Ruth Chapter 00 - Introduction

Chichewa

BUKHU LA RUTE

 

CHILINGANIZO CHA CHRISTADELPHIAN

 

NDONDOMEKO YA MA VERSE A M’MAWU A MULUNGU

 

Yolembedwa ndi

H. P. Mansfield

 

BUKHU LA RUTE

 

"Ndipo ananena, ndi chinthu chopepuka ndithu kuti iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka kumalekezero a dziko." Yesaya 49:6

Mawu Oyamba

Mabukhu awiri a m’baibulo ali ndi maina a azimayi ndipo akupereka mfundo zochititsa kaso poyerekeza azimayiwa: Rute ndi Estere. Rute ndi chitsanzo cha munthu okhulupirika kuntchito munyengo yosautsa; pamene moyo wa Estere ndi chitsanzo cha nzimayi olimbika mtima pa nthawi ya mavuto a ndale za mmasiku a ufumu wa nthawi yakale imeneyo. Nthano ya Rute ikulongosora za nzakazi, pamene nthano ya Estere itiphunzitsa za mfumukazi. Nthano ya nzakaziyu inena za chikhalidwe cha amitundu pakati pa ayuda; pamene nthano ya mfumukaziyu ikukamba za nzimayi wachiyuda pakati pa amitundu. Nkhani ya nzakazi ikukamba za munthu wa amitundu kukwatirana ndi muyuda; pamene nkhani ya mfumukazi ikukamba zambiri ya munthu wachiyuda amene anakwatirana ndi munthu wa a mitundu. Nkhani izi ziwiri zinasankhidwa ndi mzimu kuthandizira kulongosola malingaliro a Yehova mwa nkhirisitu. Pakutero, zonse zili ndi phunzitso ndi kulosera kwakuya kuposera nkhanizo mwazokha ngati nkhani wamba.

Nkhani ya Rute ndiyopatsa chidwi chifukwa ndi nkhani yomwe chiyero chinapambana, komanso kugwira ntchito mwachikondi kunapindula moyenerera.

Koma pali zambiri zokuya mu bukhu ili. Nkhani yayikulu ndi yoti ikubweretsa mfundo za chipulumutso amene ali madziko a ntchito za Yahweh mwa nkhirisitu Yesu. Pamene tikupanga chidwi ndi munthu wadzitho, waulemu, ndi mpondamatiki Boazi amene sanadzikweze koma anathangatira nzakazi waamitundu osauka amene amakunkha m’munda mwake, tikuona chithunzi thunzi cha umunthu ndi utumiki wa ambuye Yesu nkhirisitu. Pa chikhalidwe chopatsa kaso cha Rute, tili ndi chithunzi-thunzi cha umunthu omwe okhulupilira a mitundu amene afunitsitsa kukhala limodzi ndi miyanda miyanda ya mitundu yaokhulupilira nkhirisitu amene ali nkwatibwi wa khirisitu, komanso amene anyadira kutero. Pamene okhulupilika ndi wachikondi Naomi, amene anavala mazunzo ndi mavuto koma anapeza chimwemwe chodzala, yemwe, pofanana ndi Rute, anapindula pa ntchito yomwe anapanga Boazi, magwero a zonsezi ndi chipangano cha Aburahamu, ndi Israyeli amene anakhazikika mu chikhulupiliro chachipanganocho, chimene chinakhazikika ndi nkhosa za chiyuda mwa khirisitu (Yohane 10:16).

Bukhuli ndi mbiri yakale komanso chifanizo. Nkhanizi zinasankhika ndi kulembedwa ndi mzimu posonyeza "chibvumbulutso cha chinsisi ... chimene kale lonse chinali chobisika kwa ana a anthu, mpaka zinadziwika kwa atumiki ndi aneneri ndi mzimu; kuti amitundu ndi alowammalo, athupi limodzi, ndipo ndi amodzi muchipangano cha mwa nkhirisitu pa uthenga wabwino" (Aefeso 3:3-6). Naomi, Rute, ndi Boazi anasunthika ndi chiphunzitso cha Yahweh mpaka anayamba kuonetsela umulungu ndi chiyero pamiyoyo yawo mpaka chifuniro cha Mulungu ngati mpulumutsi pa mbewu imene inali nkubwera. Nkhani yamiyoyo yawo inalodzera chifuniro choyera cha Mulungu pachipulumutso. Rute aphunzitsa kuti amitundu atha kukhulupilira mwa Mulungu weniweni, ndipo atha kuludzitsana ndi anthu achipangano chimodzimodzi. Bukhuli ndi chitsanzo cha mmene Mulungu asamalira anthu ake osankhika.

