KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN Na

Chichewa

KOSI YOPHUNZITSA BAIBULO YA MA CHRISTADELPHIAN •^•^ Na. 2

KODI MA CHRISTADELPHIANS NDI NDANI?

Kuwerenga : Yohane 15

Cholinga cha kosi ya Baibuloyi ndi kuthandiza anthu kuphunzira Malemba. Komabe, mwina mungadabwe kuti, kodi ma Christadelphians ndi ndani? Choncho munkhani ino tikufotokozerani pang’ono zokhudza ifeyo.

Ma Christadelphians ndi gulu la amuna ndi akazi amene akupezeka padziko lonse, amene amawerenga Baibulo lonse ndipo amaliona kuti ndi Mawu a Mulungu ouziridwa. Amakhulupirira malonjezo onse onena za Ambuye Yesu Khristu komanso onena za dziko la m’tsogolo, amene ali m’Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano. Ma Christadelphians akuyembekezera kuti Yesu adzabweranso kuchokera kumwamba kuti adzakhazikitse ufumu wa Mulungu padziko lapansili.

Dzina lakuti Christadelphian anachokera kumawu awiri achigiriki, amene amatanthauza Abale mwa Khristu.

Kodi ma Christadelphians amakhala kuti?

Ma Christadelphians akupezeka m’mayiko oposa 50. Amapezeka ku Britain komanso m’mayiko ambiri a ku Ulaya. Amapezekanso m’mayiko ambirimbiri ku Africa; ku Far East, kuchokera ku India m’paka ku Indonesia; ku Australasia ndi kuzilumba za panyanja ya Pacific. Akupezekanso m’mayko a ku North ndi South America kuchokera ku Canada mpaka kukafika ku Argentina, komanso pazilumba za ku Caribbean. M’gululi muli amuna ndi akazi a mitundu yosiyanasiyana komanso a zikhalidwe zosiyana siyana.

Kosi iwo amakhulupirira zotani?

Chikhulupiriro cha ma Christadelphians chagona pa zinthu zimene Yesu ndi ophunzira ake ankakhupirira komanso kuphunzitsa zaka pafupifupi 2000 zapitazo. Uthenga weniweni wa Chikhristu sunasithe. Koma n’zomvetsa chisoni kuti kwa zaka mahandiredi ambirimbiri matchalitci “Achikhristu” akhala akutsatira komanso kuphunzitsa zinthu zimene zinachokera ku zipembedzo zonyenga. Ngakhale zili choncho, padzikoli pakhala pakupezeka kagulu ka anthu ochepa kwambiri amene sanasiye kutsatira choonadi. Mwachitsazon, ku Ulaya zaka zoposa 400 zapitazo kunali anthu ambiri amene anaphunzira uthenga woona wabwino chifukwa choti ankawerenga Baibulo pawokha pamene Baibulolo linasindikizidwa m’zinenero za anthuwo. Amuna ndi akazi amenewa anayamba kutchedwa "Abale mwa Khristu". Koma n’zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa anthu amenewa anazunzidwa koopsa, ndipo ena anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ambiri anathawa m’nyumba zawo, koma pamene ankathawa anatenga Uthenga Wabwino n’kumaufalitsa m’mayiko ambiri a ku Ulaya, kuwoloka nyanja zikuluzikulu. Koma sipanapite nthawi yaitali kuti choonadicho chisakanikiranenso ndi ziphunzitso zonyenga. (Pali phunziro la mphamvu apa: Choonadi sichisokonezedwa pokhapokha ngati anthu amene ali ndi choonadiwo akuwerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu pawokha.)

Kosi gulu la ma Christadelphian linayamba bwanji?

