|
KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN Na. 1 |

KUGWIRITSA NTCHITO KOSI YA BAIBULOYI
Kuwerenga : Salmo 19
Kosi Yophunzitsa Baibulo ya ma Christadelphians yakonzedwa mânjira yakuti ikuthandizeni kumvetsa Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Baibulo, lomwe nthawi zina limatchedwa "Malemba", ndi buku lokhalo lomwe limatiuza molondola zokhudza Mulungu komanso mapulani ake okhudza dziko lapansili. Baibulo limalonjeza kuti aliyense amene amaliwerenga moona mtima adzalandira madalitso.
Mukufunikira mukhale ndi Baibulo lanulanu
Kukhala ndi Baibulo ndi mwayi wapadera kwambiri. Kuti mupindule ndi kosiyi mukuyenera kukhala ndi Baibulo lanulanu lathunthu (osati Chipangano Chatsopano chokha). Ngati mulibe Baibulo, mungaligule motchipa ku nthambi ya Bible Society. Pafupifupi mâdziko lililonse muli nthambi zimenezi. Koma ngati simungakwanitse kuchita zimenezi, dziwitsani mphunzitsi wanu mwachangu. Iye angakuthandizeni kuti mupeze Baibulo lakale.
Kosiyi ili ndi mapepala a mafunso okwana 40, amene mukufunika kumayankha mlungu uliwonse. Ngati mphunzitsi wanu amakhala kutali kwambiri ndi kumene inuyo muli, ndiye kuti muzatumiziridwa maphunziro angapo komanso Mapepala a Mafunso onse nthawi imodzi. Mphunzitsi wanu ndi:
Nambala Yanu Ndi
Chonde, muzigwiritsa ntchito nambala imeneyi pa makalata onse, komanso pa mapepala a mayankho, ndi zina ndi zina.
Chonde, tumizani mayankho anu onse (pamodzi ndi mayankho) kwa mphunzitsi wanu. Zingakhale bwino ngati mutangolemba dzina la mphunzitsi lanu basi, ngakhale kuti mungaone mayina ndi maadiresi ena ambiri pa mabuku athu.
Mawu ochokera mâBaibulo amene muwapeze mu kosiyi achokera mâBaibulo Revised Nyanja (Union) Version, koma mwina Baibuloli silingapezeke mâmayiko ena. (Mwina mungaone kuti mawu a mâBaibuloli akhoza kusiyana pangâono ndi mawu a mâMabaibulo ena amene akupezeka mâdziko lanu.) Komabe, sikuti tanthauzo la mawuwo limasiyana ayi ngakhale kuti mabaibulo angasiyane.
Kosiyi ndi ya ulele. Mungafunike kulipira mtengo wotumizira kalata kwa mphunzitsi wanu kamodzi pamwezi. Cholinga chathu nâchofuna kukuthandizani kuti muzisangalala mukamawerenga Malemba, komanso tikufuna kuti inuyo mudziwe uthenga wosangalatsa wachipulumutso chodzera mwa Yesu Khristu. Sitipereka masatifiketi kwa anthu amene amaliza maphunzirowa ayi, koma mukamaliza maphunziro okwana 60, tikufuna kukuthandizani kuti mupitirize kuphunzira Baibulo.
Malifalensi a Baibulo
Pakaperekedwa lifalensi ya mâBaibulo, izilembedwa mooneka chonchi:
Genesis 1 âizi zikutanthauza kuti Buku la Genesis, chaputala 1;
Genesis 1:1 -7â zi zikutanthauza kuti buku la Genesis, chaputala 1, vesi 1 mpaka 7.
Mmene mungaphunzirire
Muziyesetsa kuphunzira mutu umodzi mlungu uliwonse. Tikukupemphani kuti muzionetsetsa kuti mwamvetsa phunziro limodzi musanapite ku lina. Zimakhala zothandiza kuwerenga phunziro lililonse katatu. Nthawi yoyamba, muziyesetsa kudziwa zokhudza phunzirolo, nthawi yachiwiri, muziwerenga mavesi onse kuchokera mâBaibulo lanu ndipo muzilemba manotsi papepala kapena muzilemba mafunso omwe mwaona kuti ndi ovuta. Nthawi yachitatu muziwerenga pamodzi ndi malifalensi ena amene aikidwa koyambirira kwa phunzirolo. Kenako kumapeto kwa phunziro lililonse, mupezako mavesi ena othandiza kwambiri, omwe mungachite bwino kumawawerenga mâBaibulo lanu, komanso lemba limodzi limene tikukulimbikitsani kuti muliloweze pa mtima. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musaiwale mavesiwa ndipo angakuthandizeni pamoyo wanu wonse.