Cholinga cha bukhu la Rute mu baibulo ndi cholinganiza ndi nthano yomwe bukhuli likukamba. Ndi bukhu limene linatsindikizidwa pa mabukhu a mafumu ndi Samuyeli, ndiye liri ngati ulalo olumikiza mabukhu awiri amenewa. Chisokonezo chimene chinadza ndi nyengo ya oweruza yalumikizana ndi zochitika zimene zinatsata kukhazikika kwaufumu. Bukhu la Rute liri ndi masomphenya amene amaunikira zochitika mu Israyeli kuti adzakhala ndi chisokonezo cha uzimu, uthenga wabwino udzafalitsidwa kwa a mitundu ngati chiyambi chokhazikitsa ufumu wa Mulungu padziko lapansi. Bukhu la Rute lithandizira uthenga wa mu bukhu la oweruza, ngakhale phunziro la nthano yamubukhuli ndiyosiyana ndi umbanda ndi uchimo umene unachitika mu bukhuli. Bukhu la Oweruza limakamba za mbiri ya dziko munthawi yakale. Bukhuli litambasula chisokonezo ndi chiopsezo cha dziko lopanda oweruza angwiro, ndipo pamene kuopa mulungu kwachoka mmitima ya anthu, mathero ake “kunalibe mfumu mu Israyeli; aliyense anachita chimene chinankomera mwa iye yekha” (Oweruza 17:6; 21:25). Bukhu lilongosola nyengo ya uchigawenga, masautso a dziko, ndi kuchuluka kwa kuwukira Mulungu, pamene kulambila Mulungu muchoonadi kunachoka ndipo kunatsala ndikulambira kongokwaniritsa chabe ndipo chinatsala ndi kuziyenereza kwa anthu pa iwo okha.

Dziko litafika muuchimo otere, Mbiri ya Rute ndi kuwala kumene kunadza pamene kunali mdima wa kusamvera Mulungu. Mbiriyi ikusonyeza kuti pamene mdima wachisokonezo ndi uchimo unagwera dziko, pali amene analimba mtima ndikukhala okhulupirika mu m’ndandanda wa chilungamo; moti ngakhale kunali chisokonezo ndi kusaopa Mulungu, kunali anthu okhulupirika ngati Boazi, azimayi osazikonda ngati Rute ndi Naomi, ndikukhazikika mu dziko pamene bwana ndi azakazi ake analumikizana mu “mchikhulupiliro chimodzi” ngati m’munda wa Boazi.

Mbiri iyi ndiyosangalatsa; osati pa nthawi yakale yokhayo, koma mu nyengo zonse. Nyengo ya chisokonezo ndi uchimo pamene njira za chilungamo ndi chiyero zikunyozeka, si nyengo imene inali ya mbiri yakale yokha mu nthawi ya oweruza: Itha kuchitika nthawi ina iliyonse. Kulephera kwa ndondomeko ya nthawi imeneyo yaonekera pa ndime yomalizira mu bukhu la Oweruza, ndime imene ikunena za mbiri ya bukhu la Rute: “M’masiku amenewo kunalibe mfumu mu Israyeli: munthu aliyense anachita izo zimene zinali zokomera iye mwini” (Oweruza 21:25). Ndipo kunayenera kukhala mfumu yomwe anthu onse amayenera kumvera ndipo mfumu yo imayenera kuti ikhale Mulungu (Oweruza 8:23). Pa mapeto ake chisokonezo chinadzala mu dziko . Kunalibe kukana Mulungu poyera, kunalibe kusakhulupilira Mulungu kodzionetsera, kapena anthu kumadzikuza nkumadzionetsera kuti ndine osakhulupilira; koma izo zimachitika komanso zina zoopsa zinalipo zachibisi bisi: Mulungu anangokhala ngati chizindikiro chabe, koma osamalabadira za Mulungu ngati mfumu; kupembedza iye mmaonekedwe, koma mphamvu yake m’miyoyo palibe. Mose anachenjeza Israyeli kuti asachimwe ngati mmene anachitira mbuyomo: "Usachite... monga umo aliyense ayesa kuti icho ndiye cholungama m’mene iye mwini awonera" (Ditoronomo 12:8). Koma manenedwe ake sanawalabadira. Phunziro lalikulu ndi funso kwa ife, titakhala mu nyengo ngati imeneyi, tingathe kuonetsa chitsanzo cha chikhulupiliro ndi kulimba mtima ngati nthano zimene bukhu la Rute likutiphunzitsa.