M’chaka cha 1832, dokotala wina wa ku England, dzina lake John Thomas, amenenso anali m’busa wa tchalitchi chinachake, anakwera sitima yapamadzi imene inkapita ku New York. Iye anachita izi chifukwa bambo ake ankafuna kusamukira ku America. Ulendowu uli mkati, sitimayo inawomba nthaka chifukwa cha namondwe woopsa amene anachitika panyanjayo, ndipo Dr. Thomas ankangoganiza kuti basi, afera pomwepo. Iye anazindikira kuti sankadziwa zambiri zokhudza tsogolo, ndipo analumbira kuti ngati safa komanso akafika kumtunda ali wabwinobwino, ndiye kuti sapuma koma nthawi yomweyo adzayamba kufufuza choonadi pa nkhani yokhudza moyo umene anthu angakhale nawo pambuyo pomwalira. N’zosangalatsa kuti mkuluyu sanafe ndipo anafikadi ku New York. Atangofika, iye anachitadi zimene analonejza zija. Anakhala masiku okwana 15 akuphunzira Baibulo mwakhama zedi

Ndipo analinso ndi mpata wounika zimene matchalitchi ambirimbiri "Achikhristu" amaphunzitsa. Atakhutira kuti wamvetsa bwino zinthu zimene zinalembedwa m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano chomwe zokhudza Yesu Khristu komanso zokhudza kubwera kwa ufumu wa Mulungu padziko lapansi, anakonza zoti abatizidwe, thupi lonse limire m’madzi. Iye anapitiriza kulalikira m’madera osiyanasiyana ku America komanso ku Britain ndipo analemba magazini ndi mabuku ambirimbiri a nkhani za mawu a Mulungu.

Pa gulu la anthu amene anayamba kukhulupirira zinthu zofanana ndi John Thomas n’kuyamba kugwirizana naye pa ntchito yakeyi panali Robert Roberts, yemwe kwawo kunali ku Scotland. Roberts anathandiza pa nthawi yokonza dongosolo labwino pakati pa Akhristu a agululi amene anayamba kuchuluka kwambiri, ndipo magulu amene ankaikamo anthuwa ankawatchula kuti ma eklesia. "Eklesia" ndi mawu a m’Baibulo amene amatanthauza "msonkhano wa anthu amene aitanidwa". Ma Christadelphians amaona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito mawu amenewa kusiyana ndi "tchalitchi"—dzina lomwe nthawi zina limatanthauza nyumba imene anthu amapemphereramo m’malo mwa anthu amene akupemphera m’nyumbayo.

Anthu amene angomva dzinali kwa nthawi yoyamba akhoza kudabwa

Dzina lakuti Christadelphian linagwiritsidwa ntchito koyamba mu 1864 pamene anthu okhulupirira anapempha boma la America kuti asamalembedwe ntchito za usilikali pa nthawi imene ku America kunali nkhondo ya pachiweniweni. Popeza pamafunika dzina loti anthuwa azidziwika nalo, John Thomas anakumbukira "Abale mwa Khristu" amene anali zaka zoposa 300 m’mbuyomo, choncho anasankha dzina lakuti ma 'Christadelphian', lomwe ndi dzina lachigiriki otanthauza Abale mwa Khristu. Ma Christadelphians a m’zaka za ma 1800 amene ankayenda zedi n’kumalalikira uthenga m’mayiko osiyanasiyana padziko lapansili. Choncho pofika kumapeta kwa zaka za m’ma 1800, anthuwa anali akupezeka m’mayiko ambirimbiri padziko lonse.

Kodi gulu la ma Christadelphians linalinganizidwa bwanji?

Pali makomiti osiyanasiyana amene amayang’anira ndi kuyendetsa ntchito ya umishonale, kuyang’anira ndi kuzonda odwala komanso okalamba, komanso anthu amene ali okhaokha. Komanso tili ndi maofesi m’mayiko angapo ndipo timafalitsa magazini ndi mabuku kudzera m’ma ofesi amenewa. Koma tilibe anthu kapena atumiki amene alipidwa. Tilibenso bungwe limene tingati ndilamphamvu kapena limene limayang’anira gulu lathu. Ndalama zoyendetsera ntchito yathu yonse anthu a m’gulu la ma Christadelphians amachita kupereka okha popanda kuwakakamiza. Tilibenso ansembe.