Tikamakutumizirani mapepala anu oyambirira, timatumizanso PULANI YOKUTHANDIZANI POWERENGA BAIBULO. Pulaniyi inakonzedwa mânjira yokuthandizani kuti muziwerenga chaputala chimodzi mâBaibulo tsiku lililonse. Mukamayesetsa kuchita zimenezi, ndiye kuti simuchedwa kuzolowera mbali zosiyanasiyana za Baibulo. (Mungachite bwino kusunga Pulani Yokuthandizani Powerenga Baibulo mkati mwa Baibulo lanu, kuti muzitha kuigwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku.) Palinso chinthu china chothandiza chimene tikufuna kuti mukhale nacho. Mphunzitsi wanu akangolandira mayankho a mafunso a Pepala Loyamba, adzakutumizirani kope laulere la buku lotchedwa BUKU LOTHANDIZA POWERENGA BAIBULO. Mâbukuli muli ndemanga zachidule za kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.Bukuli ndi lifalensi yothandiza kwambiri ya Baibulo chifukwa lili ndi zinthu ngati mapu ambirimbiri komanso zithunzi zina.
Kuyankha Mafunso
Tikukupemphani kuti mwezi uliwonse muzitumiza mayankho a mafunso kwa mphunzitsi wanu. tumizani mayankhowo pa positi.) Chonde, muziyankha mafunsowo mâmawu anuanu. Musangokopera zimene zalembedwa mâphunzirolo. Muziyesetsa kufotokoza zimene inuyo mukukhulupirira kuti nâzoona. Ngati simukugwirizana ndi mfundo zina zimene zili mâphunziro linalake kapena muli ndi funso, chonde, fotokozani. Kuchita zimenezi nâkofunika kwambiri. Musaiwale kuti tingakuthandizeni bwino ngati tikudziwa zimene mukuganiza. Ngati pa zifukwa zina simungathe kutumiza mayankho anu, tumizani uthenga wachidule wotidziwitsa kuti mukufunitsitsa kupitirizabe ndi kosiyi ndipo mukufunabe kuti muzilandira nawo mapepala a maphunzirowa.
Kugwiritsa ntchito nthawi moyenera
Nâzoona kuti kuphunzira maphunziro amenewa kuzikutengerani nthawi yanu ina tsiku lililonse, mwina 15, powerenga Baibulo. Komanso ola limodzi mlungu uliwonse pophunzira phunziro lililonse. Mungafunikenso kupeza nthawi yoti muyankhe mafunso. Mudzaonanso kuti Malemba amene ali m'maphunzirowa ndi osangalatsa ndiponso ofunika kutherapo nthawi ndithu powaphunzira.
Muzipemphera musanayambe kuwerenga Baibulo komanso mukamaliza
Musanayambe kuphunzira, muzipemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni kumvetsa mawu ake. Taonani pemphero ili lochokera mâbuku la Masalmo:
"Munditsegulire maso, kuti ndipenye Zodabwiza za mâchilamulo chanu" (Salmo 119:18)
Tikamupempha, Mulungu adzatsegula maso athu ndipo adzatithandiza kumvetsa buku Lake, Baibulo.
Zimene tidzachita mukangokhala chete, osatiuza chilichonse
Tikukhulupirira kuti mukudziwa zoti pali anthu ambirimbiri padziko lonse lapansili amene akufunitsitsa kulandira ndi kuphunzira kosi ya Baibuloyi. Tikapanda kumva chilichonse kuchokera kwa inu, (mwachitsanzo mukapanda kutitumizira mayankho onse a mafunso) tidzaganiza kuti simukufunanso kupitiriza kuphunzira. Ndiye ifeyo tidzasiya kukutumizirani maphunziro ena.
Ngati zikukuvutani kuyankha kapena kutumiza mapepala onse okhala ndi mayankho, chonde dziwitsani mphunzitsi wanu ndipo mufotokoze chifukwa chake. Mukatero ndiye kuti ife tidzapitiriza kukutumizirani maphunzirowa. Chomwe tikufuna n'kudziwa zoti zimene tikutumizazo zikulandiridwa komanso kugwiritsidwa ntchito pophunzira Mawu a Mulungu.