Nthano ya Rute ndi yamsangalutso kwa amene ali ophinjika ndi opondelezedwa ndi zoipa zowazungulira. Pamene iwo aganizira za tanthauzo, aphunzirapo phunziro, akhonza kulimbikitsidwa ndi kuzindikira kuti iwo sali okha koma ali ndi mpulumutsi owathangata. Ngati Yobu iwo anena: "Ndikudziwa mpulumutsi wanga ndi wa Moyo..." (Yobu 19:14, 25).

Kuwerenga bukhu la Rute ndi gawo limodzi lokondwerera Pentekositi pachikhalidwe cha chiyuda pamene amatenga gawo lokumbukira ubwino wamulungu. Zochitika izo zotsindikizidwa m’bukhuli zimachitika panyengo imene a Israyeli okhulupilika amakonzekera kukondwelera pentekositi (cp. Rute 2:23).

Pakuchita izi, A Israyeli akukumbutsidwa chaka ndi chaka kuti mai wa gogo wa mfumu yawo yopambana kwambiri Mfumu David anachokera ku Moabu (Rute 4:22), mtundu umene unali osalidwa pamkumano wa Yehova pachilamulo (Detoronomo 23:3). Pamene tikuona kusankhika kwa ayuda, mfundo imeneyi itsendera chilungamo, choti bukhu la Rute ndi louzilidwa ndi mzimu wa mulungu. Ndi udindo wa Mulungu yekha umene kunakoma kuti munthu wachikunja akhale olemekezedwa mu nthano yi. Likanakhala kuti bukhuli linali ganizo lamunthu, Rute akanakhala ndi maonekedwe a chiyuda. Kudzera mu bukhu ili, Yehova anaphunzitsa kuti anthu achikunja akhonza kukhala ndi udindo muchikonzero cha chipulumutso, chimodzi modzi ngati ayuda; koma njira yopereka chipulumutso imeneyo iposa mphanvu yachilamulo (Agalatiya 3:8-14) ndi njira yachibvumbulutso ndi mphanvu ya chisomo.

Ndi gawo la chikonzero chodabwitsa cha kumwamba, kuti kudzipereka ndi kudzichepetsa kwa nzakazi osauka, wachikunja kuchokera kwa mtundu osalabadiridwa, kudzachokera mpulumutsi ndi mfumu ya anthu apadziko. Kuchokera kwa nzakazi wachikunja, kuyanjana muchiyembekezo cha Israyeli, kunabwera kupyolera mwa Devidi ndi Khirisitu. Pamene bukhuli lipereka gawo limodzi la mtundu wa Devidi, chimodzimodzi Khirisitu, tikuphunzitsidwa kuti magazi achikunja anali mwa amene anadza kuti adzapulumutse anthu onse. Ndipo mwakuyerekeza kuti kubadwa kwa khirisitu kuchokera mwa iye zinali ngati mphoto ya Rute pa utumiki okhulupirika ngakhale kuti anali wachikunja, ichi ndi chimene chili chikoka cha anthu ochuluka achikunja kuti nawo akhale ndi chiyembekezo cha Israyeli, ndipo iwo adzayenda mu mapazi a Rute okhulupirika.