Koma mwina mungafunse kuti: ngati palibe gulu loyendetsa ngulu limeneli, kodi nchito yonse ya ma Christadelpians imayenda bwanji? Yankho ndi lakuti izi zimatheka chifukwa choti tonse tili ndi chikhulupiriro chofanana komanso timachita zinthu zofanana. Zimenezi zimathandiza kuti tizichita zinthu mogwirizana komanso mokondana monga mamembala a gululi.

Gulu lililonse limakhala ndi dongosolo lawo loyendetsera zinth ndipo limasankha lokha “akulu” otsogolera gululo. Izi zimachitika posankha akuluwo kamodzi chaka chilichonse mochita kuvota. Anthu amene amasankhidwa kuti azitumikira eklesia m’mautumiki osiyanasiyana, monga alembi, asungichuma, matcheyamani a misonkhano. N’zoona kuti pali m’madera ena amene mamembela a gululi amatha kupeza kapena kumanga nyumba zawozawo zopemphereramo. Komabe m’madera ambiri amapempherera m’nyumba ndi m’maholo ochita kubwereka

Zikukhulupiriro zofanana

Ma Christadelphians, kulikonse kumene ali apadzikoli, akhala akuwerenga ndi kuphunzira mabuku awo opatulika ndipo akhala akukhulupirira zinthu zofanana. Patha zaka pafupifupi 100 tsopano pamene takhala ndi mawu a chikhulupiliro chathu. Tili ndi chikalata chotchedwa Chikalata cha Chikhulupiriro (chidule cha ziphunzitso za m’Baibulo) ndipo aliyese yemwe ndi membala amayensera kuchita zimenezi nthawi zonse kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha ma Christadelphian onse, chomwe ndi chochokera m’Baibulo. Zimenezi n’zimene zimatichititsa kuti tizigwirizana kwmbiri.

"Thupi limodzi . . . mzimu umodzi" (Aefeso 4:4-5)

Zimenezi zimachititsa kuti ma Christadelphians, kuli konse kumene ali, azitha kugwirizana komanso kusangalalira pamodzi.

Mtundu wa anthu amene tikuyesetsa kukhala

Tonsefe timafunika kuthandizidwa ndi Mulungu. Pa chifukwa chimenechi, timakhulupilira kuti ndi kofunika kwambiri kuti tidzipemphera. Chinthu chimodzi chimene timayesetsa kuchita tsiku ndi tsiku ndi kuwerenga Baibulo. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri ngati mmene kulili kudya chakudya nthawi ndi nthawi. Kamodzi pa mlungu, timakumana ndi kudya mkate pang’ono ndiponso kumwa vinyo pang’ono pokumbukira imfa ya Ambuye wathu Yesu Khristu. Mudzapeza kuti ma Christadelphians ndi anthu osangalala chifukwa ali ndi chikhulupiliro chotsimikizika ndi zochita zawo. Popeza Yesu akubwera posachedwapa, tikufunika kukhala okonzeka. Izi zikutanthauza kukhala m’moyo woyera ndi wokhulupirika. Zikutanthauzanso kupewa zinthu zonse zoipa. Ma Christadelphians ndi anthu omvera malamulo a dziko lawo. Amayesetsa kuchita zinthu zabwino momwe angathere, koma salowerera ndale, ndiponso samenya nkhondo kapena kutengera anthu kubwalo la milandu kuti akaweruzidwe. Amakhala ndi mkazi m’modzi komanso amapewa chigololo. (Timazindikira kuti ena alipo kale amene ali ndi akazi opitilira m’modzi pa nthawi imene iwo afika pakukhulupilira mawuwa, ndipo zoterezo zakambidwa mu Phunziro 33.)

