agwe chambuyo. 18 Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova. 19 Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye; Koma iye adzapsinja pa chitende chawo. 20 Ndi Aseri, chakudya chake ndicho mafuta, Ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu. 21 Nafitali ndi nswala yomasuka; Apatsa mawu abwino. 22 Yosefe ndi nthambi yobala, Nthambi yobala pambali pa kasupe; Nthambi zake ziyangayanga palinga. 23 Eni uta anavutitsa iye kwambiri, Namponyera iye, namzunza: 24 Koma uta wake unakhala wamphamvu, Ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneku ndi mbusa, mwala wa Israyeli,) 25 Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, Ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalita iwe Ndi madalitso a Kuwamba, Madalitso a madzi akuya akukhala pansi, Madalitso a mabere, ndi a mimba. 26 Madalitso a atate wako Apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, Kufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire; Adzakhala pa mutu wa Yosefe, Ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake. 27 Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; M’mamawa adzadya chomotola, Madzulo adzagawa zofunkha. 28 Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wawo nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa. 29 Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m’phanga liri m’munda wa Efroni Mhiti, 30 m’phanga liri m’munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamre, m’dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efroni Mhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake: 31 pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isake ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya: 32 munda ndi phanga liri m’menemo, zinagulidwa kwa ana a Heti. 33 Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake aamuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wake.

50 Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye. 2 Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing’anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing’anga anakonza Israyeli. 3 Ndipo anatha masiku ake makumi anayi a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aaigupto anamlira iye masiku makumi asanu ndi aŵiri. 4 Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m’makutu a Farao kuti, 5 Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Tawona, ndirinkufa; m’manda mmene ndadzikonzeratu ndekha m’dziko la Kanani, mmenemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso. 6 Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe. 7 Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m’dziko la Aigupto, 8 ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: aang’ono awo okha, ndi nkhosa zawo, ndi ng’ombe zawo, anazisiya m’dziko la Goseni. 9 Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magareta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu. 10 Ndipo anafika pa dwale la Atadi, liri tsidya lija la Yordano, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi. 11 Ndipo pamene anthu okhala m’dzikomo, Akanani, anawona maliro m’dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro aakulu a Aaigupto: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano. 12 Ndipo ana ake aamuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo; 13 chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m’dziko la Kanani, ndi kumuika iye m’phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efronni Mhiti, patsogolo pa Mamre. 14 Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Aigupto, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake. 15 Ndipo pamene abale ake a Yosefe anawona kuti atate wawo anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye. 16 Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira kuti, 17 Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwawo, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. 18 Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Tawonani, ife ndife akapolo anu. 19 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m’malo a Mulungu? 20 Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri. 21 Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachezera inu, ndi ana anu aang’ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yawo, nanena nawo mokoma mtima. 22 Ndipo Yosefe anakhala m’Aigupto, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi. 23 Ndipo Yosefe anawona ana a Efraimu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. 24 Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndirinkufa ine, koma Mulungu adzawonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m’dziko muno kkubwera kunka ku dziko limene analumbirira Abrahamu ndi kwa Isake, ndi kwa Yakobo. 25 Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israyeli kuti, Mulungu adzawonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nawo mafupa anga kuchokera kuno. 26 Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m’bokosi m’Aigupto.