Pali mtengo wapatali muchiphunzitso cha bukhuli. Chibvumbulutsa mbiri yochokera ku mtundu osadziwika ngakhale iye anali mpulumutsi chifukwa cha ichi owerenga mbiri yi adzadza chifupi naye, koma chibvumbulutsanso chikhalidwe cha Rute chimene owerenga angathe kutengera phunziro kuti angathe kukondweretsa khirisitu. Mu ndondomeko yathu iyi yamasulira mawu amulungu mozama koma mwachindunji mosataya nthawi yaikulu. Izi zitanthauza, kamasulidwe kathu ndikopereka chilakolako kwa owerenga mawu kuti akasanthule mawu okha, pakuti pakutero owerenga akapindula koposa. Onse owerenga bukhu lopatsa kasoli akawerenge mopembedzera ndi mofatsa, ndipo akapeza madalitso a nzeru zokuya.

H. P. Mansfield — May, 1979

NTHANO YA RUTE

NKHANI YAMUYAYA YOTSINDIKIZIDWA YOKAMBA ZA MSANGALATSO NDI KAKOMEDWE ZIMANGO ZA NDONDOMEKO YA CHIPULUMUTSO

NGODYA YA BUKHU

Bukhu la Rute ndilofunikira mu mbiri chifukwa ikuonetsa makolo akale a Devidi kuyambira nthawi imene mafumu anali kulamulira kuchokera pa Salmoni amene anamenya nkhondo mothandizira Yoswa, mpakana mbiri ya Jesse wa ku Betelehemu, abambo ake a Devidi (1 Sam. 16:1).

Pamenepa, pakuperekedwa danga lotha kutsata mbiri ya makolo a ambuye (Mateyu 1:1,5).

Kusamalidwa kwa nthano imeneyi mu zaka zambiri za makedzana khirisitu asanabadwe zikusonyeza kuti zipatso zochokera kwa Yahweh amene adziwa zonse “Kuyambira pa chiyambi chadziko”, chifukwa mbiri ya Devidi ilumikizana ndi mbiri ya khirisitu.

Bukhuli ndilofunika posonyeza kuti si onse a Israyeli amene anakhuzidwa ndikuipa mitima ngakhale kuti amakhala munyengo yoipa yaoweruza. Moyo wa Boazi, Naomi ndi Rute zikupereka phunziro loti ndizotheka anthu, kapena mitundu yonyozeka, kukhala angwiro ngakhale ku dziko kuli nyengo yoipitsitsa, kugalukira Mulungu kuli paliponse. Ngati anthu aonetsa chikhulupiliro chokwanira, kulimba mtima ndi kutsimikiza, akhonza kuzitukula kupyoza nyengo zawo, ndikusunga mayendedwe angwiro pamaso a Mulungu amene iye awavomereza.

Bukhuli, zolembedwa zake, komanso malo amene anaikidwa mu ndandanda wa mabukhu mu baibulo, ndibukhu limene likulosera mbiri yakudza mu bukhu la Oweruza. Linatsindikizidwa ngati mwangozi, ngati kuti owerenga akukumbutsidwa kuti nyengo za anthu owerengeka zitha kusiyana ndi ena angakhale palibe chikhulupiro chotero; kuti nthano imeneyi ikhonza kukhala chilimbikitso kwa amene afunafuna chithandizo cha Yahweh pamene akumana ndi mavuto. Tiyeni tiime nji pamene tili m’mavuto kutero mokhulupirika ndi molimba mtima ngati anachitira Naomi, Rute ndi Boazi, ndi izo anapindula mu moyo wawo, dzizakondweretsa onse otsatira zitsanzo zawo m’masiku amakono ano.

Zikuonetsa poyera chikonzero pachiyambi, osati zimene baibulo likamba za chibvumbulutso cha Yehova, komanso nthawi imene mbiri imeneyi inachitikira m’mbiri ya baibulo. Mwa chitsanzo, mabukhu asanu a Mose anatambasula za mwambi wa mbiri ya baibulo nchipangano chakale motere;

Genesis: akamba za chionongeko ndi kusankhika kwa mtundu kupyolera mu mzimu kudzera mwa Abrahamu.

Eksodo: akamba zakusiyana pamene Israyeli achoka mu Aiguputo.

Levitiko: Akamba za chiyanjano ndi Yahweh chimene ngodya yake ndi nsembe.

Numeri: Akamba za chisomo cha mzimu muzopereka zaulere ndi kutsogozedwa komwe kwaonekera ndi chisamaliro chake cha Israyeli mu nkhalango.