Ma Christadelphian ali ndi Cholinga cha m’Baibulo

Ma CBM, monga mmene timatchulirana mwachidule, ntchito yathu ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’dziko lonse lapansi. CBM imalengeza maphunziro, imalemba mabuku ndi zinthu zina zowerenga ndiponso imathandiza anthu kumvetsa Baibulo. CBM ili ndi anthu ogwira ntchito amene salipidwa malipiro alionse koma ndi a Christadelphian ongodzipereka kugwira ntchitoyi kuwonjezera pa ntchito imene amagwira yolembedwa ndi ena kumene amalandira malipiro. Cholinga chake ndi kuthandiza anthu kuphunzira uthenga wabwino, kuwalimbikitsa kulapa ndi kubatizidwa, ndiponso kuti adzitsatira chitsanzo cha Yesu ndi ophunzira ake.

Tikufuna kugawana nanu zikhulupiriro zathu, chiyembekezo chathu ndiponso chimwemwe chathu

Ma Christadelphian amakhulupilira kuti chikhulupiliro chawo n’chogwirizana ndi uthenga wabwino woona umene ukupezeka m’Baibulo lonse. Tikukhulupilira kuti inunso mudzasangalala kupeza Choonadi. Sikuti mudzangosangalala basi kuti mwapeza chinthu chabwino, koma mudzakhalanso ndi chiyembekezo, chisangalalo komanso chikondi. Mulungu akudalitseni pamene mukuyesetsa kufunafuna zinthu zimenezi.

Patsamba lotsatira pali mfundo zina zofunika kwambiri za m’Baibulo. Mavesi oyenera kuwerenga : Salmo 119:130; Mateyu 28:19-20; Yohane 17:3.

Lowezani : Yohane 15:13-14

"Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu."

 

ZIPHUNZITSO ZINA ZOFUNIKA KWAMBIRI ZA M’BAIBULO

* Baibulo ndi uthenga woona wokhawo wochokera kwa Mulungu.

* Pali Mulungu m’modzi yekha basi, Mlengi, amene amayendetsa zinthu padzikoli.

* Yesu Kristu ndi mwana wa Mulungu, wobadwa mwa Mariya. Anali munthu wosachimwa. Anafa imfa ya pa mtanda kupulumutsa iwo akukhulupilira iye. Anaukitsidwa kwa akufa ndipo pakali pano ali kumwamba.

* Posachedwapa Yesu adzabwera kuchokera kumwamba. Adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pano padziko lapansi. Iye adzalamulira ngati Mfumu ndipo likulu lake lidzakhala Yerusalemu m’dziko la Israyeli.

* Ayuda ndi mboni za Mulungu pa cholinga chake, ngakhale ambiri mwa Ayudawo sadziwa zimenezi. Mulungu anapereka malonjezano kwa Abrahamu ndi kwa Davide amene adzakwaniritsidwa pakubwera kwakenso kwa Yesu pano padziko lapansi.

* Imfa ndi chilango cha uchimo ndipo anthu onse ndi ochimwa. Chiyembekezo cha moyo wina tikafa ndicho chiukiliro cha akufa Yesu akadzabwera.

* Padzakhala chiweruzo. Otsatira a Yesu onse okhulupirika adzapatsidwa moyo wosatha ndipo iwo adzathandiza iye kukonza mabvuto a dziko lapansi ndi kubweretsa mtendere ndi madalitso kwa mitundu yonse ya anthu.

* Tiyenera kukhulupilira uthenga wabwino, kulapa machimo athu ndi kubatizidwa. Ngati tiyesetsa kwambiri kutsatira malamulo a Mulungu, ndi kupemphera kuti atikhululukire tikalephera, tidzapulumutsidwa ndithu.

* Zimene Buku lopatulika lanenera zokhudza zinthu za kumbuyo ndi zinthu za nthawi yino zochitika m’dziko lapansi zaonekadi kuti zachitika. Zizindikiro zikuonetsa kuti Yesu Kristu watsala pang’ono kubwera. Ndi chifukwa chache kuli kofunika kuti muyambe kuphunzira buku lopatulika panopa.

Christadelphian Bible Mission Box CBM, 404 Shaftmoor Lane, Birmingham B28 8SZ, England

Swahili Title
Wakristadelfia ni watu gani? - Somo la 02
Swahili file
PDF file
Chichewa file
Arabic file
African text
Christadelphian Bible Mission