Kosi Yonse ya Baibulo
Mâmunsimu muli mitu ya maphunziro 60 a kosi imeneyi:
«
1 Mmene Mungagwiritsire Ntchito Kosiyi
2 Kodi ma Christadelphians ndi Ndani?
3 Baibulo ndi Buku Lothandiza
4 Uthenga Wabwino
Pepala la Mafunso Na. 1
5 Mulungu Ndiponso Chilengedwe
6 Mulungu Anakonda Dziko Lapansi
7 Kubweranso kwa Yesu Padziko Lapansi
8 Zizindikiro za Kubwera kwa Yesu
Pepala la Mafunso Na. 2
9 Ufumu Wanu Udze
10 Mmene Mulungu Amaonera Mbiri Yakale
11 Ufumu wa Mulungu Udzabweretsa Mtendere Padzikoli
Pepala la Mafunso Na. 3
12 Malonjezo Amene Mulungu Analonjeza Abulahamu
13 Mbiri Yokhudza Ayuda, Gawo I
14 Mbiri Yokhudza Ayuda, Gawo II
15 Lonjezo la Mulungu kwa Davide
Pepala la Mafunso Na. 4
16 Atate ndi Mwana
17 Moyo wa Yesu
18 Imfa ya Yesu
19 Kuukitsidwa ndi Kukwera Kumwamba kwa Yesu Khristu
Pepala la Mafunso Na. 5
20 Mzimu Woyera wa Mulungu
21 Mphatso za Mzimu Woyera
22 Uchimo ndi Zotsatirapo Zake, Gawo I
23 Uchimo ndi Zotsatirapo Zake, Gawo II
Pepala la Mafunso Na. 6
24 Mwachisomo, Mwapulumutsidwa
25 Kuukitsidwa kwa Akufa
26 Chiweruzo
27 Moyo Wosatha
Pepala la Mafunso Na. 7
28 Angelo
29 Mdyerekezi (ziwanda) ndi Satana
30 Mdyerekezi ndi Uchimo
31 Ubatizo
Pepala la Mafunso Na. 8
32 Ukwati wa Chikhristu
33 Mavuto a Mâbanja
34 Udindo Wathu ku Boma
35 Pemphero
36 Kuyenda Mâmoyo Watsopano
Pepala la Mafunso Na. 9
37 Kuwerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
38 Kusonkhana ndi Anzathu a Chikhulupiriro Chimodzi
39 Mphamvu ya Lilime
40 Kunyema Mkate
Pepala la Mafunso Na. 10
41 Moyo wa Banja pa Utumiki wa Yesu
42 Vuto la Tchimo
43 Mawu a Mulungu Mâmoyo Wathu wa Tsiku ndi Tsiku
44 Eklesia wa Mulungu
Pepala la Mafunso Na. 11
45 Mmene Timaonera Anthu Ena Zimamukhudza Kwambiri Mulungu
46 Kukonda Mnansi Wanu
47 Zimene Baibulo Limaphunzitsa pa Nkhani ya Mavuto
48 Kukhala mwa Mantha
Pepala la Mafunso Na. 12
49 Kodi Kukhala ndi Mtima Wofuna Kuchita Zinthu Zotsogola ndi Wabwino?
50 Kukhala Woona Mtima Pamaso pa Mulungu ndi Mwana Wake Yesu Khristu
51 Kusonyeza Mkwiyo Komanso Kudziletsa
52 Mmene Wophunzira wa Yesu Amaonera Boma
Pepala la Mafunso Na. 13
53 Kugonana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
54 Kusankha Munthu Womanga Naye Banja
55 Mfundo Zina Zokhudza Chiweruzo Komanso Ufumu
56 Kukhala ndi Chiyembekezo pa Moyo ndi Mphatso ya Mtengo Wamtengo Wapatali
Pepala la Mafunso Na. 14
57 Kuchita Zinthu Mogwirizana ndi âChikhulupiriroâ Komanso Chikhristu
58 Chisomo cha Mulungu
59 Chidule cha Ziphunzitso za MâBaibulo
60 Zoyenera Kuchita
Pepala Lomaliza la Mafunso
Christadelphian Bible Mission, Box CBM, 404 Shaftmoor lane, Birmingham B28 8SZ, England