Deuteronomo: akamba za kupeza chiyembekezo pamene m’badwo wa a Israyeli ukonzeka kulowa mu dziko lamalonjezano.

Komanso mabukhu ena ambiri amene atsatira ndi kukamba za kale ndi zakutsogolo za khirisitu.

Yoswa:

Amene anali m’gonjetsi pa nkhondo anapanga zotheka kuti Irayeli apeze cholowa chake; kusiyira kwa eni ake ngati anthu payekha payekha kuti azipezele zochita pa okha. Khirisitu anapanga chimodzimodzi pakugonjetsa tchimo ndi imfa.

Oweruza:

Zinthunzi za chisokonezo ndi kulephera kumene kunatsata imfa ya Yoswa; kunaphimba zoipa zimene zinapeza akeleziya kuyambila nthawi ya khirisitu mpaka nthawi yambiri yakale mpakanonso nthawi yamakono.

Rute:

Akamba za kukhulupilika kwa mitundu yaing’ono ndi anthu amene akana zaupandu ndi zochimwitsa; zingavute bwanji, kuti apitirize kutumikira kwa Yahweh moyenera ndi zina lake loyera.

Samueli:

Mabukhu awiri atsindikiza zochitika zimene zinathandiza Davidi kuti akhale pa mpando wachifumu ndipo kuti ulamuliro wake ukhale wamphanvu pogonjetsa; izi zilosera kubwera kwa Khirisitu pachigonjetso ndi kubwenzera ufumu wa Davidi.

Mafumu:

Akamba za nthawi yochititsa kaso mu Israyeli, ulemelero otsogoleredwa ndi Solomoni; amene ufumu wake wamtendere unalosera nyengo yakubweranso kwa Yesu.

Mbiri:

Ikamba za kumanga kwa utumiki wa tchalitchi; kumaliza ulemelero wa padziko.

Mautumiki asanu amenewa amene alemba za mzimu (Bukhu la Rute ndi lolosera nthawi ya oweruza) atambasula mu ndondomeko za kutsogolo pamene ufumu wa mulungu uzakhazikitsidwa. Chinthu chimenechi chikhazikitsa mitu yotere:

(1) — Kugonjetsa imfa kwa khirisitu kunapangitsa kuti aliyense atha kukhala m’mulowa malo mu

ufumu wamulungu (Yoswa).

(2) — Moyo wa a keleziya ndi mbiri ya chisokonezo, tchimo, pamene anthu achikunja anali

kukhala moyo wakuthekera (Oweruza ndi Rute).

(3) — Khirisitu adzadza kudzakhazikitsa ufumu wa Davide pogonjetsa (Samuyeli).

(4) — Khirisitu adzalamulira kumanganso kwa nyumba ya mapemphero (tchalitchi) ya mitundu

yonse ya anthu (Mafumu).

(5) — Khirisitu adzakhazikitsa ndondomeko yachipembedzo mu nyumba yopemphererayo ndipo

adzakhazikitsa kulamulira kwa Mulungu (Mbiri).

 

Kaya tivomereza kapena ayi, ndondomeko imene yatambasulidwa, izi zikulosera za mmene Khirisitu adzakhazikitsile chifuniro ndi ndondomeko yake pa dziko.

Pamene pali zochitika zazikulu, zodabwitsa mum’badwo uno, chipulumutso chathu ngati anthu ndichofunika kwambiri. Pa ngodya imeneyo bukhu la Rute likupereka njira ndi chilimbikitso.

NDONDOMEKO YA BUKHU

Munthu wa ku Betelehemu dzina lake Elimelech, ndi mkazi wake Naomi, ndi ana ake aamuna Mahlon and Chilion, achoka ku dziko la kwawo pa nthawi yanjala, ndipo anapita paulendo ku malo otchedwa Moabu. Kumeneko anafa, ndipo Naomi anakwatitsa ana ake awiri kwa azimayi ochokera ku Moabu. Mahlon anakwatira Rute, ndipo Chilion anakwatira Orpah. Patantha zaka khumi amuna amenewa anamwalira, ndipo Naomi, anaperekezedwa ndi apongozi ake awiri, kuti abwerele ku malo otchedwa Yudah, koma poti iye ananva kuti kudziko la kwawo kunali mkaka ndi uchi ngati kale.

Atafika pa malire a Moabu, anawauza azipongozi ake kuti abwelere kudziko la kwawo ndi kwa azibale awo. Orpah ananva langizo la Naomi, ndipo, atasiyana mwachikondi, anabwerela; koma Rute anakakamila kuti akhale ndi mpongozi wake. Anafika mu Betelehemu pamene inali nthawi yokola za kumunda; ndipo Rute anapita kumunda kukakunkha kuti azipedzere chakudya. Munda umene anapezekamo unali wa Boazi, m’bale wake wa Elimelech. Atamuzindikira Naomi, Boazi analamula kuti alandile maulemu onse, ndipo anaonetsetsa kuti analandila chisamaliro chapadera. Atazindikira ichi, Naomi anazindikira mwapadera zokhuza moyo wa mpongozi wake kuti ndi munthu osankhidwa ndi Mulungu, ndipo anamupempha kuti alowane ndi Boazi ndi kumanga banja molingana ndi chilamulo. Boazi, atazindikira kuti ngati nzibambo anali ndi ufulu okhala pa banja, analolela kumulora Rute, bola ngati wachibale, amene anali moyo, angamkane ukwati. Iye anapempha wachibaleyo, ngati angathe kukwatira Rute ndipo iye anakana, nasiyira mphanvu Boazi, pamaso pa akuluakulu pa mipata ya mu tawuni ya Betelehemu molingana ndi chikhalidwe cha nthawi imeneyo.

Kenako Boazi anatenga Rute kuti akhale mkazi wake. Anabereka mwana dzina lake Obed, amene ndi bambo ake a Jesse, bambo a David. Choncho kuchokera kwa munthu wa ku Moabu kunabadwa mpulumutsi wa anthu onse. Mbiri la bukhu linatero

KUUNIKIRA

Ma chaputala anayi a bukhu la Rute anagawidwa, motero kuti anasindikiza ndondomeko ya moyo wa Rute.

CHAPUTALA CHOYAMBA: CHIKONDI CHIPILIRA

Utumiki wa Rute: Iye akakamira kuti aphatane ndi Naomi pamene anali namalira.

 

a. Njala ithawitsa Elimelech kuti apite dziko lakutali vv.1-2

b. Imfa inafika katatu vv.3-5

c. Naomi anaganiza zobwerela vv.6-7

d. Rute ndi Orpah anaganiza zobwerelanso vv.8-10

e. Naomi ananena za mavuto alinkuza vv. 11-13

f. Orpah anabwerela koma Rute akana kusiya Naomi vv. 14-18

g. Naomi and Rute apita ku Betelehemu vv. 19-22

 

CHAPUTALA CHACHIWIRI: CHIKONDI CHIBWENZA:

Utumiki okhulupilika wa Rute: Iye apereka yankho pa zofuna za Naomi.

 

a. Rute akunkha m’munda wa Boaz vv.1-3

b. Ubale wa Boazi ndi antchito ake vv.4-7

c. Boazi apereka ubwino kwa Rute vv.8-10

d. Zopata zochuluka zipatsidwa kwa Rute vv. 11-17

e. Naomi apereka uphungu kwa Rute vv.18-23

 

CHAPUTALA CHACHITATU:

Pempho la Rute: Apempha chithandizo cha Boazi ngati mpulumutsi.

 

a. Naomi apereka uphungu kwa Rute kuti afikire Boazi ngati mpulumutsi vv. 1-7

b. Rute apempha modzichepetsa vv.8-9

c. Yankho lachithandizo la Boazi vv. 10-13

d. Kusamalidwa kwa Rute ndi Boazi vv.14-15

e. Uphungu wa Naomi kwa Ruth vv. 16-18

 

CHAPUTALA CHACHINAYI: CHOPATA PA CHIKONDI

Ruth mkazi okondedwa apeza chisangalalo ndi mwana

a. Boazi apempha m’bale wa Rute kuti apange ukwati vv. 1-5

b. Wachibale akana kupanga ukwati vv.6-8

c. Boazi atenga udindo ngati mpulumutsi vv.9-12

d. Banja: Chimwemwe chodzala vv. 13-17

e. Mfumu wabadwa vv.18-22

 

Literature type
Book